Mk. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu achiritsa munthu wa ziwalo zakufa(Mt. 9.1-8; Lk. 5.17-26)

1Patapita masiku pang'ono, Yesu adabwereranso ku Kapernao, anthu nkumva kuti ali kunyumba kwao.

2Anthu ochuluka adasonkhana m'nyumbamo, kotero kuti munalibenso malo ngakhale pakhomo pomwe. Iye ankaŵalalikira mau a Mulungu.

3Anthu ena anai adaanyamula munthu wa ziwalo zakufa, kubwera naye kwa Yesu.

4Koma sadathe kufika naye pafupi ndi Yesuyo chifukwa cha kuchuluka kwa anthu. Choncho adakwera pa denga, nangosasula dengalo kuyang'anana ndi pamene Yesu analiri, nkutsitsira pachiboopo machira amene adaanyamulira munthu uja.

5Poona chikhulupiriro chaocho, Yesu adauza munthu wa ziwalo zakufayo kuti, “Mwana wanga, machimo ako akhululukidwa.”

6Koma pamenepo panalinso aphunzitsi ena a Malamulo a Mose. Iwowo adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti,

7“Kodi Iyeyu angalankhule bwanji motere? Si kunyoza Mulungu kumeneku? Ndani angakhululukire machimo, si Mulungu yekha kodi?”

8Koma Yesu adaadziŵa kuti akuganiza zimenezi mumtima mwao, motero adaŵafunsa kuti, “Bwanji mukuganiza zimenezo mumtima mwanu?

9Chapafupi koposa nchiti, kumuuza wa ziwalo zakufayu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Dzuka, nyamula machira ako, yamba kuyenda?’

10Koma kuti mudziŵe kuti Mwana wa Munthu ali nazo mphamvu pansi pano zokhululukira machimo, onani.” Pamenepo adauza wofa ziwalo uja kuti,

11“Iwe, dzuka, tenga machira ako, uzipita kumudzi.”

12Munthu uja adadzukadi, natenga machira ake aja nkutuluka, onse aja akuwona. Anthu onse aja adazizwa kwambiri, nayamba kutamanda Mulungu nkumanena kuti, “Zoterezi ife sitinaziwone nkale lonse.”

Yesu aitana Levi(Mt. 9.9-13; Lk. 5.27-32)

13Yesu adapitanso ku nyanja. Anthu ambirimbiri adafika komweko, ndipo Iye adayamba kuŵaphunzitsa.

14Pamene Yesu ankayenda, adaona Levi, mwana wa Alifeyo, ali pa ntchito m'nyumba ya msonkho. Adamuuza kuti, “Iwe, unditsate.” Iye adanyamuka nkumamutsatadi.

15Tsono pamene Yesu ankadya m'nyumba mwa Leviyo, panali anthu ambiri okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa, odzadya nao ndi Yesuyo ndi ophunzira ake. Anali anthu ambiri ndithu amene adaatsagana naye.

16Pamene aphunzitsi a Malamulo a m'gulu la Afarisi adaona kuti Yesu akudya ndi anthu ochimwa, ndiponso ndi anthu okhometsa msonkho, adafunsa ophunzira ake kuti, “Bwanji akudya pamodzi ndi okhometsa msonkho ndiponso ndi anthu ochimwa?”

17Yesu atamva zimenezo adaŵayankha kuti, “Anthu amene ali bwino sasoŵa sing'anga ai, koma amene akudwala. Inetu sindidabwere kudzaitana anthu olungama, koma anthu ochimwa.”

Za kusala zakudya(Mt. 9.14-17; Lk. 5.33-39)

18Nthaŵi ina ophunzira a Yohane Mbatizi ndiponso Afarisi ankasala zakudya. Anthu adadza kwa Yesu namufunsa kuti, “Kodi bwanji ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala zakudya, koma ophunzira anu ai?”

19Yesu adati, “Kani anzake a mkwati angathe kumasala zakudya pamene mkwati ali nao pomwepo? Chosatheka! Pamene mkwati ali nao pomwepo iwo sangamasale zakudya.

20Koma idzafika nthaŵi pamene adzaŵachotsere mkwatiyo. Pamenepo ndiye azidzasala zakudya.

21“Munthu satenga chigamba cha nsalu yatsopano nkuchisokerera pa chovala chakale. Chifukwa akatero, chigamba chatsopano chija chimakoka nkunyotsolako chovala chakalecho, ndiye kung'ambika kwake kumakhala kwakukulu koposa kale.

22Ndiponso munthu sathira vinyo watsopano m'matumba achikopa akale. Chifukwa akatero, vinyoyo amaphulitsa matumba aja, ndipo choncho vinyo uja amatayika, matumbawo nkutha ntchito. Koma vinyo watsopano amamuthira m'matumba atsopanonso.”

Za tsiku la Sabata(Mt. 12.1-8; Lk. 6.1-5)

23 Deut. 23.25 Pa tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa m'minda ya tirigu. Akuyenda choncho, ophunzira ake adayamba kuthyolako ngala za tirigu nkumadya.

24Apo Afarisi adafunsa Yesu kuti, “Bwanji ophunzira anuŵa akuchita zimene siziloledwa pa tsiku la Sabata?”

25Iye adati, “Bwanji mukuchita ngati simudaŵerenge konse zimene adaachita Davide, pamene iye ndi anzake adaazingwa nayo njala?

26Lev. 24.9

1Sam. 21.1-6 Suja adaaloŵa m'nyumba ya Mulungu, pa nthaŵi imene Abiyatara anali mkulu wa ansembe onse, nkukadya buledi woperekedwa kwa Mulungu? Chonsecho buledi ameneyo nkosaloledwa kuti wina aliyense nkumudya, kupatula ansembe okha. Komanso adaagaŵirako anzake aja amene adaali naye.”

27Tsono Yesu popitiriza mau, adauza Afarisiwo kuti, “Mulungu adaika tsiku la Sabata kuti likhale lothandiza anthu. Sadalenge anthu kuti akhale akapolo a tsiku la Sabata ai.

28Choncho Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro wonse pa zokhudza tsiku la Sabata.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help