1 Mbi. 23 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 1Maf. 1.1-40 Davide atakalamba, masiku ake atatha, adaika Solomoni mwana wake kuti akhale mfumu ya Israele.

Ntchito za Alevi

2Davide adasonkhanitsa atsogoleri onse a Israele, ansembe ndi Alevi.

3Adaŵerenga Aleviwo kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo. Chiŵerengero chao chinali anthu 38,000.

4Ndipo adati, “Mwa ameneŵa anthu 24,000 adzakhale oyang'anira ntchito za m'Nyumba ya Chauta. Anthu 6,000 adzakhale nduna ndi aweruzi,

5anthu 4,000 adzakhale alonda apakhomo, ndipo anthu 4,000 enawo azidzatamanda Chauta ndi zipangizo zoimbira zimene ndazipereka kuti zikhale zotamandira Chauta.”

6Pambuyo pake Davide adaŵagaŵa anthuwo m'magulumagulu kutsata ana aŵa a Levi: Geresomo, Kohati ndi Merari.

7Ana a Geresomo anali Ladani ndi Simei.

8Ana a Ladani anali atatu: Yehiyele mtsogoleri, Zetamu ndi Yowele.

9Ana a Simei anali atatu: Selomoti, Haziyele ndi Harani. Ameneŵa ndiwo amene anali atsogoleri a mabanja a makolo a Ladani.

10Ana a Simei anali Yahati, Ziza, Yeusi ndi Beriya. Anai ameneŵa anali ana a Simei.

11Yahati anali mtsogoleri, ndipo Ziza anali wachiŵiri wake. Koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri, nchifukwa chake adaŵaŵerengera ngati makolo a banja limodzi.

12Ana a Kohati anali anai: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele.

13Eks. 28.1 Ana a Amuramu anali Aroni ndi Mose. Aaroni adampatula kuti aziyang'anira zinthu zopatulika za Mulungu. Iyeyo ndi ana ake ankapereka nsembe zofukiza pamaso pa Chauta mpaka muyaya, ndipo ankatumikira ndi kudalitsa anthu m'dzina la Chautayo mpaka muyaya.

14Koma ana a Mose, munthu wa Mulungu uja, adaŵawerengera pamodzi ndi fuko la Levi.

15Ana a Mose anali Geresomo ndi Eliyezere.

16Ana a Geresomo mtsogoleri wao anali Sebuele.

17Eliyezere anali ndi mwana mmodzi yekha dzina lake Rehabiya. Rehabiyayu anali ndi ana ambirimbiri.

18Mtsogoleri wa ana a Izara anali Selomiti.

19Ana a Hebroni naŵa: Yeriya mtsogoleri, wachiŵiri Amariya, wachitatu Yahaziele ndipo wachinai anali Yekameamu.

20Ana a Uziyele naŵa: Mika mtsogoleri, ndipo wachiŵiri anali Isiya.

21Ana a Merari naŵa: Mali ndi Musi. Ana a Malai naŵa: Eleazara ndi Kisi.

22Eleazara adafa opanda ana aamuna, koma aakazi okhaokha. Abale ao, ana a Kisi, ndiwo amene adaŵakwatira.

23Ana atatu a Musi naŵa: Mali, Edere ndi Yeremoti.

24Ameneŵa ndiwo amene anali ana a Levi potsata atsogoleri a mabanja a makolo ao, monga m'mene adalembedwera. Ankatsata chiŵerengero cha anthu kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo. Ameneŵa ndiwo amene ankayenera kugwira ntchito yotumikira ku Nyumba ya Chauta.

25Paja Davide adaati, “Chauta Mulungu wa Israele wapatsa anthu ake mtendere. Ndipo adzakhala ku Yerusalemu mpaka muyaya.

26Deut. 10.8 Motero nkosafunikiranso kuti Alevi azisenza chihema chija kapena zipangizo za chipembedzo.”

27Potsata mau omalizira a Davidewo, ameneŵa ndiwo anali chiŵerengero cha Alevi, kuyambira anthu a zaka makumi aŵiri ndi kupitirirapo.

28Num. 3.5-9 “Ntchito yao idzakhala yothandiza ana a Aroni pa ntchito yaunsembe ya ku Nyumba ya Chauta. Azidzasamala mabwalo ndi zipinda, kuyeretsa zonse zimene zili zopatulika, ndiponso azidzagwira ntchito ina iliyonse ya ku Nyumba ya Chauta.

29Ali nayonso ntchito yosamalira buledi wopatulika, ufa wa nsembe yaufa, mitanda ya buledi wosatupitsa, nsembe zopereka m'chiwaya, nsembe yosanganiza ndi mafuta. Alinso ndi ntchito yoyesa ndi kupima nsembe zonse zoperekedwa m'Nyumba ya Chauta.

30M'maŵa mulimonse azithokoza ndi kutamanda Chauta. Aziteronso ndi madzulo omwe.

31Ndipo azitero nthaŵi zonse akamapereka kwa Chauta nsembe zopsereza za masiku a Sabata, za pokhala mwezi uliwonse, ndiponso za pa chikondwerero china chilichonse chachipembedzo. Ntchito zotumikira Chautazi adzazichita kwamuyaya.

32Motero azidzayang'anira chihema cha msonkhano ndiponso malo opatulika, ndipo azidzathandiza abale ao, zidzukulu za Aroni, potumikira ku chihema chamsonkhano.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help