1Pafupi ngati nthaŵi imeneyo mfumu Herode adagwira ena a mu Mpingo kuti aŵazunze.
2Adalamula kuti Yakobe, mbale wake wa Yohane, aphedwe ndi lupanga.
3Ndipo ataona kuti zimenezi zidakondweretsa Ayuda, adapitiriza ndithu nkugwiranso Petro. Zimenezi zidachitika pa masiku a Paska, chikondwerero cha mikate yosafufumitsa.
4 ameneyo.”
16Koma Petro ankangogogodabe. Pamene adamtsekulira nkuwona kuti ndiyedi, adangoti kakasi.
17Petro adakweza dzanja kuti iwo akhale chete, naŵafotokozera m'mene Ambuye adaamtulutsira m'ndende muja. Ndipo adati, “Mumuuze Yakobe ndi abale ena aja zimenezi.” Pamenepo iye adatuluka napita kwina.
18Kutacha, asilikali aja adasokonezeka kwabasi nati, “Petro wapita kuti?”
19Herode adamufunafuna, koma osampeza. Adaŵazenga mlandu alonda aja, nalamula kuti aphedwe. Pambuyo pake Herode adachoka ku Yudeya kupita ku Kesareya, nakakhala kumeneko.
Za imfa ya Herode20 2Am. 9.5-28 Herode adaaŵakwiyira anthu a ku Tiro ndi a ku Sidoni. Tsono anthuwo adadza pamodzi kwa iye. Adaayamba akopa Blasito, kapitao wa ku nyumba ya mfumu kenaka nkukapempha mtendere, chifukwa chakudya cha m'dziko laolo chinkachokera m'dziko la mfumuyo.
21Adapangana tsiku, ndipo pa tsikulo Herode adavala zovala zake zachifumu nkukhala pa mpando wake wachifumu, nayamba kuŵalankhula anthu aja.
22Anthuwo adanena mokweza mau kuti, “Ameneŵa ndi mau a mulungu, osati a munthu ai.”
23Pompo mngelo wa Ambuye, adamkantha Herodeyo chifukwa sadapereke ulemu kwa Mulungu. Mphutsi zidamudya ndipo adafa.
24Koma mau a Mulungu adanka nafalikirafalikira.
25Tsono Barnabasi ndi Saulo atakwaniritsa zimene adaaŵatumira ku Yerusalemu, adabwerako. Adatengako Yohane wotchedwa Marko uja.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.