Zef. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yerusalemu ali pa tsoka

1Tsoka kwa Yerusalemu,

mzinda wopanduka, wonyansa ndi wankhanza.

2Sudamvere mau ouchenjeza.

Sudasamale mau oudzudzula.

Sudakhulupirire Chauta

kapena kuyandikira kwa Mulungu wake.

3Nduna zake zinkakhuluma m'kati mwake,

ngati mikango yobangula.

Oweruza ake anali ngati mimbulu yoyenda madzulo,

yosasiyako ndi fupa lomwe kuti lifike mpaka m'maŵa.

4Aneneri ake anali achabechabe,

anthu osakhulupirika.

5Koma Chauta ndi wolungama mumzindamo,

Iyeyo salakwa.

Amaweruza molungama tsiku ndi tsiku,

nthaŵi zonse salephera,

koma osalungama akuchitabe zoipa opanda manyazi.

6Chauta akuti,

“Ndaononga mitundu yonse ya anthu

ndipo malinga ao onse ankhondo ndaŵaphwasula.

Miseu yao ndaifafaniza

palibenso anthu oyendamo.

Mizinda yao yachitika bwinja,

mulibe munthu ndi mmodzi yemwe wotsalamo.

7Ndidaaganiza kuti ndithudi anthu anga andiwopa,

kuti avomera malango anga,

ndipo kuti saiŵala malamulo anga.

Koma ndi pamene iwo adanyanyira

kumachita zoipa pa zochita zao zonse.”

8Chauta akunena kuti,

“Nchifukwa chake mundidikire,

mudikire tsiku limene ndidzakuimbeni mlandu.

Pakuti ndatsimikiza zosonkhanitsa mitundu

ya anthu pamodzi ndi maufumu onse,

kuti ndiŵaonetse kusakondwa kwanga

amve ululu wa ukali wanga.

Dziko lonse lapansi lidzapserera

ndi moto waukali wa mkwiyo wanga.”

9“Pamenepo ndidzasintha malankhulidwe

a mitundu yonse,

nkuŵapatsa malankhulidwe abwino,

kuti onse azitama dzina la Chauta mopemba

ndi kumamtumikira mogwirizana.

10Ngakhale kutali kutsidya kwa mitsinje

ya ku Etiopiya,

anthu ondipembedza, anthu anga obalalika,

adzapereka nsembe kwa Ine.”

Otsala osungidwa

11“Tsiku limenelo inu a ku Yerusalemu

simudzachitanso manyazi,

chifukwa cha zoipa zonse zimene mudandichita,

zimene mudandipandukira nazo.

Pakuti nthaŵi imeneyo ndidzakuchotserani

onse odzikuza ndi onyada.

Simudzachitanso zonyada zanuzo

pa phiri langa loyera.

12Pakati panu ndidzasiya anthu

odzichepetsa ndi otsika.

Iwowo adzafunafuna populumukira m'dzina la Chauta.

13 Chiv. 14.5 Otsala a mu Israeleŵa sadzalakwanso,

sadzalankhulanso zabodza,

sadzachitanso zonyenga,

Adzakhala pabwino mwamtendere,

popanda wina woŵaopsa.”

Nyimbo yachisangalalo

14Imbani mokweza, inu anthu a ku Ziyoni!

Fuulani inu Aisraele!

Sangalalani, kondwani ndi mtima wonse,

inu okhala mu Yerusalemu.

15Chauta wachotsa chilango chanu.

Wapirikitsa adani anu.

Chauta, Mfumu ya Israele, ali nanu pamodzi.

Simudzaopanso choipa chilichonse.

16Tsiku limenelo adzauza Yerusalemu kuti,

“Usaope, iwe Ziyoni,

usataye mtima.

17Chauta, Mulungu wako, ali nawe pamodzi,

ngati wankhondo wokuthandiza kugonjetsa adani.

Adzasangalala ndi chimwemwe chifukwa cha iwe.

Adzakubwezera m'chikondi chake.

Adzakondwera nawe poimba nyimbo zachimwemwe.

18Monga pa masiku achikondwerero,

ndidzakuchotsera tsoka,

limene lingokuvutitsa ndi kukunyozetsa.

19Nthaŵi imeneyo ndidzaŵakhaulitsa

onse amene amakuzunzani.

Ndidzapulumutsa otayika

ndi kusonkhanitsa onse obalalika.

Ndidzaŵatamanda ndi kuŵapatsa ulemu,

kulikonse kumene adani ao ankaŵachititsa manyazi.

20Nthaŵi imeneyo ndidzakusonkhanitsani,

Ndidzakubwezerani kwanu.

Ndidzakusandutsani otchuka ndi olemekezeka,

pakati pa anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi.

Ndidzakubwezerani ufulu wanu inu mukupenya.

Ndatero Ine Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help