1Yefita wa ku Giliyadi anali wankhondo wamphamvu. Bambo wake anali Giliyadi, mai wake anali mkazi wadama.
2Giliyadi analinso ndi mkazi amene anali ndi ana. Tsono ana amenewo atakula, adampirikitsa Yefita namuuza kuti, “Sudzalandirako choloŵa m'nyumba ya bambo wathu, pakuti ndiwe mwana wa kwa mkazi wina.”
3Choncho Yefita adaŵathaŵa abale akewo nakakhala m'dziko la Tobu. Kumeneko adakakopa anzake achabechabe kuti azimtsata ndi kunka nasakaza zinthu pamodzi naye.
4Patapita nthaŵi, Aamoni adadzamenyana nkhondo ndi Aisraelewo.
5Ndipo pamene Aamoniwo adadzathira nkhondo Aisraele, akuluakulu a ku Giliyadi adapita kukamtenga Yefita ku dziko la Tobu.
6Akuluakuluwo adauza Yefita kuti, “Bwera udzakhale mtsogoleri wathu kuti timenyane nawo nkhondo Aamoni.”
7Koma Yefita adaŵafunsa akuluakulu a ku Giliyadiwo kuti, “Kodi suja inu mudadana nane nkundipirikitsa ku nyumba ya bambo wanga? Chifukwa chiyani tsopano mwabwera kwa ine poona kuti muli m'mavuto?”
8Apo akuluakuluwo adamuyankha Yefita kuti, “Nchimene tabwerera kwa iwe tsopano lino, kuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo ukhale mtsogoleri wathu wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.”
9Yefita adaŵauza akuluakulu a ku Giliyadiwo kuti, “Mukandibwezeranso kwathu kuti ndikamenye nkhondo ndi Aamoni, ndipo Chauta akandithandiza kuŵagonjetsa, ndidzakhaladi wokulamulirani.”
10Akuluakulu a ku Giliyadi aja adamuuza Yefita kuti, “Chabwino, tikuvomera zimene ukunenazi, Chauta ndiye mboni yathu.”
11Choncho Yefita adapita nawo akuluakulu a ku Giliyadiwo, ndipo anthu akumeneko adamsandutsa mfumu ndi mtsogoleri wao woŵalamulira. Tsono Yefita adabwerezanso kulankhula mau ake omwe aja pamaso pa Chauta ku Mizipa.
12Pambuyo pake Yefita adatuma amithenga kwa mfumu ya Aamoni kukanena kuti, “Kodi ine ndakulakwirani chiyani kuti muzimenyana nkhondo ndi dziko langa?”
13Mfumu ya Aamoniyo idaŵayankha amithenga a Yefita kuti, “Chifukwa chakuti Aisraele, pochoka ku Ejipito, adalanda dziko langa kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki mpakanso ku mtsinje wa Yordani. Tsono mundibwezere dziko mwamtendere.”
14Yefita adatumanso amithenga kwa mfumu ya Aamoni,
15kukanena kuti, “Yefita akuti: Aisraele sadalande dziko la Amowabu kapenanso dziko la Aamoni ai.
16Koma pamene Aisraele ankachoka ku Ejipito, adadzera njira yakuchipululu mpaka ku Nyanja Yofiira nakafika ku Kedesi.
17Num. 20.14-21 Nthaŵi imeneyo Aisraele adatuma amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kukaiwuza kuti, ‘Tapota nanu, mutilole kuti tidzere m'dziko mwanu.’ Koma mfumu ya ku Edomuyo sidafune kumva zimenezo. Adatumanso amithenga ena kwa mfumu ya ku Mowabu, koma nayonso sidavomereze zimenezo. Choncho Aisraele adakhala ku Kedesi.
18Num. 21.4 Pambuyo pake adanyamuka ulendo wao kudzera ku chipululu nazungulira dziko la Edomu ndi dziko la Mowabu, ndipo adafika kuvuma kwa Arinoni. Koma sadaloŵe m'dziko la Mowabu, pakuti mtsinje wa Arinoni unali malire a dziko la Mowabu.
19Num. 21.21-24 Pambuyo pake Aisraele adatuma amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankalamula ku Hesiboni. Aisraelewo adamupempha kuti, ‘Tapota nanu, mutilole kuti tidzere m'dziko mwanu popita kwathu.’
20Koma Sihoni sadaŵalole Aisraele kuti adzere m'dziko mwake. Kenaka Sihoni adasonkhanitsa anthu ake onse, nakamanga zithando zankhondo ku Yahazi, ndipo adamenyana nkhondo ndi Aisraele.
21Koma Chauta, Mulungu wa Aisraele, adampereka Sihoniyo pamodzi ndi anthu ake onse m'manja mwa Aisraele naŵagonjetsa. Choncho Aisraele adalanda chigawo chonse cha dziko la Aamori amene ankakhala m'dzikolo.
22Adalanda chigawo chonse cha dziko la Aamori kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki, ndipo kuyambira ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yordani.
23Choncho ndi Chauta, Mulungu wa Aisraele, amene adalandira Aisraele anthu ake maiko a Aamori. Nanga inu mukufuna kutilandanso maikowo?
24Khalani ndi dziko limene mulungu wanu Kemosi wakupatsani kuti likhale lanu. Koma maiko onse amene Chauta Mulungu wathu watilandira, akhala athu ndithu.
25Num. 22.1-6 Ndiponso kodi inuyo mukupambana Balaki, mwana wa Zipori, mfumu ya ku Mowabu? Kodi iye uja adaaputanapo ndi Aisraele kapena kumenyana nawo nkhondo?
26Pa zaka mazana atatu Aisraele ankakhala ku Hesiboni ndi m'milaga yake, ku Aroere ndi m'milaga yake, ndiponso m'mizinda yonse imene ili m'mbali mwa mtsinje wa Arinoni, nanga chifukwa chiyani simunkalanda malowo nthaŵi imeneyo?
27Choncho ine sindidakuchimwireni, ndipo mukundilakwira pomenyana nane nkhondo. Woweruza ndi Chauta, ndiye amene agamule lero lino pakati pa Aisraele ndi Aamoni.”
28Koma mfumu ya Aamoni sidasamaleko mau amene Yefita adaitumizira.
29Tsono Mzimu wa Chauta udatsikira Yefita, ndipo iye adanyamuka nadzera ku Giliyadi ndi ku Manase. Adakafika ku Mizipa, mzinda wa Giliyadi, ndipo kuchokera ku Mizipako adakafika kumbuyo kwa Aamoni.
30Yefita adalumbira kwa Chauta kuti, “Mukandithandiza kugonjetsa Aamoniŵa,
31aliyense amene atuluke pakhomo pa nyumba yanga kudzandichingamira pobwerera, nditagonjetsa Aamoniwo, adzakhala wake wa Chauta ndipo ndidzampereka kuti akhale nsembe yopsereza.”
32Choncho Yefita adaoloka kunka kwa Aamoni kukamenyana nawo nkhondo. Ndipo Chauta adamthandiza kuŵagonjetsa.
33Adaŵakanthadi kuyambira ku Aroere mpaka pafupi ndi mzinda wa Miniti, mizinda makumi aŵiri pamodzi, ndiponso mpaka ku Abele-Keranimu. Motero Aamoni adagonjetsedwa ndi Aisraele.
Za mwana wamkazi wa Yefita.34Pambuyo pake Yefita adabwerera kwao ku Mizipa. Ndipo adangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamchingamira, akuimba ng'oma ndi kumavina. Iye anali mwana wake mmodzi yekhayo. Analibenso mwana wina, wamwamuna kapena wamkazi.
35Num. 30.2 Yefita atamuwona mwana wake wamkaziyo, adang'amba zovala zake nati, “Kalanga ine, iwe mwana wanga! Wandidula mtima ndipo wandibweretsera mavuto aakulu kopambana, pakuti ndidalonjeza Chauta ndi pakamwa pangapa ndipo sindingathe kubweza malumbiro anga.”
36Mwanayo adayankha kuti, “Atate, ngati mwalonjeza Chauta ndi pakamwa panu, chiteni zimene mwalonjeza, pakuti tsopano Chauta wakuthandizani kulipsira Aamoni, adani anu.”
37Iye adamuuzanso bambo wakeyo kuti, “Mundichitire ichi chokha. Bandilekani miyezi iŵiri ndizikayendayenda ku mapiri, kuti ndizikalira pamodzi ndi anzanga kuti ndikufa ndili namwali.”
38Bambo wakeyo adamuuza kuti, “Pita.” Adamulola kuti apite pa miyezi iŵiri. Choncho mtsikanayo adachoka pamodzi ndi anzake kunka ku mapiri, namakalira kuti akukafa osakwatiwa, opanda mwana.
39Miyezi iŵiriyo itatha, adabwerera kwa bambo wake ndipo adamchita monga momwe adaalonjezera. Namwaliyo anali asanadziŵe mwamuna. Motero chidasanduka chizoloŵezi m'dziko la Aisraele,
40kuti ana aakazi a ku Israele ankapita chaka ndi chaka kukalira maliro a mwana wa Yefita Mgiliyadi uja, masiku anai pa chaka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.