Hos. 14 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Hoseya apempherera Israele

1Inu Aisraele, bwererani kwa Chauta,

Mulungu wanu,

pakuti mwagwa chifukwa cha machimo anu,

2Bwererani kwa Chauta, ndipo mumpemphe kuti,

“Mutikhululukire machimo athu onse.

Mumvere pempho lathu

ndipo tidzakuyamikani ndi mau otamanda.

3Aasiriya sadzatipulumutsa,

akavalo ankhondo sadzatiteteza.

Chimene tidapanga ndi manja athu

sitidzachitchulanso kuti, ‘Mulungu wathu,’

pakuti ndinu amene mumachitira chifundo amasiye.”

Chauta alonjeza moyo watsopano kwa Aisraele

4Chauta akuti,

“Ndidzachiza matenda ao a kusakhulupirika.

Ndidzaŵakonda kwambiri,

pakuti ndaleka kuŵakwiyira.

5Ndidzatsitsimutsa Israele ngati mame.

Adzachita maluŵa ngati kakombo,

adzazika mizu ngati mtengo wa ku Lebanoni.

6Ziphukira zake zidzatambasukira kutali,

adzakhala wokongola ngati mtengo wa olivi,

adzakhala wonunkhira ngati mkungudza wa ku Lebanoni.

7Aisraele adzapezanso chitetezo mwa Ine.

Adzakolola tirigu wambiri,

adzachuluka ngati mphesa.

Adzakhala otchuka ngati vinyo wa ku Lebanoni.

8Kodi Aefuremu adzachita nawonso chiyani mafano?

Ndine amene ndimamva pemphero lao ndi kuŵasamala.

Ndili ngati mkungudza wogudira nthaŵi zonse,

ndine amene ndimaŵapatsa zipatso.”

Mau omariza

9Amene ali wanzeru amvetse zimenezi.

Amene ali womvetsa, azisunge.

Pakuti njira za Chauta nzolungama,

ndipo olungama amayendamo,

koma ochimwa amakhumudwamo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help