Mt. 23 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yesu achenjeza anthu za aphunzitsi a Malamulo ndi za Afarisi(Mk. 12.38-39; Lk. 11.46, 52; 20.45-46)

1Pambuyo pake Yesu adalankhula ndi gulu la anthu ochuluka pamodzi ndi ophunzira ake.

2Adaŵauza kuti, “Aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi ali ndi udindo wotanthauzira malamulo a Mose.

3Nchifukwa chake muzichita ndi kutsata zonse zimene iwo amakuphunzitsani. Komatu musamatsanzira zimene amachita, pakuti sachita zimene amaphunzitsa.

4Iwo amamanga katundu wosautsa kunyamula nkusenzetsa anthu, koma iwowo samukhudzako mpang'ono pomwe.

5Mt. 6.1; Deut. 6.8; Num. 15.38Zonse zimene amachita amangozichita kuti anthu aŵaone. Amadzimangirira timapukusi tikulutikulu ta mau a Mulungu pa mphumi ndi pa mkono. Amatalikitsanso mphonje za zovala zao.

6Amakonda malo olemekezeka pa maphwando ndiponso mipando yaulemu kwambiri ku nyumba zamapemphero.

7Amakondanso kuti anthu aziŵalonjera mwaulemu pa misika, ndipo kuti aziŵatchula aphunzitsi.

8“Koma inuyo anthu asati azikutchulani aphunzitsi, pakuti muli ndi Mphunzitsi mmodzi yekha, ndipo nonsenu muli pa chibale.

9Musamatchulanso munthu pansi pano kuti atate, popeza kuti muli ndi atate amodzi okha, ndiwo Atate anu akumwamba.

10Anthu asatinso azikutchulani atsogoleri, popeza kuti Mtsogoleri wanu ndi mmodzi yekha, ndiye Khristu.

11Mt. 20.26, 27; Mk. 9.35; 10.43, 44; Lk. 22.26Pakati panupa wamkulu akhale mtumiki wanu.

12Lk. 14.11; 18.14Pajatu aliyense wodzikuza adzamchepetsa, ndipo aliyense wodzichepetsa adzamkuza.”

Yesu adzudzula aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi(Mk. 12.40; Lk. 11.39-42, 44, 52; 20.47)

13“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumatseka pakhomo pa Ufumu wakumwamba kuti anthu asaloŵemo. Paja inu nomwe simuloŵamo, ndipo mumatsekereza amene amafuna kuloŵamo.”

[

14“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumagongolera azimai amasiye nkumaŵadyera chuma chao, kwinaku nkumanyengezera kunena mapemphero ataliatali. Chifukwa cha zimenezi Mulungu adzakulangani koposa.”]

15“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumayenda maulendo ambirimbiri pa nyanja ndi pa mtunda, kufunafuna ngakhale munthu mmodzi yekha kuti atembenuke ndi kusanduka wophunzira wanu. Tsono akapezeka, mumamsandutsa woyenera kulangidwa ku Gehena kuposa inu kaŵiri.

16“Muli ndi tsoka, inu atsogoleri akhungu! Inu mumati, ‘Munthu akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti, Pali chuma cha m'Nyumba ya Mulungu, asunge lumbiro lakelo.’

17Inu anthu opusa ndi akhungu! Chachikulu nchiti, chuma chija, kapena Nyumba imene ikusandutsa chumacho kuti chikhale chopatulika?

18Mumatinso, ‘Munthu akalumbira kuti, Pali guwa lansembe, lumbirolo nlachabe. Koma akalumbira kuti, Pali choperekedwa pa guwa, asunge lumbiro lakelo.’

19Anthu akhungu inu! Chachikulu nchiti, choperekedwa chija, kapena guwa lansembe lija limene likusandutsa choperekedwacho kuti chikhale chopatulika?

20Tsonotu munthu akalumbira kuti, Pali guwa la nsembe, walumbiranso pa zonse zimene zili paguwapo.

21Akalumbira kuti, Pali Nyumba ya Mulungu, walumbiranso pa zonse zimene zili m'Nyumbamo.

22Yes. 66.1; Mt. 5.34Ndipo akalumbira kuti, Kumwambadi, walumbiranso pa mpando wachifumu wa Mulungu, ndiponso pa Iye amene amakhala pampandopo.

23 Lev. 27.30 “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumapereka chachikhumi cha timbeu tonunkhira, ndi cha timbeu tokometsera chakudya, koma simusamala zazikulu zenizeni pa Malamulo a Mulungu, monga kuweruza molungama, kuchita zachifundo, ndi kukhala okhulupirika. Mukadayenera kuchitadi zimenezi, komabe osasiya zinazo.

24Inu atsogoleri akhungu, mumasuza zakumwa zanu kuti muchotsemo kanchenche, koma mumameza ngamira.

25“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumatsuka kunja kwa chikho ndi kwa mbale koma m'kati mwake m'modzaza ndi nzeru zakuba, ndi zaumbombo.

26Afarisi akhungu inu, yambani mwatsuka m'kati mwa chikho, ndipo kunja kwakenso kudzayera.

27 Ntc. 23.3 “Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Muli ngati manda opaka njeresa, amene amaoneka okongola kunja, pamene m'kati mwake m'modzaza ndi mafupa a anthu akufa ndi zoola zina zilizonse.

28Inunso muli chimodzimodzi: pamaso pa anthu mumaoneka olungama, pamene m'kati mwanu m'modzaza ndi chiphamaso ndi zoipa zina.

29“Muli ndi tsoka, inu aphunzitsi a Malamulo ndi Afarisi, anthu achiphamaso! Mumakonza bwino manda a aneneri, ndipo mumakongoletsa ziliza za anthu olungama.

30Ndiye mumati, ‘Tikadakhala ndi moyo pa nthaŵi ya makolo athu ija, sibwenzi ife titaŵapha nao aneneriwo ai.’

31Koma potero mukuvomera nokha kuti ndinu zidzukulu za anthu amene adapha aneneriwo.

32Chabwino tsono, itsirizeni ntchitoyo imene makolo anu aja adaiyamba.”

Yesu aneneratu za chilango chao(Lk. 11.47-51)

33 Mt. 3.7; 12.34; Lk. 3.7 “Njoka inu, ana a mamba, mudzachipeŵa bwanji chilango cha ku Gehena?

34Mvetsetsani tsono! Ine ndidzakutumizirani aneneri, ndiponso anthu anzeru ndi aphunzitsi. Ena mudzaŵapha ndi kuŵapachika pa mtanda. Ena mudzaŵakwapula m'nyumba zanu za mapemphero, ndipo mudzaŵazunza pakuŵapirikitsa kuchokera ku mudzi wina mpaka ku mudzi wina.

35Gen. 4.8; 2Mbi. 24.20, 21Motero chilango chidzakugwerani chifukwa cha anthu olungama onse amene adaphedwa, kuyambira kuphedwa kwa Abele, munthu wolungama uja, mpaka kuphedwa kwa Zakariya, mwana wa Barakiya, amene mudamuphera m'Nyumba ya Mulungu pakati pa guwa lansembe ndi Malo Opatulika kopambana.

36Ndithu ndikunenetsa kuti chilango cha zonsezi chidzaŵagwera ndithu anthu amakonoŵa.”

Yesu alira chifukwa cha Yerusalemu(Lk. 13.34-35)

37“Iwe Yerusalemu, Yerusalemu! Umapha aneneri, nkuŵaponya miyala anthu amene Mulungu amakutumizira. Nkangati ndakhala ndikufuna kusonkhanitsa anthu ako, monga momwe nkhuku imasonkhanitsira anapiye ake pansi pa mapiko ake, iwe nkumakana!

38Yer. 22.5Ndithu nyumba yanu yaikuluyi idzasanduka bwinja.

39Mas. 118.26Ndipo ndikunenetsa kuti simudzandiwonanso konse mpaka mudzati, ‘Ngwodala amene alikudza m'dzina la Ambuye.’ ”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help