1Chauta adauza Mose kuti,
2“Uza Aisraele kuti: Mwisraele aliyense, kapena mlendo wokhala nao m'dziko mwanu, akapereka ana ake kwa Moleki, aphedwe: anthu am'dzikomo amponye miyala.
3Munthu ameneyo ndidzamfulatira, ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anzake, chifukwa wapereka ana ake kwa Moleki ndi kuipitsa malo anga oyera, ndiponso waipitsa dzina langa loyera.
4Anthu am'dzikomo akachita ngati sakumuwona munthuyo, pamene akupereka mmodzi mwa ana ake kwa Moleki, namleka osamupha,
5Ineyo ndidzamfulatira munthu ameneyo ndi banja lake lonse. Ndidzaŵachotsa pakati pa anthu anzao, pamodzi ndi onse amene amaŵatsanzira nadziipitsa pakupembedza Moleki.
6“Munthu akapita kwa wolankhula ndi mizimu yoipa ndi kwa wanyanga, nadziipitsa pakutsatira iwowo, ndidzamfulatira ndipo ndidzamchotsa pakati pa anthu anzake.
7Nchifukwa chake mudziyeretse, ndipo mukhale oyera, poti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu.
8Muzimvera malamulo anga ndi kuŵatsata. Ine ndine Chauta amene ndikukuyeretsani.
9Eks. 21.17; Mt. 15.4; Mk. 7.10 Munthu aliyense wotemberera bambo wake ndi mai wake ayenera kuphedwa. Munthu ameneyo watemberera bambo wake ndi mai wake, tsono magazi ake akhale pa iyeyo.
10 Eks. 20.14; Lev. 18.20; Deut. 5.18 “Munthu akachita chigololo ndi mkazi wa mwiniwake, mwamunayo pamodzi ndi mkaziyo onsewo aphedwe.
11Lev. 18.8; Deut. 22.30; 27.20 Munthu wogona ndi mkazi wa bambo wake, wavula bambo wake, ndipo onsewo ayenera kuphedwa. Magazi ao akhale pa iwowo.
12Lev. 18.15 Munthu akagona ndi mkazi wa mwana wake, onsewo ayenera kuphedwa. Iwowo achita chigololo pachibale, ndipo magazi ao akhale pa iwowo.
13Lev. 18.22 Munthu akagona ndi munthu wamwamuna mnzake ngati mkazi, onsewo achita chinthu chonyansa, ndipo ayenera kuphedwa. Magazi ao akhale pa iwowo.
14Lev. 18.17; Deut. 27.23 Munthu akakwatira mkazi, nakwatiranso mai wake wa mkaziyo, kuteroko nkuchita chinthu choipa kwambiri. Onsewo ayenera kuŵatentha pa moto, mwamunayo pamodzi ndi akazi omwewo, kuti chinthu choipa kwambiri chotere chisapezeke pakati panu.
15Eks. 22.19; Lev. 18.23; Deut. 27.21 Mwamuna akagona ndi nyama, ayenera kuphedwa, ndipo nyamayo muiphenso.
16Mkazi akagona ndi nyama, aphedwe pamodzi ndi nyamayo. Aphedwe ndipo magazi ao akhale pa mkaziyo ndi nyamayo.
17 Lev. 18.9; Deut. 27.22 “Munthu akakwatira mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo wake, kapena mwana wamkazi wa mai wake, onse aŵiriwo achita chinthu chochititsa manyazi, ndipo onsewo aphedwe pakhamu pa anthu a mtundu wao. Chifukwa aphwanya malamulo motero, alipire choipa chake.
18Lev. 18.19 Munthu akagona ndi mkazi wosamba, ndiye kuti wavula msambo wake, nayenso mkaziyo wadzivula. Onse aŵiriwo achotsedwe pakati pa anthu anzao.
19Lev. 18.12-14 Musavule mbale wa mai wanu kapena mlongo wa bambo wanu, poti kuteroko nkuvula wa pa chibale chanu. Onse aŵiriwo adzalipira machimo ao.
20Munthu akagona ndi mkazi wa mbale wa bambo wake, wavula mbale wa bambo wake. Onse aŵiriwo adzasenza machimo ao ndipo adzafa opanda ana.
21Lev. 18.16 Munthu akakwatira mkazi wa mbale wake, ndiye kuti wachita chinthu chonyansa. Wavula mbale wake, ndipo onse aŵiriwo adzakhala opanda ana.
22“Nchifukwa chake muzisunga malamulo anga, ndipo muzichita zonse zimene ndimakulamulani ndi kuzitsata, kuti dziko limene mukupita kuti mukakhalemolo lingakudeni.
23Musatsanzire miyambo ya mtundu wa anthu amene ndikuupirikitsa inu mukufika. Iwo ankachita zimenezi, nchifukwa chake ndidanyansidwa nawo kwambiri.
24Koma inuyo ndakuuzani kuti: Mudzalandira dziko lao, ndipo ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale lanu, dziko lake lamwanaalirenji. Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, amene ndakupatulani pakati pa mitundu yonse ya anthu.
25Nchifukwa chake muzisiyanitsa pakati pa nyama zoipitsidwa ndi zosaipitsidwa, pakati pa mbalame zosaipitsidwa ndi zoipitsidwa. Musadziipitse pakudya nyama kapena mbalame, kapenanso zinthu zilizonse zimene zadzaza pansi pano, zomwe ndazipatula kuti inu muzidziŵe kuti nzoipitsidwa.
26Muzikhala oyera pamaso panga, pakuti Ine Chauta ndine woyera, ndipo ndakupatulani pakati pa anthu onse kuti mukhale anthu anga.
27“Mwamuna kapena mkazi wolankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kapena munthu wanyanga, ayenera kuphedwa. Aŵaponye miyala, ndipo magazi ao akhale pa iwowo.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.