1Chauta adauza Yeremiya kuti,
2“Imva mau a chipangano ichi, ndipo ulankhule nawo anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu.
3Uŵauze kuti mau a Chauta, Mulungu wa Israele, ndi aŵa: Atembereredwe munthu amene sasunga mau a chipangano,
4chimene ndidachita ndi makolo anu, nditaŵatulutsa ku dziko la Ejipito. Nditaŵachotsa m'ng'anjo ya moto ija, ndidati, ‘Mukamandimvera ndi kumachita zimene ndikuuzani, inu mudzakhala anthu anga, Ine ndidzakhala Mulungu wanu.
5Choncho ndidzachita zimene ndidalonjeza makolo anu molumbira, zakuti ndidzaŵapatsa dziko lamwanaalirenji, dziko limene mukukhalamoli.’ ” Tsono ine ndidayankha kuti, “Zikhale momwemo, Inu Chauta.”
6Tsono Chauta adandiwuza kuti, “Ulalike mau onseŵa ku mizinda ya ku Yuda ndi m'miseu ya mu Yerusalemu. Uŵauze kuti, ‘Imvani mau a chipangano ichi, ndipo muŵasunge.
7Nthaŵi ndi nthaŵi ndakhala ndikuŵachenjeza makolo anu kuyambira pamene ndidaŵatulutsa ku dziko la Ejipito mpaka lero lino. Ndakhala ndikuŵauza kuti, “Mverani mau anga.”
8Koma sadamvere, sadalabadeko. Aliyense adangoti nkhongo gwa, kutsata makhalidwe a mtima wake woipa. Ndidaŵalamula kuti asunge chipangano changa, koma iwo sadachisunge. Nchifukwa chake ndidaŵalanga monga m'mene ndidaanenera.’ ”
9Kenaka Chauta adandiwuza kuti, “Anthu a ku Yuda ndi anthu a mu Yerusalemu andiwukira.
10Abwereranso ku machimo a makolo ao amene adakana kundimvera. Akutsata milungu ina ndi kumaipembedza. A ku Israele ndi a ku Yuda aphwanya chipangano chimene ndidapangana ndi makolo ao.
11Nchifukwa chake Ine Chauta ndikunena kuti ndidzaŵagwetsa m'mavuto amene sangathe kuŵalewa. Ngakhale alire kwa Ine, sindidzamvera.
12Anthu a m'mizinda ya ku Yuda ndi a mu Yerusalemu adzapita kukalirira chithandizo kwa milungu imene ankaperekako nsembe. Koma singathe kuŵapulumutsa pa nthaŵi ya mavuto ao.
13Zoonadi, iwe Yuda, milungu yako yachuluka ngati chiŵerengero cha midzi yako. Maguwa ootcherapo nsembe kwa Baala achuluka ngati miseu ya mu Yerusalemu.
14Tsono iwe Yeremiya, usaŵapempherere anthu ameneŵa. Usaŵapepesere kwa Ine kapena kuŵadandaulira. Ndithu, Ine sindidzaŵamvera akadzandiitana pa nthaŵi ya mavuto ao.
15Kodi anthu anga okondedwa adzachitanji m'Nyumba mwanga? Suja iwowo achita zoipa kwambiri? Kodi malumbiro anu ndi nyama zopereka ku nsembe zingathe kukutetezani ku tsoka lanu?
16Kale Chauta ankakuyerekezani ndi mtengo wa olivi wa masamba obiriŵira ndi wa zipatso zokongola. Koma tsopano adzautentha ndi mkuntho wamkokomo, ndipo nthambi zake zidzapserera.
17Chauta Wamphamvuzonse, yemwe adakubzalani, ndiye wagamula kuti adzakulangani koopsa, chifukwa cha zoipa zimene mudachita, inu a m'banja la Israele ndi la Yuda. Mwamukwiyitsa pakupereka nsembe zopsereza kwa Baala.”
Anthu amchita chiwembu Yeremiya18Chauta adandiwululira,
ndipo ndidadziŵa za chiwembu cha anthu.
Iye adatsekula maso anga
nandiwonetsa ntchito zao zoipa.
19Ndidakhala ngati mwanawankhosa
amene akupita naye kokamupha.
Sindidadziŵe kuti chidaloza pa ine
chiwembu chimene ankakonzekera nkumanena kuti,
“Tiyeni tiwudule mtengowu ukali moyo.
Tiyeni timuphe munthu ameneyu,
kuti asadzakumbukikenso.”
20 Lun. 1.6-9 Inu Chauta Wamphamvuzonse
amene mumaweruza molungama,
amene mumayesa mtima ndi maganizo,
onetseni kuti mwaŵalipsira,
pajatu ndidadzipereka m'manja mwanu!
21Nchifukwa chake Chauta akunena za anthu a ku Anatoti amene afuna kuwononga moyo wanga namanena kuti, “Usalosenso m'dzina la Chauta kuti tingakuphe.”
22Nchifukwa chake Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Ndidzaŵalanga. Anyamata ao adzaphedwa ku nkhondo. Ana ao aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala.
23Sadzapulumuka ndi mmodzi yemwe, chifukwa ndidzaononga anthu a ku Anatoti, chikadzafika chaka chao cha chilango.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.