Yer. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Fanizo la mbiya yophwanyika

1Chauta adandiwuza kuti, “Pita ukagule mtsuko wadothi kwa munthu woumba. Utenge akuluakulu ena, ndiponso ansembe ena okhwimapo.

22Maf. 23.10; Yer. 7.30-32; 32.34, 35 Mupite ku Chigwa cha Benihinomu, pafupi pa Chipata cha Mapale. Kumeneko ukalengeze zimene ndikukuuza tsopano.

3Ukanene kuti, Inu mafumu a ku Yuda ndi onse okhala ku Yerusalemu, imvani mau a Chauta. Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akuti, ‘Ndidzagwetsa tsoka loopsa pa malo ano, kotero kuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka kwambiri.

4Anthu andikana Ine, ndipo aipitsa malo ano. Akhala akufukiza lubani kwa milungu yachilendo imene iwowo, makolo ao ndiponso mafumu a ku Yuda sadaidziŵe. Ndipo pa malo ano adakhetserapo magazi a anthu osachimwa.

5Lev. 18.21 Adamanga nsanja yopembedzerapo Baala, pamene amaperekapo ana ao kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala. Zimenezo sindidalamule konse, sindidazilankhule, ngakhale kuziganiza komwe.

6Nchifukwa chake nthaŵi ikubwera pamene malo ano sadzatchedwanso Tofeti, kapena Chigwa cha Benihinomu, koma Chigwa cha Chipheiphe.

7Pamalo pano ndidzasokoneza maganizo a anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Anthu am'menemo ndidzaŵaphetsa kwa adani ao ku nkhondo, ndipo ndidzaŵakanthitsa kwa anthu oŵazonda. Mitembo yao ndidzaisandutsa chakudya cha mbalame zamumlengalenga ndi zilombo za pa dziko lapansi.

8Mzinda umenewu ndidzausandutsa malo ochititsa nyansi ndiponso odzetsa mfuu wa mantha. Aliyense wodutsapo adzachita nawodi nyansi ndipo adzafuula ndi mantha poona kukanthidwa kwake.

9Ndidzaumiriza anthuwo kuti adye ana ao omwe aamuna ndi aakazi. Adzadyana choncho pa nthaŵi yoopsa pamene adzazingidwa ndi adani ao ofuna kuŵazunza.’

10“Tsono iweyo udzaphwanye mtsuko uja, anthu amene udzapite nawowo akuwona.

11Ndiye udzaŵauze kuti, Chauta Wamphamvuzonse akuti, Umu ndi m'mene ndidzaonongere anthu ameneŵa, monga momwe woumba amaphwanyira mbiya yake, kotero kuti sangathenso kuikonza. Anthu akufawo adzaŵaika ku Tofeti, chifukwa choti kwina kulikonse sikudzakhala malo oŵaika.

12Umu ndimo m'mene ndidzaŵachitire malo ano pamodzi ndi anthu ake omwe. Mzindawu ndidzausandutsa ngati Tofeti.

13Nyumba za ku Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti, chifukwa ndizo nyumba zimene pa madenga ao ankaotcherapo nsembe kwa milungu ya mumlengalenga, namapereka nsembe yazakumwa kwa milungu ina.”

14Pambuyo pake Yeremiya adabwerako ku Tofeti kumene Chauta adaamtuma kuti akalose, naimirira m'bwalo la Nyumba ya Chauta. Ndipo adauza anthu onse kuti,

15“Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, akunena kuti, Ndidzagwetsa tsoka pa mzinda uwu pamodzi ndi pa midzi yake yonse monga ndidaanenera, chifukwa choti anthu ake ndi okanika, ndipo akukana kumvera mau anga.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help