1Mafumu onse okhala kuzambwe kwa Yordani adamva zimenezi. Onse okhala ku mapiri, m'zigwa ndiponso m'mbali mwa Nyanja Yaikulu cha kumpoto kwa Lebanoni, nawonso adamva. Ameneŵa ndiwo mafumu a Ahiti, Aamori, Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi.
2Ndiye onseŵa adapangana za kulimbana ndi Yoswa ndi Aisraele onse.
3Tsono Ahivi a ku Gibiyoni atamva zimene Yoswa adaachita mzinda wa Yeriko ndi wa Ai,
4adaganiza zoti amugwire m'maso. Adapita nasenzetsa abulu chakudya cha m'matumba akalekale, ndiponso matumba a vinyo a chikopa cha zigamba zokhazokha.
5Adavala nsapato zothaitha za zigamba zokhazokha, ndiponso zovala zansanza. Buledi amene adatenga anali wouma ndi wachuku.
6Tsono adapita kwa Yoswa ku zithando ku Giligala kuja, namuuza iyeyo pamodzi ndi Aisraele onse kuti, “Ife tachoka ku dziko lakutali, ndipo tikufuna kuti tichite nanu chipangano.”
7Eks. 23.32; 34.12; Deut. 7.2 Koma Aisraele adayankha kuti, “Mwina mwake kwanu nkufupi konkuno. Nanga tingachite nanu chipangano bwanji?”
8Iwo adauza Yoswa kuti, “Ife ndife akapolo anu.” Tsono Yoswa adaŵafunsa kuti, “Kodi inu ndinu yani? Mwachoka kuti?” Anthuwo adamuuza nkhani yonse, adati,
9“Ife tachoka kutali kwambiri, chifukwa choti tamva za Chauta, Mulungu wanu. Tamva mbiri yonse ya zimene Iye adachita ku Ejipito,
10Num. 21.21-35 ndiponso zimene adachita kwa mafumu aŵiri a Aamori kuvuma kwa Yordani, kwa Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndiponso kwa Ogi, mfumu ya ku Basani, imene imakhala ku Asitaroti.
11Tsono atsogoleri athu ndi anthu onse okhala m'dziko lathu adatiwuza kuti, ‘Konzani chakudya chapaulendo, pitani mukakumane nawo anthu amenewo ndipo mukanene kuti, “Ife tadzagonja, chonde mupangane nafe zamtendere.” ’
12Tangoonani bulediyu. Pochoka kwathu, buledi ameneyu anali wofunda ndithu, koma tangoonani ali gwaa ndiponso wochita chuku.
13Pamene tinali kuthira vinyo, matumbaŵa anali atsopano ndithu, koma taonani ngong'ambika. Zovala zathu ndi nsapatozi zangokhala nsanza zokhazokha, chifukwa cha kutalika kwa ulendo.”
14Ndipo Aisraele adalaŵako chakudya chao, osafunsa Chauta.
15Motero Yoswa adapangana nawo za mtendere, nanena kuti sadzaŵapha. Atsogoleri a Aisraelewo adatsimikiza chipanganocho ndi malumbiro.
16Patangopita masiku atatu atachita chipanganocho, Aisraele adaŵazindikira anthuwo kuti ngochokera pafupi.
17Tsono Aisraele adachoka napita kwao kwa anthuwo, napeza kuti mizinda yao inali Gibiyoni, Kefira, Beeroti ndi Kiriyati-Yearimu.
18Komatu Aisraele sadathe kuŵapha anthuwo, poti paja atsogoleri ao anali atalonjeza m'dzina la Chauta, Mulungu wa Israele, za anthu ameneŵa; apo Aisraele ena adayamba kudandaula kwa atsogoleri za zimenezi.
19Koma atsogoleriwo adayankha kuti, “Ife tidaŵalonjeza m'dzina la Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndipo tsopano sitingathe kuŵapha.
20Tiŵalole akhale moyo, kuti ukali wa Mulungu ungatigwere.
21Alekeni akhale moyo, komatu azitidulira nkhuni ndi kumatitungiranso madzi.” Zimenezi ndizo zimene adanena atsogoleri aja.
22Yoswa adaŵaitana Agibiyoniwo, naŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mudatinyenga potiwuza kuti mwachokera kutali, chikhalirecho ndinu a pafupi pompano?
23Popeza kuti mwachita zimenezi, Mulungu wakutembererani. Nthaŵi zonse inu ndiye muzidzatidulira nkhuni, ndi kutitungira madzi ku Nyumba ya Mulungu.”
24Ndipo iwo adayankha kuti, “Mbuyathu, ife tidachita zimenezi chifukwa choti tidamva kuti Chauta, Mulungu wanu, adalamula mtumiki wake Mose kuti adzakupatseni dziko lonseli, ndipo kuti mudzaphe anthu onse kulikonse kumene mukaŵapeze. Motero tidachita zimenezi poti tidakuwopani kwambiri ndipo tidafuna kupulumutsa moyo wathu.
25Tsopano lino, otilamulira ndinu, ndipo mungotichita zimene zingakukomereni,”
26Apo Yoswa adaŵatchinjiriza anthuwo, kuti Aisraele angaŵachite zoipa, kapena kuŵapha.
27Komabe nthaŵi yomweyo, adasanduka odulira anthu nkhuni, ndiponso otunga madzi a ku guwa lansembe la Chauta. Mpakana lero lino, akuchitabe zimenezi ku malo aliwonse amene Chauta adasankha.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.