Ezek. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kusakhulupirika kwa Yerusalemu

1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2“Iwe mwana wa munthu, umuwonetse Yerusalemu makhalidwe ake onyansa.

3Umuuze kuti, Ambuye Chauta akukuuza kuti, ‘Kanani ndi dziko la makolo ako, ndipo udabadwira kumeneko. Atate ako anali Mwamori, amai ako anali Muhiti.

4Ndipo utabadwa adakuchita izi: sadadule ntchofu yako, sadakusambitse m'madzi kuti akuyeretse. Sadakuthire mchere monga kudayenera, ndipo sadakukulunge m'nsalu.

5Palibe ndi mmodzi yemwe amene adakusamala kapena kukumvera chisoni chokwanira kuti akuchitire zimenezi. Koma adakutaya panja poyera, chifukwa adaanyansidwa nawe pa tsiku limene udabadwa.

6“ ‘Ndiye Ine nditabwera, ndidakuwona ukuvimvinizika m'magazi ako. Ndidalankhula nawe uli m'magazi momwemo ndi kukuuza kuti, “Ukhale ndi moyo,

7ndipo ukule ngati mbeu ya m'munda.” Udakuladi, ndipo udatalika nkutha msinkhu. Maŵere adayamba kumera, tsitsi lako lidayamba kutalika. Komabe unali wamaliseche ndi wausiŵa.

8“ ‘Nditabweranso, ndidaona kuti nthaŵi yako yomanga banja idakwana. Tsono ndidakufunditsa mwinjiro wanga ndi kubisa maliseche ako. Ndidachita nawe chipangano chaukwati, ndipo udasanduka wanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

9“ ‘Tsono ndidakusambitsa m'madzi ndi kukutsuka magazi ako, ndipo ndidakudzoza mafuta.

10Ndidakuveka zovala zopetapeta ndi nsapato zachikopa. Ndidakupatsa nsalu zabafuta ndi kukuveka zovala zasilika.

11Ndidakukongoletsa ndi zamakaka, nkukuveka zigwinjiri m'manja, ndi mkanda m'khosi mwako.

12Ndidakuveka chipini pa mphuno. Ndidakuika nsapule ku makutu ndi chisoti chaufumu chokongola kumutu kwako.

13Motero udavaladi zokongoletsa zagolide ndi zasiliva. Zovala zako zinali za bafuta wosalala, zasilika ndi za nsalu zopetapeta. Unkadya ufa wosalala, uchi ndi mafuta a olivi. Udakula mokongola zedi, ndipo udasanduka mfumukazi.

14Mbiri ya kukongola kwako idawanda pa dziko lonse lapansi, chifukwa choti ulemerero umene ndidakuveka nawo udakukongoletsa kwambiri. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

15“ ‘Koma udadzitama nako kukongola kwako ndi kutchuka kwako, ndipo udayamba kuchita zadama. Unkachita chigololo, kumangodzipereka kwa aliyense amene wabwera.

16Udatengako zovala zako zina nukakongoletsera akachisi akoako, ndipo kumeneko unkakachitirako zigololo. Zotere sizinachitikepo, ndipo sizidzachitikanso.

17Udatenganso zokongoletsera, zopangidwa ndi golide wanga ndi siliva wanga, zimene ndidakupatsa, ndipo udapangira mafano achimuna amene udachita nawo chigololo.

18Mafanowo udaŵaveka zovala zako zopetapeta, ndipo udapereka mafuta anga ndi lubani wanga kwa iwo.

19Udatenga chakudya chimene ndidakupatsa, ufa, mafuta ndi uchi zimene ndinkakudyetsa, nuzipereka kwa iwo ngati nsembe za fungo lokoma. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

20“ ‘Udatenga ana ako aamuna ndi aakazi amene udabalira Ine, nukaŵapereka ngati nsembe kwa mafano. Kodi zigololo zakozo sizidakukwanire,

21apa ukupha ana anga ndi kuŵapereka kwa mafano ako?

22Chifukwa cha zigololo zako zonyansazo, udaiŵala masiku a ubwana wako, pamene unali wamaliseche, wausiŵa ndi womangovimvinizika m'magazi ako.’ ”

Moyo wa Yerusalemu ndi wadama

23Ambuye Chauta akuti, “Uli ndi tsoka, ndithu uli ndi tsoka, chifukwa kuwonjezera pa zoipa zako zonsezo,

24udadzimangira nsanja pamodzi ndi guwa lake pa bwalo lililonse.

25Udamanga nsanja zakozo pa mseu uliwonse. Pamenepo udanyazitsa kukongola kwako, podzipereka kwa aliyense wodutsapo. Wakhala ukuchita zigololo kosaŵerengeka.

26Udachita zigololo ndi Aejipito adama oyandikana nawe, ndipo udandikwiyitsa chifukwa udachulukitsa zigololo zako.

27Ndidakukantha ndi dzanja langa ndipo ndidakuchepetserako dziko lako. Ndidakupereka kwa adani ako, Afilisti, amene ankaipidwa ndi makhalidwe ako onyansa.

28Chifukwa cha zilakolako zako udachitanso chigololo ndi Aasiriya.

29Pambuyo pake udapitirira kuchita chigololo ndi Ababiloni, anthu a m'dziko lokonda lamalonda. Komabe sudakhutire nazo.”

30Ambuye Chauta akunena kuti, “Mtima wako ndi wofooka kwambiri chifukwa udachita zonsezo monga ngati mkazi wadama wopanda manyazi.

31Udamanga nsanja ndi guwa lake pa mseu uliwonse ndiponso kachisi pa bwalo lililonse. Koma iweyo sunkachita monga amachitira adama ena, chifukwa sunkachitira malipiro.

32Mkazi wadama iwe, unkakonda amuna achilendo kupambana mwamuna wako.

33Amuna amapereka ndalama kwa akazi onse adama. Koma iwe zibwenzi zako zonse unkazipatsa mphatso. Potero unkazinyengerera kuti zizibwera kuchokera mbali zonse kudzagona nawe.

34Choncho udaali wosiyana ndi akazi ena pochita zadama, chifukwa panalibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye amene unkapereka ndalama, osati ena kukupatsa ndalama ai. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.”

Mulungu adzalanga Yerusalemu

35“Tsono mkazi wadama iwe, imva mau a Chauta.

36Ambuye Chautawo mau ao ndi aŵa, Udavula mopanda manyazi, udaonetsa maliseche ako pochita zadama ndi zibwenzi zako ndi mafano ako, ndipo udapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zopereka kwa mafanowo.

37Nchifukwa chake ndidzasonkhanitsa abwenzi ako amene unkasangalala nawo, ndiponso onse amene unkaŵakonda pamodzi ndi onse amene unkadana nawo. Ndidzaŵasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse, nkukuvula pamaso pao, kuti iwowo adzaone thupi lako lonse lamaliseche.

38Ndidzakulanga monga amalangira akazi achigololo ndiponso opha anthu. Chifukwa cha nsanje yanga ndidzakhetsa magazi ako mokwiya kwambiri.

39Ndidzakupereka m'manja mwa abwenzi ako. Adzaononga nsanja zako ndi maguwa ako ndi kugwetsa akachisi ako aja. Adzakuvula zovala zako ndi kukukolopola zodzikongoletsera zako zabwinozo. Motero adzakusiya wamaliseche ndi wausiŵa.

40Adzatuma gulu la anthu kuti akuponye miyala ndi kukudula pafupipafupi ndi malupanga ao.

41Adzatentha nyumba zako, ndipo adzakulanga poyera, akazi ambiri akuwona. Ndidzathetsa dama lako, ndipo sudzazilipiranso zibwenzi zako.

42Pamenepo ndidzaleka, ukali wanga udzatha, ndipo sindidzakuchitiranso nsanje. Ndidzakhala phee, osachitanso ukali.

43Iwe udaiŵala masiku a ubwana wako, ndipo udandikwiyitsa ndi zinthu zonse zimene udachita. Nchifukwa chake Ine ndidzakubwezera pamutu pako chilango cha zimene udachitazo. Pajatu udaonjezera zigololo pa zonyansa zako zina zonse. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Mwana amatengera make

44“Iwe Yerusalemu, akuluakulu adzakuphera mwambi uwu wakuti, ‘Mwana watengera cha make.’

45Ndiwedi mwana wa mai wako amene adadana ndi mwamuna wake ndi ana ake. Ndiwe mbale wa abale ako amene adadana ndi amuna ao ndiponso ana ao. Mai wako anali Muhiti, bambo wako anali Mwamori.

46Mkulu wako ndi Samariya amene ankakhala cha kumpoto kwako pamodzi ndi midzi yake. Mng'ono wako amene ankakhala ndi midzi yake chakumwera kwako, ndi Sodomu.

47Iwe sudakhutire nkutsata njira zao zoipa ndiponso kuchita zonyansa. Koma patangopita nthaŵi pang'ono chabe, unkachita zoipa kupambana iwowo.

48Pali Ine ndemwe Chauta wamoyo, ngakhale mbale wako Sodomu ndi midzi yake sadachite monga m'mene iweyo wachitira pamodzi ndi midzi yako. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.

49Tchimo la mbale wako Sodomu linali lakuti iyeyo pamodzi ndi midzi yake ankanyadira chuma chake ndi chakudya chake chambiri, koma osalabadako zothandiza osauka ndi aumphaŵi.

50Ankadzitukumula kwambiri namachita zonyansa zambiri pamaso panga. Nchifukwa chake ndidaŵachotsa monga m'mene waoneramu.

51Ngakhale Samariya yemwe sadachite theka la machimo amene udachita iwe. Iweyo udachita zonyansa zambiri kupambana abale ako aŵiriwo, kotero kuti iwo amaoneka ngati osachimwa poyerekeza ndi iwe.

52Tsopano mwiniwakewe uyenera kuchita manyazi ndi kunyozedwa, iwe amene waonetsa abale ako ngati osachimwa. Machimo ako ndi onyansa kwambiri kupitirira a abale ako, motero iwo aoneka ngati osalakwa. Iwenso tsono, amene udaonetsa abale ako ngati osachimwa, uchite manyazi ndi kunyozedwa.

Sodomu ndi Samariya adzadalitsidwanso

53“Koma ndidzadalitsanso Sodomu pamodzi ndi midzi yake. Ndidzachita chimodzimodzi ndi Samariya pamodzi ndi midzi yake. Pa nthaŵi yomweyo, nawenso Yerusalemu ndidzakudalitsa.

54Choncho uchite manyazi ndi kunyozedwa, chifukwa udaonetsa abale akoŵa ngati angwiro.

55Koma pamene mbale wako Sodomu pamodzi ndi midzi yake adzakhalanso monga momwe adaaliri kale, ndipo pamene mbale wako Samariya pamodzi ndi midzi yake adzakhalanso monga momwe adaaliri kale, nawenso ndi midzi yako udzakhalanso monga momwe udaaliri kale.

56Kodi kale lija pamene iwe unkanyada, paja unkakonda kujeda mbale wako Sodomu,

57kuipa kwako kusanadziŵike. Koma tsopano walingana naye posanduka chinthu chonyozeka kwa anthu a ku Edomu ndi kwa onse oyandikana nawo, ndiponso kwa Afilisti. Ndithu okuzungulira onsewo akukunyoza kwambiri.

58Motero iwe uyenera kulangidwa chifukwa cha zigololo zako ndi makhalidwe ako onyansa. Ndikutero Ine Chauta.

Chipangano chosatha

59“Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Ndidzakulanga potsata zimene udachita. Iwe udanyoza lumbiro lako pakuphwanya chipangano.

60Komabe ndidzakumbukira chipangano chimene ndidachita nawe pa ubwana wako. Ndidzachita nawe chipangano china, chipangano chake chosatha.

61Tsono udzakumbukira makhalidwe ako akale. Udzachita manyazi pamene udzalandiranso abale ako, wamkulu ndi wamng'ono yemwe. Ndidzaŵapereka kwa iwe kuti akhale ngati ana ako aakazi, ngakhale kuti iwowo sali nao m'chipangano changa ndi iwe.

62Ndidzachita chipangano changa ndi iwe, ndipo udzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.

63Ndikadzakukhululukira zoipa zako zonse zimene udachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzathanso nkulankhula komwe. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help