1Chauta, Mulungu Wamphamvu uja, akulankhula,
akuitana anthu a ku dziko lonse lapansi,
kuyambira kotulukira dzuŵa
mpaka koloŵera kwake.
2Mulungu akuŵala atakhala m'Ziyoni,
mzinda wake wokongola kotheratu.
3Mulungu wathu akubwera, sakhala chete.
Patsogolo pake pali moto wonyeketsa,
M'mbali mwake monse muli mkuntho wamphamvu.
4Amaitana zamumlengalenga ndi za pansi pano,
kuti zichite umboni pamene akuweruza anthu ake.
5Iye akuti,
“Sonkhanitsani pamaso panga,
anthu anga okhulupirika,
amene adachita chipangano ndi Ine popereka nsembe.”
6Zamumlengalenga zikulalika chilungamo cha Mulungu,
pakuti Iye mwini ndiye muweruzi.
7“Imvani anthu anga, Ine ndidzalankhula.
Ndidzapereka umboni wokutsutsani inu Aisraele.
Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.
8“Sindikudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu,
popeza kuti mumapereka nsembe zanu zopsereza
kwa Ine nthaŵi zonse.
9Ndithudi, sindilandira ng'ombe
kapena mbuzi iliyonse ya m'makola anu.
10“Popeza kuti nyama iliyonse yam'nkhalango
ndi yanga,
pamodzi ndi nyama zonse zokhala ku mapiri ochuluka.
11Mbalame zonse zamumlengalenga,
zamoyo zonse zoyenda ku thengo ndi zanga.
12“Ndikadakhala ndi njala sindikadakuuzani,
pakuti dziko lonse ndi zonse zam'menemo, ndi zanga.
13Kodi ndimadya nyama yang'ombe
kapena magazi ambuzi?
14“Koma perekani nsembe zanu zothokozera kwa Mulungu,
ndipo muchite zimene mudalumbira kwa Wopambanazonse.
15Mupemphere kwa Ine pa tsiku lamavuto.
Ine ndidzakupulumutsani,
ndipo inu mudzandilemekeza.”
16Koma kwa munthu woipa Mulungu amati,
“Ukuvutikiranji ndi kutchula malamulo anga?
Bwanji pakamwa pako pakulankhula za chipangano changa?
17Iwe sufuna kulangizidwa,
umaponya mau anga ku nkhongo.
18“Ukaona mbala umasanduka bwenzi lake,
ndipo umayenda ndi anthu achigololo.
19Suwopa kulankhula zoipa pakamwa pako,
lilime lako limapeka mabodza.
20“Umakhala pansi
nkumachitira mbale wako miseche,
inde, umasinjirira mbale wako weniweni.
21Iwe wachita zinthu zimenezi,
ndipo Ine ndakhala ndili chete.
Unalikuganiza kuti ndimafanafana nawe.
Koma tsopano ndikukudzudzula
ndi kukuwonetsa zimene wachita.
22“Ganizani bwino izi tsono,
inu amene mumaiŵala Mulungu,
kuti ndingakukadzuleni,
ndipo palibe amene angakupulumutseni.
23Koma wopereka mtima wake kwa Ine mothokoza,
ndiye amene amandilemekeza.
Woyenda m'njira zolungama,
ndidzamuwonetsa chipulumutso changa.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.