Eks. 9 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zoŵeta zifa

1Pambuyo pake Chauta adalamula Mose kuti, “Pita kwa Farao ukamuuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, akunena kuti uŵalole anthu anga apite akandipembedze.

2Koma ukakananso kuŵalola kuti apite, ndi kuŵaletsa ndithu,

3dzanja la Chauta lidzakulanga ndi mliri woopsa pa zoŵeta zako monga akavalo, abulu, ngamira, ng'ombe, nkhosa ndi mbuzi zomwe.

4Ndidzasiyanitsa pakati pa zoŵeta za Aisraele ndi za Aejipito. Motero palibe choŵeta nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidzafe.

5Chauta waika nthaŵi, ndipo akunena kuti zimenezi azichita maŵa.’ ”

6Tsono m'maŵa mwake Chauta adachitadi monga momwe adanenera, ndipo zoŵeta zonse za Aejipito zidafa. Koma panalibe choŵeta nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo.

7Ndipo Farao atafunsitsa zimene zidaachitikazo, adamva kuti palibe ndi chiŵeto nchimodzi chomwe cha Aisraele chimene chidafapo. Komabe Farao adakhala wokanika ndithu, ndipo sadalole konse kuti anthuwo apite.

Zithupsa

8Pamenepo Chauta adalamula Mose ndi Aroni kuti, “Tapaniko phulusa lapamoto. Tsono Mose awaze phulusalo kumwamba pamaso pa Farao.

9Phulusalo lidzaulukira m'dziko lonse la Ejipito ngati fumbi. Ndipo konse kumene lidzaulukireko, kudzabuka zithupsa zomaphulika ndi kusanduka zilonda pa anthu ndi pa nyama zomwe.”

10Chiv. 16.2 Choncho Mose adatapa phulusalo pa moto ndipo adakaimirira pamaso pa Farao. Adawaza phulusalo kumwamba, ndipo padabuka zithupsa zimene zidaphulika ndi kusanduka zilonda pa anthu ndi pa nyama zomwe.

11Amatsenga aja sadathenso kufika pamaso pa Mose chifukwa iwonso anali ndi zithupsa zokhazokha, monga Aejipito onse.

12Koma Mulungu adamuumitsa mtima Farao, ndipo Faraoyo sadaŵalole anthuwo kuti apite monga momwe Chauta adaauzira Mose muja.

Matalala

13Apo Chauta adauza Mose kuti, “Maŵa m'mamaŵa upite ukakumane ndi Farao, ukamuuze kuti, ‘Chauta, Mulungu wa Ahebri, akunena kuti uŵalole anthu anga kuti apite, akandipembedze.

14Tsopano ndikuti ndigwetsere miliri yanga yonse pa iwe, pa nduna zako, ndi pa anthu ako, ndipo udzadziŵa kuti palibe wina aliyense wofanafana ndi Ine pa dziko lonse lapansi.

15Ndikadasamula dzanja langa kuti ndikumenye iwe pamodzi ndi anthu ako, bwenzi tsopano nonsenu mutatha.

16Aro. 9.17 Koma ndakusungani ndi moyo kuti muwone mphamvu zanga, kuti mbiri yanga iwande pa dziko lonse lapansi.

17Koma ukunyozabe anthu anga, osafuna kuŵalola kuti apite.

18Imvani tsono, nthaŵi yomwe ino maŵa, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo nkale lonse mu Ejipito muno chiyambire cha dziko lino.

19Tsopano lamula kuti zoŵeta zanu zonse zikhale m'khola pamodzi ndi zonse zimene muli nazo. Matalala adzagwa pa anthu ndi pa nyama zonse zongoyenda pa bwalo, chifukwa chosaziloŵetsa m'khola, ndipo zonsezo zidzafa.’ ”

20Nduna zina za Farao zidachita mantha chifukwa cha mau amene adanena Chauta, ndipo zidatsekera akapolo ao m'nyumba pamodzi ndi zoŵeta zao zomwe.

21Komabe ena sadasamaleko zimene Chauta adanenazo, ndipo adangosiya panja akapolo ao pamodzi ndi zoŵeta zomwe.

22Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Kweza dzanja lako kumwamba, ndipo matalala adzagwa pa anthu, pa nyama, ndi pa zomera zonse zam'minda, m'dziko lonse la Ejipito.”

23Mose adakweza ndodo yake kumwamba. Pompo Chauta adatumiza mabingu ndi matalala, ndipo mphezi zidaomba pa nthaka. Chauta adagwetsa matalala pa dziko la Ejipito.

24Chiv. 8.7; 16.21 Ndipo panali mvula yamatalala ndi mphezi zong'anima kwambiri. Matalala ake anali oopsa kwambiri, kotero kuti chiyambire pamene Aejipito adasanduka mtundu wa anthu oima paokha, matalala otere sadagwepo.

25Matalalawo adaononga zonse zokhala panja m'dziko lonse la Ejipito, anthu onse pamodzi ndi nyama zomwe. Adaononganso zomera zonse zam'minda ndi kukadzulanso mitengo yonse.

26Dziko la Goseni lokha, kumene kunkakhala Aisraele, matalalawo sadagweko mpang'ono pomwe.

27Pamenepo Farao adaitana Mose ndi Aroni naŵauza kuti, “Zoonadi, ndachimwa ndithu tsopano. Chauta ndi wolungama, koma ineyo pamodzi ndi anthu anga, tonse ndife ochimwa.

28Pemphera kwa Chauta kuti aŵaletse mabingu ndi matalalaŵa ndipo ndidzakulolani kuti mupite. Simudzakhalanso kuno ai.”

29Mose adamuuza kuti, “Ndikangotuluka mumzinda muno, ndikweza manja anga kwa Chauta. Tsono mabingu ndi matalala aleka, kuti inuyo mudziŵe kuti dziko lonse lapansi ndi la Chauta.

30Komabe ndikudziŵa kuti inu ndi nduna zanu simukuwopa Chauta.”

31Ndipo thonje lidaonongeka pamodzi ndi barele yemwe, chifukwa choti bareleyo anali atacha, ndipo thonjelo linali ndi nkhunje.

32Koma tirigu ndi rayi sizidaonongeke, chifukwa zimenezi amabzala mochedwa.

33Mose adachoka kwa Farao kuja, natuluka mumzindamo. Ndipo adakweza manja ake kumwamba, napemphera kwa Chauta. Tsono mabingu aja ndi matalala adaleka, ndipo mvula idakata.

34Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu, zonsezo zaleka, adakhala wokanikabe, nauma ndithu mtima iyeyo ndi nduna zake zija.

35Adakhala wokanika kwambiri, ndipo sadalole kuti Aisraele apite monga momwe Chauta adaauzira Mose muja.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help