1 Ezek. 26.1—28.19; Yow. 3.4-8; Amo. 1.9, 10; Zek. 9.1-4; Mt. 11.21, 22; Lk. 10.13, 14 Nawu ulosi wonena za Tiro.
Fuulani mwachisoni,
inu oyendetsa zombo za ku Tarisisi!
Pakuti mzinda wa Tiro waonongeka,
kulibenso nyumba kapena dooko!
Zimenezi adazimva pochokera ku Kitimu.
2Khalani chete, inu anthu okhala
m'mphepete mwa nyanja,
inu amalonda a ku Sidoni!
Amithenga anu adaoloka nyanja,
ndipo adayenda pa nyanja zazikulu.
3Phindu lanu linali tirigu wa ku Sihore,
zokolola za ku Nailo,
ndipo munkachita malonda
ndi anthu a mitundu yonse.
4Chita manyazi, iwe Sidoni,
mzinda wamalinga wakunyanja,
chifukwa nyanjayo yalankhula, yanena kuti,
“Sindinamvepo zoŵaŵa za kubala,
sindinaberekepo ana,
ndipo sindinalerepo mwana,
wamwamuna kapena wamkazi.”
5Aejipito adzadzidzimuka ndi kuchita mantha,
akadzamva kuti Tiro adaonongeka.
6Thaŵirani ku Tarisisi,
fuulani mwachisoni, inu okhala
m'mphepete mwa nyanja.
7Kodi ndi uwu mzinda wa Tiro wotchukawu,
mzinda wakalekale uja?
Kodi ndi uwu mzinda uja unkatumiza anthu
kuwoloka nyanja kukakhala ku maiko ena?
8Kodi ndani amene adakonza zimenezi
kuti zigwere Tiro,
mzinda uja wopereka ukulu kwa anthuwu,
umene amalonda ake anali akalonga
ndiponso otchuka kwambiri pa dziko lonse lapansi?
9Chauta Wamphamvuzonse ndiye adakonza zimenezi
kuti athetse kunyada kwao,
kuti atsitse anthu onse olemekezeka a pansi pano.
10Mubalalike m'dziko mwanu
ngati mtsinje wa Nailo,
inu anthu a ku Tarisisi.
Palibenso china choti nkukutchinjirizani.
11Chauta watambalitsa dzanja lake
kuloza nyanja ndipo wagwedeza maufumu.
Walamula a ku Kanani kuti agwetse malinga ao.
12Ndipo adati, “Simudzakondwanso,
inu anthu a mu mzinda wa Sidoni,
mudzapanikizidwa,
ndipo ngakhale muthaŵire ku Kitimu,
nkumeneko komwe simukapeza mpumulo.”
13Onani dziko la Ababiloni, anthu ameneŵa palibenso, adatheratu. Aasiriya ndi amene asandutsa Tiro kuti akhale malo a zilombo. Adamanga nsanja zao zankhondo, adagumula malinga ake nasandutsa mzindawo bwinja.
14Lirani kwambiri, inu oyendetsa zombo a ku Tarisisi, chifukwa mzinda wanu wamalinga wagwetsedwa.
15Nthaŵi ikubwera pamene Tiro adzaiŵalika pa zaka makumi asanu ndi aŵiri, imene ili ngati nthaŵi ya moyo wonse wa mfumu imodzi. Zitatha zaka zimenezo, Tiro adzakhala ngati mkazi wachiwerewere uja woimbidwa nyimbo ija yakuti:
16“Tenga zeze wako,
uzungulire mzinda,
iwe mkazi wachiwerewere woiŵalika.
Uimbe zezeyo mokometsera,
uimbenso nyimbo zako zija,
kuti anthu akukumbukire.”
17Zitatha zaka makumi asanu ndi aŵiri, Chauta adzachitapo kanthu pa Tiro. Mzindawo udzabwerera ku ganyu wake wakale uja. Ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu a dziko lonse lapansi.
18Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Chauta. Sadzachita nazo kaligwiritsa kapena kuzikundika, koma adzazipereka kwa otumikira Chauta, kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.