1 Yer. 25.1-38; Dan. 1.1, 2 Pa nthaŵi ya Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adadzathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo Yehoyakimu adakakamizidwa kutumikira Nebukadinezarayo zaka zitatu. Koma pambuyo pake Yehoyakimuyo adapandukira Nebukadinezara.
2Tsono Chauta adatumiza magulu ankhondo a Ababiloni, a Asiriya, a Amowabu, ndi a Aamoni kuti akathire nkhondo Yuda, mpaka kuwononga dzikolo, monga momwe Chauta adaanenera kudzera mwa atumiki ake aneneri.
3Zoonadi, zimenezi zidagwera Yuda, monga momwe Chauta adaalamulira. Adachotsa Ayudawo pamaso pake, chifukwa cha zoipa zimene mfumu Manase ankachita,
4ndiponso chifukwa cha magazi a anthu osachimwa amene iye adakhetsa. Manaseyu adadzaza Yerusalemu ndi magazi a anthu osachimwa, ndipo Chauta sadamkhululukire ai.
5Tsono ntchito zina za Yehoyakimu ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
6Motero Yehoyakimu adamwalira, naikidwa m'manda. Ndipo Yehoyakini mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
7Nthaŵi imeneyo mfumu ya ku Ejipito sidatulukenso m'dziko lake, poti mfumu ya ku Babiloni inali italanda maiko onse a mfumu ya ku Ejipito kuchokera ku mtsinje wa ku Ejipito mpaka ku mtsinje wa Yufurate.
Yehoyakini mfumu ya ku Yuda8Yehoyakini anali wa zaka 18 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira miyezi itatu ku Yerusalemu. Mai wake anali Nehusita, mwana wa Elinati, wa ku Yerusalemu.
9Yehoyakini adachita zoipa pamaso pa Chauta potsata zonse zimene ankachita bambo wake.
10Nthaŵi imeneyo ankhondo a Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, adadza ku Yerusalemu, nazinga mzindawo ndi zithando zankhondo.
11Ndipo Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adafika ku mzindawo pa nthaŵi imene ankhondo ake ankauzinga.
12Yer. 22.24-30; 24.1-10; 29.1, 2 Tsono Yehoyakini mfumu ya ku Yuda adadzipereka kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi mai wake, alangizi ake, nduna zake ndiponso akuluakulu a kunyumba kwake. Mfumu ya ku Babiloni idamgwira Yehoyakini ukapolo pa chaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake.
13Adatenga chuma chonse cha ku Nyumba ya Chauta, pamodzi ndi chuma chonse cha ku nyumba ya mfumu. Adaononga ziŵiya zonse zagolide za ku Nyumba ya Chauta zimene Solomoni mfumu ya ku Israele adapanga.
14Adatenga anthu onse a ku Yerusalemu, ndiye kuti nduna zonse ndi anthu onse amphamvu. Onsewo pamodzi analipo 10,000. Adatenganso anthu onse aluso ndi amisiri osula. Sadatsalepo ndi mmodzi yemwe, kupatula anthu osauka okha am'dzikomo.
15Ezek. 17.12 Nayenso Yehoyakini adamtenga kupita naye ku Babiloni. Adatenganso mai wake wa mfumuyo, akazi ake, nduna zake ndiponso anthu omveka am'dzikomo. Onsewo adaŵagwira ukapolo ku Yerusalemu kunka nawo ku Babiloni.
16Tsono mfumu ya ku Babiloni idagwira ukapolo anthu otchuka onse okwanira 7,000, ndiponso anthu aluso pamodzi ndi amisiri osula 1,000. Onsewo anali amphamvu odziŵa kumenya nkhondo.
17Yer. 37.1; Ezek. 17.13 Kenaka mfumu ya ku Babiloni idalonga ufumu Mataniya, malume wa Yehoyakini, m'malo mwake, ndipo adasintha dzina lake kuti akhale Zedekiya.
Zedekiya mfumu ya ku Yuda(2 Mbi. 36.11-12; Yer. 52.1-3a)18 Yer. 27.1-22; 28.1-17 Zedekiya anali wa zaka 21 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Hamutala, mwana wa Yeremiya, wa ku Libina.
19Zedekiyayo adachita zoipa pamaso pa Chauta potsata zonse zimene ankachita Yehoyakimu.
20Ezek. 17.15 Chifukwa cha zonse zimene zidachitika ku Yerusalemu ndi ku Yudazi, Chauta adakwiya kwambiri, mpaka kuŵachotsa anthuwo pamaso pake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.