1Usalimbane naye munthu wamphamvu,
kuwopa kuti ungagwe m'manja mwake.
2Usakangane naye munthu wolemera,
mwina ngwolemera koposa iwe.
Paja ndalama zidaononga anthu ambiri,
zidasokeretsa ngakhale mitima ya mafumu.
3Usatsutsane ndi munthu wolongolola,
ukatero wamsonkhezera.
4Usamaseka naye munthu wopanda mkhalidwe,
kuti angakunyozere makolo ako.
5Usadzudzule munthu wolapa tchimo lake,
kumbukira kuti tonsefe timalakwa.
6Usanyoze munthu akakalamba,
paja enafensotu tikunka tikukalamba.
7Usasekerere imfa ya mnzako,
kumbukira kuti tonsefe tidzafa.
Za kukumbukira zakale8Usanyoze malangizo a anthu anzeru,
koma uzigwiritsa ntchito kwambiri miyambi yao.
Ukamaŵamvera udzaphunzira nzeru,
ndipo udzadziŵa njira yotumikira akuluakulu.
9Usanyoze nkhani za nkhalamba,
poti nawonso adachita kuphunzira kwa makolo ao.
Angathe kukuphunzitsa kumvetsa zinthu
ndi kudziŵa choyankha pa nthaŵi yake.
Za kuchenjera10Munthu wochimwa usachite kumsonkhezera,
kuwopa kuti ungaonongekerepo iwenso.
11Usaputane naye munthu wachipongwe
kuti angakutchere msampha pokutapa m'kamwa.
12Usakongoze ndalama munthu wamkulu kuposa iwe.
Ukatero, zapita zimenezo.
13Usaperekere wina chikole mopitirira zomwe uli nazo.
Ngati wapereka kale, ukhale wokonzeka kuti ulipire.
14Usamzenge mlandu munthu woweruza,
chifukwa pogamula mlandu zidzakomera iyeyo.
15Usayende ndi munthu wosimbwa
kuti ungadzavutike naye.
Adzangochita zomwe zamudzera m'mutu,
ndiye uchitsiru wake udzaononga aŵiri nonsenu.
16Usakangane ndi munthu wopsa mtima msanga,
usayende naye kopanda anthu.
Iye kupha munthu sayesa kanthu.
Choncho adzakupha pamene palibe wokuthandiza.
17Chitsiru usachikambire zakukhosi,
poti sichingathe kusunga chinsinsi.
18Usachite zinthu zachinsinsi pamaso pa mlendo,
poti sukudziŵa kuti adzachita nazo chiyani.
19Usamauza munthu aliyense maganizo ako,
ukatero udzataya mwai.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.