1 Eks. 20.16; Lev. 19.11, 12; Deut. 5.20 “Usachite umboni wonama. Munthu wolakwa usamthandize pakumchitira umboni wonama.
2Ngakhale anthu ambiri akamachita choipa, usamavomerezana nawo. Ndipo usamapereka umboni wopotoza chiweruzo m'bwalo lamilandu, kuti ukondweretse anthu ambiri.
3Lev. 19.15 Munthu wosauka ukamuweruza, usaweruze mokondera.
4 Deut. 22.1-4 “Ukaona ng'ombe ya mdani wako ikusokera, kapena bulu wake, utenge ukampatse.
5Bulu wa mdani wako akagwa ndi katundu, usabzole ndi kumsiya, koma umthandize kuti adzuke.
6 Lev. 19.15; Deut. 16.19 “Ngati mmodzi mwa anthu ako osauka aimbidwa mlandu, umuweruze molungama ndithu.
7Ulewe zabodza, zosinjirira. Usaphe munthu wosalakwa ndi wosapalamula, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa.
8Usalandire chiphuphu poti chimadetsa m'maso anthu oweruza, ndipo motero mlandu umaipira anthu osalakwa.
9 Eks. 22.21; Lev. 19.33, 34; Deut. 24.17, 18; 27.19 “Musazunze mlendo. Inu nomwe mukudziŵa m'mene amamvera mlendo, poti paja inunso munali alendo ku Ejipito kuja.
Chaka chachisanu ndi chiŵiri ndiponso tsiku lachisanu ndi chiŵiri10 Lev. 25.1-7 “Muzibzala mbeu zaka zisanu ndi chimodzi m'munda mwanu, ndi kumakolola mbeuzo.
11Koma chaka chachisanu ndi chiŵiri mudzaipumuze mindayo. Anthu osauka a mtundu wanu ndiwo adzadye zomera m'mindamo, ndipo nyama zakuthengo zidzadya zotsala. Muzidzachita chimodzimodzi ndi minda yamphesa ndi yaolivi yomwe.
12 Eks. 20.9-11; 31.15; 34.21; 35.2; Lev. 23.3; Deut. 5.13, 14 “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri musamagwira ntchito, kuti ng'ombe zanu zipume pamodzi ndi abulu anu omwe, kutinso akapolo anu ndi alendo omwe apezenso mphamvu.
13Mumvetse zonse zimene ndakuuzanizi. Musamapemphera kwa milungu ina, ndi maina ake omwe musamaŵatchula.
Masiku atatu aakulu achikondwerero(Eks. 34.18-26; Deut. 16.1-17)14“Muzikhala ndi tsiku lachikondwerero katatu pa chaka, kuti mundilemekeze Ine.
15Eks. 12.14-20; Lev. 23.6-8; Num. 28.17-25 Muzikhala ndi tsiku la chikondwerero cha Buledi Wosatupitsa. Monga ndidakulamulirani, muzidya Buledi Wosatupitsa masiku asanu ndi aŵiri pa mwezi wa Abibu, pa nthaŵi yake, chifukwa mudatuluka ku Ejipito mwezi umenewo. Munthu asadzaonekere pamaso panga ali chimanjamanja.
16Lev. 23.15-21; Num. 28.26-31; Lev. 23.39-43 Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha Masika pokolola mbeu zoyamba zochokera ku zobzala zanu. Muzikhalanso ndi tsiku la chikondwerero cha kututa zokolola zonse pakutha pa chaka, pamene muika m'nkhokwe dzinthu dzanu dzonse.
17Anthu aamuna onse aziwonekera pamaso pa Ine Chauta pa masiku atatu ameneŵa.
18“Mukamapereka magazi a nyama ngati nsembe kwa Ine, musapereke pamodzi ndi buledi wofufumitsa, ndipo mafuta a nyama yopereka pa tsiku langa lachikondwerero asakhale mpaka m'maŵa.
19 Deut. 26.2; Eks. 34.26; Deut. 14.21 “Muzibwera ndi zokolola zoyamba zabwino kwambiri za kumunda kwanu ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu.
“Musamaphika kamwanakanyama mu mkaka wa make.
Malonjezo ndi malangizo20“Ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu, kuti akutchinjirizeni pa njira ndi kukufikitsani ku malo amene ndakukonzerani.
21Mumvere iyeyo, ndipo mumvetse zimene akunena. Musamchite zaupandu, chifukwa sadzakhululukira tchimo lotere. Iye akuchita zimenezi m'dzina langa.
22Koma mukamvera iyeyo ndi kuchita zonse zimene ndinena, Ineyo ndidzadana ndi adani anu, ndipo onse amene atsutsana nanu ndidzalimbana nawo.
23“Mngelo wanga adzapita patsogolo panu, ndipo adzakuloŵetsani m'dziko la Aamori, Ahiti, Aperizi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzaŵaononga onsewo.
24Tsono musagwadire milungu yao kapena kuipembedza. Musamachita nao zimene amachita anthu amenewo. Mukaonongeretu milungu yao, ndiponso mukaphwanye miyala yao yopembedzerapo.
25Muzipembedza Chauta, Mulungu wanu, tsono ndidzakudalitsani pokupatsani chakudya ndi madzi, ndipo ndidzakuchiritsani matenda onse.
26Palibe mkazi amene adzapititse padera m'dziko mwanumo, ndipo wosabala sadzaoneka. Ndidzakupatsani moyo wautali.
27Anthu onse olimbana nanu ndidzaŵachititsa mantha kuti andiwope Ine. Ndidzadzetsa chisokonezo pakati pa anthu amene mukumenyana nawo. Ndipo adani anu onse ndidzaŵathamangitsa liŵiro lamtondowadooka.
28Ndidzapirikitsa Ahivi, Akanani ndi Ahiti, inu musanafike, ndipo adzathaŵa monga ngati ndaŵatumira mavu.
29Sindidzaŵapirikitsa chaka chimodzinchimodzi, kuti dzikolo lingadzakhale lopanda anthu ndi kukusiyirani nyama zakuthengo zokhazokha.
30Koma ndidzaŵapirikitsa pang'onopang'ono, mpaka mutabala ana ambiri amene angathe kutenga dzikolo,
31kuyambira ku Nyanja Yofiira mpaka ku Nyanja Yaikulu ya Afilisti, ndi kuyambiranso ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Ndidzakupatsani mphamvu zopambanira anthu a m'dzikolo, ndipo mudzaŵapirikitsa.
32Musadzachite nawo chipangano iwowo kapenanso milungu yao.
33Asadzakhale m'dziko mwanu, kuwopa kuti angadzakuchimwitseni. Mukamapembedza milungu yao, ndithu mudzakodwa mu msampha.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.