Yow. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Nawu uthenga umene Chauta adapatsa Yowele,

mwana wa Petuwele:

Anthu alira chifukwa cha dzombe loononga minda

2Inu akuluakulu, mverani.

Tcherani khutu, inu nonse okhala m'dziko.

Kodi zoterezi zidaonekapo nthaŵi yanu

kapena nthaŵi ya makolo anu?

3Muŵauze ana anu,

iwowo auze ana ao,

ndipo anawo aziwuzanso ana ao.

4Chimene chiwala chidasiya, dzombe lidadya.

Chimene dzombe lidasiya, mandowa adadya,

chimene mandowa adasiya, chilimamine adadya.

5Dzukani inu zidakwa, ndipo mulire.

Mulire modandaula inu nonse okonda vinyo:

mphesa zotchezera vinyo watsopano zaonongedwa,

6 Chiv. 9.8 Chikhamu cha dzombe chagwa m'dziko lathu

nchamphamvu ndiponso chosaŵerengeka.

Mano ake ali ngati a mkango wamphongo,

zibwano zake ngati za mkango waukazi.

7Aononga mpesa wanga,

athyolathyola mitengo yanga ya mikuyu.

Aisadza, aikungunula makungwa, naŵataya,

nthambi zake nkumazisiya zili mbee.

8Inu anthu, lirani kwambiri

ngati namwali wovala chiguduli.

Wolira chifukwa cha imfa ya mnyamata

wofuna kumkwatira.

9Chopereka cha chakumwa ndi cha chakudya

siziperekedwanso ku Nyumba ya Chauta.

Ansembe akulira,

atumiki a Chauta aja.

10Minda yaguga, nthaka ikulira

poti tirigu waonongeka,

mphesa zaumiratu,

mitengo ya mafuta yauma.

11Tayani mtima, inu alimi,

lirani, inu olima mphesa,

chifukwa tirigu ndi barele,

ndi zonse zam'minda zalephera.

Mulungu aitana anthu kuti atembenuke mtima

12Mpesa wauma, mkuyu wafota.

Mkangaza, kanjedza,

mitengo ya apulosi ndi mitengo yonse ya m'dziko

yaumiratu.

Choncho chikondwerero cha anthu chatheratu.

13Inu ansembe, valani ziguduli

mudzigunde pa chifuwa chifukwa cha chisoni.

Lirani, inu otumikira ku guwa.

Tiyeni, mufunde ziguduli usiku wonse,

inu atumiki a Mulungu wanga.

Pakuti chopereka cha chakudya ndi chakumwa

sizidzaonekanso ku Nyumba ya Mulungu wanu.

14Lamulani kuti anthu asale zakudya.

Itanitsani msonkhano waulemu.

Akulu ndi onse okhala m'dziko

asonkhane ku Nyumba ya Chauta, Mulungu wanu,

ndipo iwowo alire kwa Iye.

15 Yes. 13.6 Kalanga ine! Tsiku loopsa layandikira,

tsiku la Chauta, likubwera ndi chiwonongeko

chochokera kwa Mphambe.

16Chakudya chathu chikutha ife tikuwona.

Mulibenso chimwemwe ndi chisangalalo

m'Nyumba ya Mulungu wathu.

17Mbeu zakongonyala, poti pansi mpouma.

Nyumba zosungiramo dzinthu zaonongeka,

nkhokwe zapasuka, popeza kuti zokolola palibe.

18Zoŵeta zikulira ndi njala.

Ng'ombe zikungoyenda uku ndi uku

chifukwa choti zilibe busa.

Nazonso nkhosa zikusauka.

19Ndikulira kwa Inu Chauta,

pakuti moto wapsereza mabusa akuthengo,

ndipo malaŵi a moto apsereza mitengo

yonse yam'tchire.

20Nazonso nyama zakuthengo zikulira kwa Inu,

chifukwa timitsinje tonse taphwa,

ndipo moto wapsereza mabusa akuthengo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help