2 Mbi. 22 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ahaziya mfumu ya ku Yuda(2 Maf. 8.25-29; 9.21-28)

1Anthu okhala mu Yerusalemu adalonga ufumu Ahaziya, mzime wa Yehoramu uja, m'malo mwa bambo wakeyo, pakuti gulu lankhondo limene lidadza pamodzi ndi Arabu kuzithandoko, linali litapha ana onse akuluakulu aamuna. Motero Ahaziya, mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda, ndiye amene adaloŵa ufumu.

2Ahaziyayo anali wa zaka 42 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira chaka chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Ataliya, mdzukulu wake wa Omuri.

3Iyeyonso ankatsata chitsanzo cha banja la Ahabu, poti mai wake ndiye ankamupatsa uphungu woipa.

4Adachita zoipa pamaso pa Chauta, monga momwe linkachitira banja la Ahabu. Pakuti atafa bambo wake uja, anthuwo ndiwo amene ankamupatsa uphungu pa ntchito zake zoipa.

5Iyeyo adatsatanso uphungu wao, ndipo adapita pamodzi ndi Yoramu, mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israele, kuti akamenyane nkhondo ndi Hazaele, mfumu ya ku Siriya, ku Ramoti ku Giliyadi. Kumeneko Asiriya adamlasa Yoramu.

6Tsono iye adabwerera napita ku Yezireele kuti akamchiritse mabala amene adaamlasa ku Rama, pamene ankamenyana ndi Hazaele mfumu ya ku Siriya. Motero Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda adapita ku Yezireele kukazonda Yoramu, mwana wa Ahabu, chifukwa chakuti ankadwala.

7Koma Mulungu adazikonzeratu kuti Ahaziya aonongedwe pokacheza kwa Yoramuyo. Atafika kumeneko, adapita pamodzi ndi Yoramu kuti akakumane ndi Yehu, mwana wa Nimisi, amene Chauta adaamsankha kuti aononge banja la Ahabu.

8Pamene Yehu ankalanga banja la Ahabu lija, adakumana ndi atsogoleri a ku Yuda ndiponso ana aamuna a abale ake a Ahaziya, amene ankatumikira Ahaziya, iye nkuŵapha onsewo.

9Adafunafuna Ahaziya, ndipo adamgwira pamene ankabisala ku Samariya. Adabwera naye kwa Yehu, namupha. Anthuwo adamuika m'manda, poti ankati, “Ameneyu ndi mdzukulu wa Yehosafati uja amene ankatumikira Chauta ndi mtima wake wonse.” Choncho banja la Ahaziya linalibe munthu woti nkukhala mfumu yomalamulira.

10Tsono Ataliya, mai wake wa Ahaziya, ataona kuti mwana wake wafa, adanyamuka nakaononga onse a pa banja laufumu la Yuda.

11Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu, adatenga Yowasi mwana wa Ahaziya. Adachita momuba, kumuchotsa pakati pa ana aamuna a mfumu amene ankati aŵaphewo. Adamuika m'chipinda china chogona cha m'Nyumba ya Chauta pamodzi ndi mlezi wake. Motero Yehoseba, mwana wamkazi wa mfumu Yehoramu, mkazi wake wa wansembe Yehoyada, poti anali mlongo wake wa Ahaziya, adambisa mwanayo, kotero kuti Ataliya sadamuphe.

12Mwanayo adakhala ndi iwowo zaka zisanu ndi chimodzi, akubisala m'Nyumba ya Chauta, pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help