1“Iwe mwana wa munthu, tenga lupanga lakuthwa ngati lumo la wometa, umete tsitsi ndi ndevu. Tsono utenge choyesera, ugaŵe tsitsilo patatu.
2Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiŵiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda mozungulira mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga.
3Utengeko tsitsi pang'ono, ulimange mu mpendero wa mkanjo wako.
4Pa tsitsi limeneli utapepo lina, uliponye pa moto, nkulitentha. Moto wa tsitsilo udzayaka mpaka kutentha Israele yense.”
5“Zimene akunena Ambuye Chauta ndi izi, akuti, ‘Uyu ndi Yerusalemu. Ndamuika pakati pa dziko lapansi, ndipo maiko onse akumzungulira.
6Koma anthu a ku Yerusalemu adapandukira malamulo anga, kupambana anthu a mitundu ina. Adakhala osamvera kupambana anthu a m'maiko ozungulira. Adakanadi malamulo anga ndipo sadasunge malangizo anga.’
7Nchifukwa chake zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Chipongwe chanu nchachikulu kupambana cha anthu a mitundu yokuzungulirani. Simudatsate malamulo anga, simudasunge malangizo anga, koma mudatsata malamulo a anthu a mitundu yokuzungulirani.
8Nchifukwa chake Inenso ndakukanani. Ndidzakulangani anthu a mitundu ina akuwona.
9Ndidzakulangani ndi chilango chimene sindidakulange nachoni nkale lonse, ndipo sindidzakulanga nachoninso nkutsogolo komwe, poti zolakwa zanu nzonyansa kwambiri.
10Mali. 4.10Tsono mwa inu makolo adzadya ana ao ndipo ana adzadya makolo ao. Ndidzakulanganidi, ndipo onse otsala pakati pa inu, ndidzaŵamwazira ku mphepo zonse zinai.”
11“Pali Ine ndemwe Mulungu wamoyo, ndidzakuwonongani mopanda chifundo, chifukwa choti mwaipitsa Nyumba yanga ndi mafano anu oipa ndi miyambo yanu yonyansa. Tsono Ine sindidzakulekererani, sindidzakuchitirani chisoni mpang'ono pomwe.
12Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu anu chidzafa ndi mliri, kapena chidzaonongeka ndi njala. Chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda. Ndipo chigawo china ndidzachimwazira ku mphepo zonse zinai, pochita kuchipirikitsa ndi lupanga langa losolola.”
13“Ndimo m'mene udzachitire mkwiyo wanga, ndipo ndidzaŵakalipira mpaka mtima wanga utakhala pansi. Choncho adzadziŵa kuti Ine Chauta ndidalankhula mwansanje pokulangani monga m'mene ndachitiramu.”
14“Iwe Yerusalemu, ndidzakusandutsa bwinja. Udzakhala chinthu chonyozeka m'maso mwa anthu a mitundu yokuzungulira ndi kwa onse odutsapo.
15Udzakhala chinthu chonyozeka, ndipo adzakunyodola. Udzakhala ngati chenjezo ndi chinthu choopsa kwa mitundu ya anthu okuzungulira, pamene ndidzakulanga mwamphamvu ndi kugamula mlandu wako mokwiya ndi mwaukali. Ndatero Ine Chauta.
16Ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza, kuti ndikuwononge. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku.
17Chiv. 6.8Ndidzatumiza njala ndi zilombo zakuthengo ndipo zidzakulanda ana ako. Ndidzakugwetsa ndi mliri ndipo padzakhala kuphana pakati pa anthu ako. Ndidzakudzetsera nkhondo yokuwononga. Ndatero Ine Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.