Tob. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tobiyasi akwatira Sara

1Atatha kudya ndi kumwa, adafuna kugona. Adaperekeza mnyamatayo m'chipinda muja.

2Tsono Tobiyasi adakumbukira mau a Rafaele aja. Adatulutsa m'thumba muja chiŵindi cha nsomba chija pamodzi ndi mtima wake uja, naziika pa moto wa lubani.

3. Rafaele adamutsatira komweko, ndipo atamupeza adamukwidzinga ndi unyolo.

4Tobiyasi ndi Sara atakhala okha ndipo atatseka pakhomo pa chipinda, Tobiyasi adadzuka m'bedi, nauza Sara kuti, “Mlongo wanga, dzuka, tiyambe tapemphera ndi kupembedza Ambuye, kuti atichitire chifundo ndi kutiteteza.”

5Dani.Sara adadzuka, ndipo onse aŵiri adayamba kupemphera kuti Ambuye aŵateteze. Tobiyasi adati,

“Tikukutamandani, Inu Mulungu wa makolo athu,

dzina lanu litamandike pa mibadwo yonse.

Zakumwamba zikuyamikeni,

zonse zimene mudazilenga

zikuyamikeni mpaka muyaya.

6 Gen. 2.18 “Ndinu mudalenga Adamu,

ndinunso mudalenga Heva mkazi wake

kuti azimuthandiza ndi kumuchirikiza.

Ndipo mwa aŵiriwo mudafumira

mtundu wonse wa anthu.

Ndinu mudaanena kuti,

‘Sibwino kuti munthuyu akhale yekha,

tiyeni timupangire mthandizi wake

wofanafana naye.’

7“Tsopano ndikumtenga mlongo wangayu

osati chifukwa cholakalaka chisangalatso chabe,

koma kuti ndichite ukwati weniweni.

Choncho mutichitire chifundo, ine ndi iyeyu,

kuti aŵirife tidzakalambire pamodzi.”

8Tsono aŵiriwo adati, “Amen, Amen,”

9nkupita kukagona usikuwo.

Usiku womwewo Raguele adadzuka, naitana akapolo ake, kuti akamthandize kukumba manda.

10Mumtima mwake ankaganiza kuti, “Mwina Tobiyasiyunso afa, ndiye anthu ena adzatiseka ndi kutinyoza.”

11Atatha kukumba mandawo, Raguele adabwerera kunyumba. Adaitana mkazi wake nati,

12“Tumiza mdzakazi mmodzi kuchipindako, akaone ngati Tobiyasi ali moyobe. Ngati wafa, timuikiretu asanadziŵe ndi munthu mmodzi yemwe.”

13Adamutumizadi mdzakaziyo. Iye adayatsa nyale, nakatsekula pa khomo. Adaloŵa, naŵapeza ali m'tulo, atagona pamodzi.

14Mdzakaziyo adatuluka, nadzaŵanong'oneza iwo aja kuti, “Ai, ali moyo, ali bwinobwino ndithu.”

15Apo iwowo adayamika Mulungu wakumwamba, nati,

“Tikukutamandani, Inu Mulungu,

ndi chiyamiko chonse changwiro.

Mutamandike mpaka muyaya.

16“Mulemekezeke chifukwa chondikondwetsa.

Zimene ndinkaopa sizidachitike.

M'malo mwake mwatiwonetsa

kuti muli ndi chifundo chosaneneka.

17“Mutamandike chifukwa cha chifundo

chimene mwaŵaonetsa ana athu aŵiriŵa,

amene aliyense ndi mmodzi yekha m'banja mwao.

Muŵakomere mtima ndi kuŵatchinjiriza,

Inu Ambuye,

pa moyo wao wonse adzapeze chimwemwe

ndi chifundo.”

18Tsono Tobiti adalamula akapolo ake kuti akafotsere dzenje lija kusanache.

19Pambuyo pake adauza mkazi wake kuti aphike buledi wambiri. Adapita ku khola kukatenga ng'ombe ziŵiri ndi nkhosa zinai. Adalamula kuti azikonze, ndipo adayambadi kuziphika.

20Gen. 24.55Adaitana Tobiyasi namuuza kuti, “Pa milungu iŵiri usachoke kuno, ubakhala konkuno, kuti udye nafe ndi kumwa, ndipo uzisangalatsa mtima wa mwana wanga amene wakhala akuvutika ndi chisoni.

21Ulandire theka la chuma changa, ndipo ubwerere uli moyo kwa atate ako. Theka lina, tikadzafa ine ndi mkazi wanga, lidzakhalanso lako. Limba mtima, mwana wanga! Ndine bambo wako, Edina ndi mai wako. Ndife makolo ako mpaka m'tsogolo, monga m'mene takhalira makolo a mkazi wako tsopano ndi nthaŵi zonse. Limba mtima, mwana wanga.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help