1Pamenepo mpingo wonse udafuula kwambiri, ndipo anthu adalira usiku umenewo.
2Aisraele onse adayamba kuŵiringulira Mose ndi Aroni. Mpingo wonse udaŵauza kuti, “Kukadakhala bwino tikadangofera ku Ejipito, kapena m'chipululu mommuno.
3Chifukwa chiyani Chauta akutiloŵetsa m'dziko limenelo kuti tikaphedwe pa nkhondo? Akazi athu adzatengedwa ku ukapolo pamodzi ndi ana athu. Kodi sikukadakhala bwino koposa kuti tibwerere ku Ejipito?”
4Ndipo adayamba kuuzana kuti, “Tiyeni tisankhe mtsogoleri kuti tibwerere ku Ejipito.”
5Mose ndi Aroni adadziponya pansi pamaso pa mpingo wonse wa Aisraele.
6Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, amene adaali m'gulu la anthu okazonda dziko lija, adang'amba zovala zao.
7Ndipo adauza mpingo wonse wa Aisraele uja kuti, “Dziko limene tidakalizondalo ndi labwino kwambiri.
8Ngati Chauta amatikonda, adzatiloŵetsa m'dziko lamwanaalirenjilo ndi kutipatsa kuti likhale lathu.
9Ahe. 3.16 Koma musagalukire Chauta. Musaope anthu a m'dzikolo chifukwa tidzaŵaononga. Iwowo alibe oŵatchinjiriza, koma ife Chauta ali nafe, musaŵaope.”
10Koma mpingo wonse udaati uŵaponye miyala.
Pomwepo ulemerero wa Chauta udaonekera Aisraele onse m'chihema chamsonkhano.
Mose apempherera Aisraele11Chauta adafunsa Mose kuti, “Kodi anthu ameneŵa adzaleka liti kundinyoza? Ndipo adzaleka liti kusandikhulupirira, ngakhale aone zizindikiro zimene ndachita pakati pao?
12Ndidzaŵapha ndi mliri ndi kuŵalanda choloŵa chao, ndipo iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kupambana iwoŵa.”
13 Eks. 32.11-14 Koma Mose adayankha Chauta kuti, “Zimenezitu Aejipito adzazimva, pakuti ndinu amene mudaŵatulutsa anthu ameneŵa m'dziko la Ejipito.
14Tsono Aejipito azidzasimbira anthu a m'dziko muno. Iwo amva kale kuti Inu Chauta muli pakati pa anthu ameneŵa. Inu Chauta mumaŵaonekera maso ndi maso, ndipo mtambo wanu umaŵaphimba. Masana mumaŵatsogolera ndi mtambo, usiku mumaŵatsogolera ndi moto.
15Tsopano mukaŵapha onse anthu ameneŵa, mitundu ina imene yamva mbiri yanu idzati,
16‘Chauta waŵaphera m'chipululu anthuŵa, chifukwa choti sadathe kuŵaloŵetsa m'dziko limene adalumbira kuti adzaŵapatsa kuti likhale lao.’
17Tsono ndikukupemphani, Chauta muwonetse kuti mphamvu zanu nzazikulu monga mudalonjezera kuti,
18Eks. 20.5, 6; 34.6, 7; Deut. 5.9, 10; 7.9, 10 ‘Chauta ndi wosakwiya msanga, ndi wodzaza ndi chifundo chosasinthika, ndi wokhululukira ochimwa ndi opalamula. Koma sadzaleka kulanga ochimwa, amalanga ana a mbadwo wachitatu ndi wachinai chifukwa cha kuchimwa kwa makolo ao.’
19Ndikukupemphani kuti muŵakhululukire kuchimwa kwao anthu ameneŵa kaamba ka chifundo chanu chachikulu ndi chosasinthika, ndiponso chifukwa mwakhala mukuŵakhululukira anthu ameneŵa kuyambira ku Ejipito mpaka tsopano lino.”
20Chauta adati, “Ndaŵakhululukira chifukwa cha mau ako.
21Ahe. 3.18 Koma ndikulumbira kuti pali Ine ndemwe ndiponso malinga nkuti dziko lonse lapansi ndi lodzaza ndi ulemerero wa Chauta,
22Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaloŵe m'dzikolo. Anthu ameneŵa adaona ulemerero wanga ndi zizindikiro zanga zimene ndidachita ku Ejipito ndi m'chipululu muno, komabe adandipenekera kakhumi konse osamvera mau anga.
23Palibe amene adzaone dziko limene ndidalonjeza makolo ao molumbira kuti ndidzaŵapatsa. Mwa amene adandikana palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaliwone dzikolo.
24Yos. 14.9-12 Koma Kalebe mtumiki wanga, chifukwa ali ndi mtima wosiyana ndi ena, ndipo wanditsata ndi mtima wonse, ndidzamloŵetsa m'dziko limene adapitamolo, ndipo zidzukulu zake zidzalandira dzikolo kuti likhale lao.
25Tsono popeza kuti Aamaleke ndi Akanani amakhala m'zigwa, maŵa mubwerere, muyambepo ulendo wopita ku chipululu, mudzere ku Nyanja Yofiira.”
Chauta alanga anthu chifukwa cha kuŵiringula kwao26Chauta adafunsa Mose ndi Aroni kuti,
27“Kodi anthu oipa chotereŵa, adzaleka liti kundiŵiringulira? Ndamva maŵiringulo ao amene akundichitira.
28Uŵauze kuti, Chauta akunena kuti, ‘Zimene mwanena, Ine ndamva, ndipo ndi zimene ndidzakuchitani.
29Ahe. 3.17 Mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu muno. Anthu onse, kuyambira a zaka makumi aŵiri ndi opitirirapo, amene adandiŵiringulira,
30palibe ndi mmodzi yemwe amene adzaloŵe m'dziko limene ndidalumbira kuti mudzaloŵamo, kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.
31Ana anu amene munkati adzagwidwa mu ukapolo, ndidzaŵaloŵetsa m'dzikomo, ndipo adzalidziŵa dziko limene inu mukunyozalo.
32Koma enanu, mitembo yanu idzakhala ili mbwee m'chipululu mommuno.
33Ntc. 7.36 Ana anu adzakhala abusa m'chipululu akungoyendayenda zaka makumi anai, ndipo adzasauka chifukwa cha kusakhulupirika kwanu, mpaka inuyo mutatha ndi kufa m'chipululu.
34Padzapita zaka makumi anai mukulangidwa chifukwa cha zolakwa zanu, kuŵerenga chaka chimodzi pa tsiku lililonse la masiku makumi anai aja amene munkazonda dziko. Mudzadziŵa kuwopsa kwake kwa kukangana ndi Ine.’
35Ine Chauta ndanena. Ndithudi, ndidzachitadi zimenezi kwa anthu onse oipaŵa, amene agwirizana kuti andiwukire. M'chipululu mommuno ndimo m'mene athere, ndipo afera mommuno.”
36Anthu amene Mose adaŵatuma kuti akazonde dziko aja atabwerako, ena adayamba kuutsa mitima ya anthu kuti aukire Mose pakuŵauza zoipa za dzikolo.
37Anthu onsewo amene ankasimba zoipa za dzikolo, adafa ndi mliri pamaso pa Chauta.
38Koma mwa anthu amene adapita kukazonda dziko aja, Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune ndiwo adatsala amoyo.
39Mose adaŵafotokozera Aisraele mau onseŵa, ndipo anthu adalira kwambiri.
40Adalaŵirira m'mamaŵa, ndipo adakwera cha ku dziko lamapiri, nati “Ife pano takonzeka kukwera mpaka kukafika ku malo amene Chauta adatilonjeza. Ndithu tachimwadi.”
41Koma Mose adati, “Chifukwa chiyani mukunyoza lamulo la Chauta, poti zimenezo sizidzatheka?
42Musapite, kuti mungaphedwe pamaso pa adani anu, pakuti Chauta sali nanu.
43Kumeneko Aamaleke ndi Akanani ali m'tsogolo mwanu, ndipo mudzaphedwa pa khondo. Chauta sadzakhala nanu, chifukwa choti mwaleka kumtsata.”
44Koma iwo adapitabe osasamala, nakwera ku dziko lamapiri, ngakhale kuti sadatsakane ndi Bokosi lachipangano cha Chauta, kapena ndi Mose, pochoka pamahemapo.
45Tsono Aamaleke ndi Akanani, amene ankakhala m'dziko lamapirilo, adatsika ndipo adaŵagonjetsa, ndi kuŵapirikitsa mpaka ku Horoma.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.