Yak. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aŵachenjeza kuti asamachite tsankho

1Abale anga, popeza kuti mumakhulupirira Ambuye athu Yesu Khristu, Ambuye aulemerero, musamakondera.

2Mwachitsanzo: munthu wina aloŵa mumsonkhano mwanu atavala mphete zagolide m'manja, alinso ndi zovala zokongola. Winanso nkuloŵa, koma ali mmphaŵi, nsanza zili wirawira.

3Tsono inu pofuna kusamala kwambiri wovala zokongolayo, mumuuza kuti, “Khalani apa pabwinopa”, mmphaŵi uja nkumuuza kuti, “Iwe, kaimirire apo, kapena dzakhale pansi kumapazi kwangaku.”

4Limenelotu ndi tsankho pakati pa inu nokhanokha, ndipo inuyo mwasanduka oweruza a maganizo oipa.

5Mverani, abale anga okondedwa, kodi suja Mulungu adasankha ooneka amphaŵi m'maso mwa anthu, kuti akhale olemera pa chikhulupiriro, ndi kuti alandire madalitso amene Iye adalonjeza anthu omukonda?

6Koma inuyo mwakhala mukumnyoza mmphaŵiyo. Kodi si anthu olemera amene amakupsinjani? Si anthu olemera kodi amene amakukokerani ku mabwalo amilandu?

7Kodi si omwewo amene amalichita chipongwe dzina lolemekezekali la Khristu, limene inu mumatchulidwa?

8Lev. 19.18Tsono mumachita bwino ngati mumatsatadi lamulo lachifumu lija limene limapezeka m'Malembo, lonena kuti, “Uzikonda mnzako monga momwe umadzikondera iwe wemwe.”

9Koma mukamaonetsa kukondera, mukuchimwa, ndipo Malamulo a Mulungu akukutsutsani kuti ndinu opalamula.

10Pajatu munthu wotsata Malamulo onse, akangophonyapo ngakhale pa mfundo imodzi yokha, ndiye kuti wachimwira Malamulo onsewo.

11Eks. 20.14; Deut. 5.18; Eks. 20.13; Deut. 5.17 Pakuti Mulungu amene adanena kuti, “Usachite chigololo”, adanenanso kuti, “Usaphe”. Ngati inu chigololo simuchita, koma kupha mumapha, ndiye kutitu mwachimwira Malamulo onse.

12Tsono muzilankhula ndi kuchita zinthu monga anthu oti Mulungu adzaŵaweruza potsata lamulo loŵapatsa ufulu.

13Paja munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso Mulungu adzamuweruza mopanda chifundo. Koma wochita chifundo alibe chifukwa choopera chiweruzo cha Mulungu.

Za chikhulupiriro ndi ntchito zake

14Abale anga, pali phindu lanji, ngati munthu anena kuti, “Ndili ndi chikhulupiriro,” koma popanda chimene akuchitapo? Kodi chikhulupiriro chotere chingampulumutse?

15Mwachitsanzo: mbale wina kapena mlongo ali ndi usiŵa, ndipo masiku onse alibe chakudya chokwanira.

16Tsono wina mwa inu angoŵauza kuti. “Pitani ndi mtendere, mukafundidwe ndipo mukakhute”, koma osaŵapatsa zimene akusoŵazo, pamenepo phindu lake nchiyani?

17Choncho, chikhulupiriro pachokha, chopanda ntchito zake, nchakufa basi.

18Koma kapena wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro, ineyo ndili ndi ntchito zabwino.” Pamenepo ine nkumuyankha kuti, “Uyesetse kundiwonetsa chikhulupiriro chako chopanda ntchito zakecho, ine ndi ntchito zanga ndikuwonetsa chikhulupiriro changa.”

19Inu mumakhulupirira kuti Mulungu ndi mmodzi yekha. Ai chabwino, mumakhoza, komatu ndi mizimu yoipa yomwe imakhulupirira zimenezi, imachitanso kunjenjemera.

20Wopusawe, kodi ukufuna umboni wotsimikiza kuti chikhulupiriro chopanda ntchito zake nchachabe?

21Gen. 22.1-14; Mphu. 44.19-21; 1Am. 2.52Nanga Abrahamu, kholo lathu, suja adakhala wolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha ntchito yomwe adachita, muja adaapereka mwana wake Isaki pa guwa lansembe?

22Waona tsono kuti chikhulupiriro chake ndi zochita zake zidachitikira pamodzi. Zochita zake zidasandutsa chikhulupiriro chake kuti chifike pake penipeni.

23Gen. 15.6; 2Mbi. 20.7; Yes. 41.8Motero zidachitikadi zimene Malembo adaanena, kuti, “Abrahamu adakhulupirira Mulungu, nchifukwa chake Mulungu adamuwona kuti ngwolungama;” mwakuti ankatchedwa bwenzi la Mulungu.

24Mukuwonatu kuti zochita zake za munthu ndizo zimamsandutsa wolungama pamaso pa Mulungu, osati chikhulupiriro chokha.

25 Yos. 2.1-21 Kodi suja zidaateronso ndi Rahabu, mkazi wadama uja? Iye adaalandira azondi aja, nkuŵabweza kwao poŵadzeretsa njira ina, ndipo adapezeka kuti ngwolungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha zimene adaachitazo.

26Paja monga momwe thupi lopanda mzimu limakhala lakufa, moteronso chikhulupiriro chopanda ntchito zake nchakufa.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help