1 Yoh. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za ana a Mulungu

1 Yoh. 1.12 Onani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate adatikonda nacho. Adatikonda kwambiri, kotero kuti timatchedwa ana a Mulungu. Ndipo ndifedi ana ake. Anthu odalira zapansipano satidziŵa ifeyo, chifukwa Iyeyonso sadamdziŵe.

2Inu okondedwa, ndife ana a Mulungu tsopano. Mulungu sadatiwonetsebe chimene tidzakhale. Koma tikudziŵa kuti Iye akadzaoneka, tidzakhala ofanafana naye, pakuti tidzamuwona monga momwe aliri.

3Munthu aliyense amene ali ndi chiyembekezo chimenechi pa Khristu, amadzisandutsa woyera monga momwe Khristuyo ali woyera.

4Aliyense amene amachimwa, alinso ndi mlandu wa kuphwanya malamulo. Paja kuchimwa nkuphwanya malamulo kumene.

5Yoh. 1.29Mukudziŵa kuti Khristu adaoneka kuti adzachotse machimo, ndipo mwa Iye mulibe tchimo.

6Munthu aliyense wokhala mwa Khristu, sachimwa. Aliyense amene amachimwa, sadamuwone ndipo sadamdziŵe.

7Ana anga, wina aliyense asakusokeretseni. Munthu amene amachita chilungamo, ngwolungama monga Khristu ali wolungama.

8Munthu amene amachimwa, ndi wa Satana, pakuti Satana ndi wochimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu adaoneka ndi cholinga chakuti aononge zochita za Satana.

9Aliyense amene ali mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza kuti umulungu wake wa Mulunguyo uli mwa iye. Sangathe kumachimwirachimwira, chifukwa ndi mwana wa Mulungu.

10Kusiyana kwake pakati pa ana a Mulungu ndi ana a Satana kumaoneka motere: aliyense wosachita chilungamo, ndiponso wosakonda mnzake, sali mwana wa Mulungu.

Za kukondana

11 Yoh. 13.34 Uthenga umene mudamva kuyambira pa chiyambi ndi wakuti tizikondana.

12Gen. 4.8Tisakhale ngati Kaini amene anali wake wa Woipa uja, ndipo adapha mbale wake. Chomuphera chinali chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoipa, koma za mbale wake zinali zolungama.

13Motero musadabwe abale, anthu odalira zapansipano akamadana nanu.

14Yoh. 5.24Ife tikudziŵa kuti mu imfa tidatulukamo nkuloŵa m'moyo, popeza kuti timakonda anzathu. Munthu amene sakonda mnzake, akali mu imfa.

15Aliyense wodana ndi mnzake, ndi wopha anthu. Ndipo mukudziŵa kuti aliyense wopha anthu, alibe moyo wosatha mumtima mwake.

16Tazindikira chikondi tsopano pakuwona kuti Khristu adapereka moyo wake chifukwa cha ife. Choncho ifenso tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale athu.

17Koma munthu akakhala ndi chuma, ndipo aona mnzake ali wosoŵa, iye nkumuumira mtima namumana, kodi chikondi cha Mulungu chingakhalemo bwanji mumtima mwake?

18Ananu, chikondi chathu chisamangokhala cha nkhambakamwa chabe, koma chiziwoneka pa zochita zathu.

19Apo tidzadziŵa kuti tili pa choona, ndipo tidzakhala okhazika mtima pamaso pa Mulungu

20nthaŵi zonse pamene mtima wathu ukutitsutsa kuti ndife olakwa. Paja Mulungu ndi wamkulu kopambana mtima wathu, ndipo amadziŵa zonse.

21Inu okondedwa, ngati mtima wathu sutitsutsa, titha kuima mopanda mantha pamaso pa Mulungu.

22Ndipo chilichonse chimene timpempha, amatipatsa, chifukwa timatsata malamulo ake, ndipo timachita zomkondweretsa.

23Yoh. 13.34; 15.12, 17Chimene Mulungu amalamula nchakuti tizikhulupirira Mwana wake Yesu Khristu, ndipo kuti tizikondana monga Iye adatilamulira.

24Munthu wotsata malamulo a Mulungu, amakhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu amakhala mwa iye. Chifukwa cha Mzimu Woyera amene adatipatsa, timadziŵa kuti Mulungu amakhaladi mwa ife.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help