Yuda 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 mtumiki wa Yesu Khristu, ndiponso mbale wa Yakobe. Ndikulemba kalatayi kwa inu amene Mulungu adakuitanani, amene Mulungu Atate athu amakukondani ndi kukusungani, kusungira Yesu Khristu.

2Mulungu achulukitse chifundo chake, mtendere wake ndi chikondi chake kwa inu.

Za aphunzitsi onyenga

3Inu okondedwa, ndinkafunitsitsa kukulemberani kalata, kuti ndikufotokozereni za chipulumutso chokhudza tonsefe. Ndiye mtima wanga udandikakamiza kuti ndikulembereni tsopano ndi kukupemphani kolimba, kuti mumenye ndithu nkhondo yotchinjiriza chikhulupiriro, chimene Mulungu adapatsa anthu ake kamodzi kokhako.

4Paja anthu ena osasamala za Mulungu adaloŵa mobisika pakati panu. Iwo amapotoza kukoma mtima kwa Mulungu, ndi kukuyesa ufulu wochitira zonyansa. Amakana Yesu Khristu, amene Iye yekha ndiye Mbuye wathu ndi Mfumu yathu. Zakuti anthu ameneŵa adzalangidwa zidalembedwa kale lomwe.

5 yemwe, mkulu wa angelo, pamene iye ankakangana ndi Satana ndi kutsutsana naye za mtembo wa Mose, sadafune kutchuliliza mwachipongwe kuti ndi wolakwa. Adangoti, “Ambuye akulange!”

10Koma anthu ameneŵa amachita chipongwe zinthu zimene sazidziŵa. Ndipo zinthu zimene amazidziŵa ndi nzeru zachibadwa, zonga za nyama, ndizo zimene zimaŵaononga.

11Gen. 4.3-8; Num. 22.1-35; Num. 16.1-35 Iwoŵa ali ndi tsoka, chifukwa adatsata njira ya Kaini. Monga adaachitira Balamu, iwonso adagwa m'cholakwa chifukwa chotsata phindu la ndalama. Adaonongeka chifukwa cha kuukira Mulungu, monga adaachitira Kora.

12Ameneŵa ndiwo amaipitsa maphwando anu achikondi. Amadya nanu mochitisa manyazi, nangosamala za iwo okha. Ali ngati mitambo youluzika ndi mphepo, koma osadzetsa mvula. Ali ngati mitengo yosabala zipatso ngakhale pa nyengo yake, imene idaferatu ndipo anthu adaizula.

13Ali ngati mafunde aukali apanyanja, amene amatulutsa thovu la zonyansa zao. Ali ngati nyenyezi zosokera, ndipo Mulungu akuŵasungira mdima wandiweyani mpaka muyaya. Mbiri iyi idadziŵika pakati pa Aisraele, koma siinalembedwe m'Chipangano Chakale.

14 Gen. 5.18, 21-24 Enoki, wa mbadwo wachisanu ndi chiŵiri kuyambira pa Adamu, adaalosa za anthu okhaokhaŵa pamene adati, “Onani, Ambuye akubwera ndi angelo ake osaŵerengeka,

15kuti adzaweruze anthu onse. Adzagamula kuti ngolakwa onse osasamala za Mulungu, chifukwa cha ntchito zao zonse zosalungama, zimene adachita mosaopa Mulungu. Adzaŵatsutsa chifukwa cha mau onse achipongwe amene iwo, anthu ochimwa ndi onyozera za Mulungu, adanyoza nawo Ambuye.”

16Anthu ake ndi aŵa: ong'ung'udza, odandaula, ndi omangotsata zilakolako zao zoipa. Amalankhula zonyada, ndipo amangotamanda anthu moshashalika chifukwa chofuna kupezerapo phindu.

Machenjezo ndi malangizo

17Koma inu okondedwa, muzikumbukira mau amene atumwi a Ambuye athu Yesu Khristu adaneneratu.

182Pet. 3.3Paja adakuuzani kuti, “Pa masiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, otsata zilakolako zao zoipa.”

19Anthu ameneŵa ndi oyambitsa mipatuko. Amangotsata zapansipano, ndipo mumtima mwao alibe Mzimu Woyera.

20Koma inu okondedwa, muzithandizana kuti uzikulirakulira moyo wanu, umene udakhazikika pa maziko a chikhulupiriro chanu changwiro. Muzipemphera ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

21Mudzisunge m'chikondi cha Mulungu podikira moyo wosatha, umene Ambuye athu Yesu Khristu adzakupatseni mwa chifundo chake.

22Pali ena amene ali okayika, amenewo muziŵachitira chifundo.

23Koma ena muŵapulumutse pakuŵalanditsa ku moto. Enanso muŵachitire chifundo, koma mwamantha, muzidana ngakhale ndi chovala chao chomwe choipitsidwa ndi machimo.

Mau olemekeza Mulungu

24Akhale ndi ulemerero Iye amene angathe kukusungani kuti mungagwe m'machimo, amene angathenso kukufikitsani pamaso pa ulemerero wake, muli okondwa ndi opanda chilema konse.

25Mulungu, amene Iye yekha ndiye Mpulumutsi wathu mwa Yesu Khristu Ambuye athu, akhale ndi ulemerero, ukulu, mphamvu ndi ulamuliro, isanayambe nthaŵi, tsopano, ndi mpaka muyaya. Amen.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help