Yes. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Tsiku limenelo akazi asanu ndi aŵiri adzagwira mwamuna mmodzi, nkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu nkumavala zovala zathu; inu mungotilola tizitchulidwa akazi anu, kuti manyazi aumbeta atichoke.”

Yerusalemu adzakhalanso pabwino

2Tsiku limenelo Chauta adzaphukitsa Nthambi yake imene idzakhala yokongola ndi yaulemerero. Ndipo chipatso cha m'dziko la Israele chidzaŵanyaditsa ndi kuŵapatsa ulemerero onse otsalira.

3Tsono otsalira ku Ziyoni, amene Mulungu waŵasankha kuti akhale ndi moyo ku Yerusalemu, adzatchedwa oyera.

4Pamenepo Ambuye adzakhala atasambitsa akazi a ku Ziyoni ndi kuchotsa zonyansa zao, ndipo adzakhala atatsuka magazi amene adakhetsedwa mu Yerusalemu. Adzachita zimenezi ndi mpweya woweruza ndi woyeretsa ndi moto.

5Eks. 13.21; 24.16 Tsono masana Chauta adzaika mtambo ndi utsi kuzungulira phiri lonse la Ziyoni, pamwamba pa anthu ake. Usiku adzaika malaŵi a moto oŵala. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Chauta.

6Ulemerero wake udzakhala mthunzi wothaŵiramo kutentha kwa masana, udzakhala malo opeweramo mphepo ndi ousiramo mvula.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help