1Holofernesi adauza Yuditi kuti, “Mai, limba mtima, usaope. Chikhalire ine sindidapwetekepo aliyense wosankha kutumikira Nebukadinezara, mfumu ya pa dziko lonse lapansi.
2Ngakhale tsopano, sindikadaŵasamulira lupanga anthu akumapiriŵa, akadapanda kundichita chipongwe. Iwowo adangodziputira okha nkhondo.
3Tsono tanena, waŵathaŵiranji ndi kubwera kwa ife kuno? Wapulumutsa moyo wako pobwera kuno. Limba mtima, zoopsa sizikugwera usiku uno, ngakhale m'tsogolo muno. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzakuchite kanthu koipa.
4Udzakhala pabwino, monga momwe amakhalira anthu ake a mbuye wanga, mfumu Nebukadinezara.”
5Yuditi adayankha kuti, “Mundilole kuti ndilankhule nanu mbuye wanga, ndipo chonde mumve zimene nditi ndilankhule nanu. Mau amene ndikukuuzani usiku uno ngoona.
6Mukatsata malangizo anga, Mulungu adzachita zazikulu kudzera mwa inu, ndipo mbuye wanga sadzalephera kuchita zimene adakonza kuti achite.
7Yer. 27.6; Dan. 2.38Ndikulumbira pali Nebukadinezara wamoyo, mfumu ya dziko lonse lapansi, ndiponso pali mphamvu zake. Paja ndiye amene adakutumani inuyo kuti muzilamulira zolengedwa zonse. Choncho si anthu okha amene adzamtumikira, koma nyama zakuthengo ndi zoŵeta ndiponso mbalame zomwe zidzamtumikira iye ndi banja lake lonse chifukwa cha inu mbuye wanga.
8Tamva kuti ndinu wanzeru ndi waluntha kwambiri. Pa dziko lonse lapansi anthu akukudziŵani kuti abwino ndinu nokha mu ufumu wonse uno, ndipo kuti ndinu wodziŵa kwambiri ndiponso walusodi pa nzeru zomenyera nkhondo.
9“Tikudziŵa mau amene Akiyore adalankhula mu msonkhano wanu, chifukwa anthu a ku Betuliya adampulumutsa, ndipo iye adaŵauza zonse zimene adakuuzani.
10Musanyozere zimene adakuuzanizo, inu mbuye wanga ndi bwana wanga, koma mau akewo muŵasamale kwambiri. Mauwo ngoona. Anthu a mtundu wathu salangidwa, ndipo sagonjetsedwa ndi lupanga, kupatula akachimwira Mulungu wao.
11“Komabe inu mbuye wanga, simudzalephera kuŵagonjetsa. Imfa ili pafupi kuŵagwera, poti pangotsala pang'ono kuti achimwe, ndipo machimo aowo adzautsa mkwiyo wa Mulungu, iwo akadzachita zoipazo.
12Popeza kuti chakudya chaŵathera, ndipo alibe madzi, atsimikiza zoti azidya ziŵeto zao ndi zakudya zina zimene Mulungu adaŵaletsa.
13Eks. 23.19; Lev. 27.30Atsimikizanso zoti azidya tirigu woyambirira kucha ndiponso zachikhumi za vinyo ndi za mafuta, ngakhale kuti zimenezo nzoyenera kuzipereka kwa Mulungu ndiponso nzoyenera kudya ansembe okha otumikira Ambuye Mulungu wathu ku Yerusalemu, mwakuti anthu wamba sayenera nkuzikhudza komwe.
14Atuma anthu ku Yerusalemu kuti akapemphe chilolezo kwa akulu, popeza kuti anthu akumeneko nawonso akuchita zomwezo.
15Tsono akangolandira chilolezo namadyadi zoperekazo, ndiye kuti tsiku lomwelo adzaperekedwa kwa inu, ndipo mudzaŵaononga.
16“Motero mbuye wanga, ine nditamva zimenezi, ndidaŵathaŵira, ndipo Mulungu wandituma kwa inu, kuti ine ndi inu tichite zinthu zimene zidzadabwitsa dziko lonse lapansi, anthu atazimva.
17Pajatu ine mdzakazi wanu ndine wokonda kupemphera, ndimapembedza Mulungu wa Kumwamba usana ndi usiku. Choncho ndidzakhala ndi inu mbuye wanga, koma usiku uliwonse ndidzapita ku chigwa kukapemphera kwa Mulungu, ndipo Iyeyo adzandiwuza anthu aja akadzachimwa.
18Ine pobwera ndidzakuuzani; apo inu mudzanyamuka ndi ankhondo anu onse, ndipo anthuwo sadzakukanikani.
19Ndidzakutsogolerani kubzola ku Yudeya mpaka ku Yerusalemu ndipo ndidzakulongani ufumu mumzindamo. Anthuwo adzakutsatani ngati nkhosa zopanda mbusa, ndipo ndi galu yemwe sadzakuuŵani. Mulungu wandiwuziratu zimenezi, ndipo wandituma kuti ndidzakuuzeni.”
20Mau a Yuditi adakondweretsa Holofernesi ndi atumiki ake onse. Onse adadabwa ndi nzeru zake.
21Adati, “Pa dziko lonse lapansi palibe mkazi woti angafanane ndi ameneyu kukongola kwake ndi kuchenjera polankhula.”
22Holofernesi adauza Yuditi kuti, “Uthokoze Mulungu pokutuma kuno kuti udzatilimbikitse, kuti tiwononge anthu onyoza mbuye wanga Nebukadinezara.
23Sindiwe mkazi wokongola chabe, komanso umalankhula zanzeru. Ukachita monga m'mene walonjezera, Mulungu wako adzakhala Mulungu wanga, udzakhala m'nyumba ya mfumu Nebukadinezara, ndipo udzatchuka pa dziko lonse lapansi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.