1Maiko amene Aisraele adalandira ku Kanani adagaŵidwa motere: Wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri a mabanja a mafuko a Aisraele, onseŵa ndiwo adagaŵa maikowo, kugaŵira Aisraele.
2 kwa mafuko asanu ndi anai ndi theka.
3Num. 32.33; 34.14, 15; Deut. 3.12-17 Mose adagaŵira mafuko aŵiri ndi theka aja magawo ao a dziko kuvuma kwa Yordani, koma Alevi okha sadaŵagaŵire.
4Tsono fuko la Yosefe adaligaŵa paŵiri, Manase ndi Efuremu. Alevi sadalandire gawo lililonse la dziko. Adangolandira mizinda kuti azikhalamo ndi timaiko todyetsamo zoŵeta zao.
5Aisraelewo adangogaŵana dzikolo potsata zimene Chauta adaalamula Mose.
Apereka Hebroni kwa Kalebe.6 Num. 14.30 Anthu a fuko la Yuda adabwera kwa Yoswa ku Giligala. Kalebe mmodzi mwa iwowo, mwana wa Yefune Mkenizi, adauza Yoswa kuti, “Inu mukudziŵa zimene Chauta adauza Mose, munthu wa Mulungu uja, za inu ndi ine ku Kadesi-Baranea.
7Num. 13.1-30 Nthaŵi imene ija ndinali ndi zaka makumi anai pamene Mose mtumiki wa Chauta adandituma kuchokera ku Kadesi-Baranea kukazonda dziko lija. Nditabwerako, ndidamuuzadi zoona zonse zimene ndidaona.
8Komabe anthu amene anali nane pa ulendowo, adachititsa mantha anthu. Koma ine ndidamvera mokhulupirika Chauta, Mulungu wanga.
9Num. 14.24 Pamenepo Mose adandilonjeza kuti, ‘Chifukwa choti wamvera mokhulupirika Chauta, Mulungu wanga, iweyo pamodzi ndi ana ako, udzalandiradi dziko limene walipondalo, kuti likhale choloŵa chako.’ ”
10Kalebe adapitiriranso kunena kuti, “Koma tsopano, papita zaka 45 Chauta atauza kale Mose zimenezi. Taonani, ndili ndi zaka 85 tsopano,
11komabe ndikadali ndi mphamvu lero, monga ndidaaliri muja, pamene Mose adandituma. Ndikadali wamphamvu, mwakuti ndingathe kumenya nkhondo ndithu, ndiponso ndingathe kuchita zina zonse.
12Tsopano mundigaŵire dziko lamapiri lomwe Chauta adandilonjezeratu. Paja mudamva kuti Aanaki, anthu amphamvu, adalipodi kumeneko m'mizinda yao yamalinga. Komabe mwina Chauta adzakhala nane, ndipo ndidzaŵapirikitsa monga momwe Chauta adanenera.”
13Pamenepo Yoswa adadalitsa Kalebe, mwana wa Yefune, nampatsa Hebroni kuti likhale dziko lake.
14Mpaka lero lino dziko la Hebroni ndi la zidzukulu za Kalebe, mwana wa Yefune Mkenizi, poti adamvera mokhulupirika Chauta, Mulungu wa Aisraele.
15Zisanachitike zimenezi, Hebroni ankatchedwa Kiriyati-Ariba. Arabayo ndiye anali wotchuka kopambana pakati pa Aanaki. Pambuyo pake m'dziko lonselo mudakhala mtendere.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.