Mik. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 2Maf. 15.32-38; 2Mbi. 27.1-7; 2Maf. 16.1-20; 2Mbi. 28.1-27; 2Maf. 18.1—20.21; 2Mbi. 29.1—32.33 Pa nthaŵi ya ufumu wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda, Chauta adampatsa mthenga Mika wa ku Moreseti. Nazi zimene iyeyu adaona m'masomphenya zokhudza Samariya ndi Yerusalemu.

Samariya ndi Yerusalemu adzudzulidwa

2Imvani nonsenu anthu a mitundu yonse.

Tchera khutu iwe dziko lapansi

ndi zonse zokhala m'menemo.

Ambuye Chauta akuimbani mlandu,

akulankhulira ku Nyumba yao yoyera.

3Taonani, Chauta akubwera kuchokera ku malo ake.

Akutsika pansi ndipo akuyenda pa nsonga za mapiri.

4Mapiriwo akusungunuka ngati phula pa moto.

Akuyenderera m'zigwa ngati madzi ochokera m'phiri.

5Zonsezi zikuchitika chifukwa cha zoipa

za zidzukulu za Yakobe,

chifukwa cha machimo a banja la Israele.

Ndani adachimwitsa Aisraele?

Si a ku Samariya kodi?

Ndani adalakwitsa Ayuda?

Si a ku Yerusalemu kodi?

6Tsono Chauta akuti,

“Samariyayo ndidzamsandutsa bwinja,

malo olimamo munda wamphesa.

Miyala yake ndidzaitaya ku zigwa,

ndipo maziko ake ndidzaŵafukula.

7Mafano ake onse ndidzaŵaphwanyaphwanya,

ndipo mitulo yake yonse idzatenthedwa m'moto.

Zithunzi zonse za milungu yake ndidzaziwononga.

Mphatso zake adazilandira

kuchokera ku malipiro a akazi adama,

choncho enanso adzazigwiritsa ntchito

ngati malipiro a akazi adama.”

8Tsono Mika adati,

“Nchifukwa chake ndidzalira komvetsa chisoni.

Ndidzayenda maliseche,

ndidzakuwa ngati nkhandwe

ndi kulira ngati nthiŵatiŵa.

9Samariya, zilonda za uchimo wake sizingathe kupola,

zafika mpaka ku Yuda.

Chiwonongeko chili pafupi ndi mzinda wa anthu anga,

chafika mpaka ku Yerusalemu kwenikweni.”

Adani ayandikira ku Yerusalemu

10Musaŵauze zimenezi a ku Gati,

musalire konse.

Muvimvinizike m'fumbi ku Beteleafura,

kuwonetsa chisoni.

11Inu anthu a ku Safiri mudzapita ku ukapolo

muli maliseche ndi amanyazi.

Anthu a ku Zanani satuluka mu mzinda wao.

Mukamva anthu a ku Betezele akulira,

mudzadziŵa kuti sangathe kukuthandizani.

12Anthu a ku Maroti ali ndi nkhaŵa

poyembekeza thandizo,

chifukwa Chauta wadzetsa chiwonongeko

pafupi ndi Yerusalemu.

13Mangani akavalo ku magaleta,

inu anthu a ku Lakisi.

Mudatsanzira machimo a Israele,

potero mudachimwitsa anthu a ku Ziyoni.

14Tsono a ku Moreseti-Gati mutsazikane nawo.

Anthu a ku Akizibu adzanamiza mafumu a ku Israele.

15Inunso anthu a ku Maresa, ndidzakutumirani

adani kuti akugonjetseni.

Akuluakulu a ku Israele adzabisala

m'thanthwe la Adulamu.

16Inu a ku Yuda, metani mpala,

kuwonetsa kuti mukulira ana anu amene munkaŵakonda.

Mukhale ndi dazi la dembo

poti anawo adakusiyani,

adatengedwa ku ukapolo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help