1 Maf. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mfumukazi ya ku Sheba ibwera kudzachezera Solomoni(2 Mbi. 9.1-12)

1 Mt. 12.42; Lk. 11.31 Mfumukazi ya ku Sheba itamva za mbiri ya Solomoni yobukitsa dzina la Chauta, idadza ku Yerusalemu kudzamuyesa ndi mafunso apatali.

2Idabwera ndi atumiki ambiri ndi ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yamtengowapatali. Itafika kwa Solomoni, idamuuza zonse za kumtima kwake.

3Solomoni adayankha mafunso ake onse. Panalibe kanthu kalikonse kobisika kwa Solomoniyo, kamene sadathe kuimasulira mfumukaziyo.

4Tsono itaona nzeru zonse za Solomoni, nyumba imene adaamanga ija,

5chakudya cha patebulo pake, m'mene zinkakhalira nduna zake, m'mene ankasungira mwambo atumiki ake ndi zovala zao, atumiki ake operekera zakumwa, ndiponso nsembe zake zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Chauta, mfumukaziyo idangoti kukamwa pululu, kusoŵa chonena.

6Pamenepo idauza mfumu Solomoni kuti, “Zimene ndinkamva ndili ku dziko lakwathu, zonena za ntchito zanu ndi nzeru zanu, nzoonadi.

7Zimenezo sindidazikhulupirire, mpaka nditafika ndi kuziwona chamaso. Ndipotu anthu sadaandiwuze zonse, ngakhale ndi theka lomwe. Nzeru zanu ndiponso zabwino zimene muli nazo zikuposa zimene ndinkazimva.

8Ngodala anthu anu. Ngodala atumiki anuŵa, amene amaima pamaso panu nthaŵi zonse ndi kumamva nzeru zanu.

9Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wakondwera nanu, nakukhazikani pa mpando waufumu wa dziko la Israele. Chifukwa choti Chauta adakonda Israele mpaka muyaya, wakuikani kuti mukhale mfumu yolamulira moyenera ndi mwachilungamo.”

10Itanena zimenezo mfumukaziyo idapatsa mfumu Solomoni golide wa makilogramu 4,000, zokometsera chakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yamtengowapatali. Sikudafikenso konse zokometsera zakudya zochuluka chotere zonga zimene mfumukazi ya ku Sheba idapatsa mfumu Solomoni.

11Zombo za mfumu Hiramu nazonso zidabwera ndi golide wa ku Ofiri. Zidatenganso mitengo yambiri ya alimugi ndi miyala yamtengowapatali.

12Mitengo imeneyo mfumuyo idasemera mizati yochirikizira Nyumba ya Chauta ndi ina yochirikizira nyumba yachifumu. Adasemanso azeze ndi apangwe a anthu oimba. Panalibe mitengo yotere imene idabweranso kapena kuwonekanso mu Israele mpaka lero lino.

13Mfumu Solomoni adapatsa mfumukazi ya ku Sheba ija zonse zimene inkafuna, ndiponso chilichonse chimene idaapempha, osaŵerengera mphatso zachifumu zimene anali ataipatsa kale. Tsono mfumukaziyo idabwerera ku dziko lakwao pamodzi ndi atumiki ake aja.

Chuma cha mfumu Solomoni(2 Mbi. 9.13-29)

14Golide amene ankabwera kwa Solomoni pa chaka chimodzi ankakwanira makilogramu 23,000,

15osaŵerengera amene ankabwera ndi alendo ndi anthu amalonda, ndiponso wina wochokera kwa mafumu onse a ku Arabiya, ndi kwa nduna zam'dzikomo.

16Mfumu Solomoni adapangitsa zishango 200 zazikulu za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide pafupi makilogramu asanu ndi awiri.

17Adapanganso zishango 300 zazing'ono za golide wonsansantha. M'chishango chilichonse munkaloŵa golide wokwanira kilogramu limodzi ndi theka. Tsono mfumu idaika zishangozo m'Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni.

18Mfumu idapangitsanso mpando waukulu waufumu wa minyanga yanjovu, niwukuta ndi golide wabwino kwambiri.

19Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi okafikirapo, ndipo chosamira chake unali woulungika pamwamba. Mpandowo unali ndi chosanjikapo manja uku ndi uku, ndipo zifanizo ziŵiri za mikango itaima pambali pa zosanjikapo manjazo.

20Panalinso mikango pa mbali zonse ziŵiri za khwerero lililonse, mikango khumi ndi iŵiri yonse pamodzi. Mpando wotere sudapezekepo mu ufumu wina uliwonse.

21Zikho zonse zimene mfumu Solomoni ankamwera zinali zopangidwa ndi golide. Ziŵiya zonse za ku Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni nazonso zinali za golide weniweni. Panalibe zasiliva popeza kuti silivayo sanali kanthu pa nthaŵi ya Solomoni.

22Mfumu inali ndi zombo zochokera ku Tarisisi zimene zinkayenda pa nyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu; ndipo chaka chachitatu chilichonse zinkabwera zitanyamula golide, siliva, minyanga yanjovu, anyani ndi apusi.

23Motero mfumu Solomoni adapambana mafumu onse a pa dziko lonse lapansi pa chuma ndi pa nzeru.

24Ndipo anthu onse a pa dziko lapansi ankafunafuna kuti amuwone Solomoni ndi kumva nzeru zake zimene Mulungu adaaika mumtima mwake.

25Aliyense mwa iwowo ankabwera ndi mphatso zake, zinthu zasiliva ndi zagolide, zovala, zida zankhondo, zokometsera chakudya, akavalo ndi abulu. Ndipo zimenezi zinkhachitika choncho chaka ndi chaka.

26 1Maf. 4.26 Choncho Solomoni adasonkhanitsa magaleta ndiponso anthu okwera pa akavalo. Magaletawo anali nawo 1,400, anthu okwera pa akavalo analipo 12,000. Adaŵakhazika ena ku mizinda yokhalako ankhondo, ena pafupi ndi mfumu ku Yerusalemu.

27Deut. 17.17 Tsono mu Yerusalemumo mfumu idasandutsa siliva kukhala wambiri ngati miyala wamba. Adasandutsanso mikungudza kukhala wochuluka ngati mikuyu ya m'zigwa.

28Deut. 17.16 Solomoni ankagula akavalo ku Ejipito ndi ku Kuwe. Anthu amalonda a mfumu ankalandirira akavalo ku Kuwe, atapereka ndalama.

29Anthuwo ankagula galeta ku Ejipito pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo kavalo pa mtengo wa masekeli asiliva 150. Momwemonso mafumu onse a Ahiti ndi a ku Siriya, nawonso ankhagula zinthuzo kudzera mwa anthu amalonda omwewo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help