Yer. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Adani athira nkhondo Yerusalemu

1Inu anthu a ku Benjamini thaŵani,

tulukanimo m'Yerusalemu.

Lizani lipenga ku Tekowa,

kwezani mbendera ku Betehakeremu.

Tsoka likudzakugwerani kuchokera kumpoto,

ndipotu nchiwonongeko chachikulu.

2Ndidzauwononga mzinda wa Ziyoni,

mzinda wooneka bwino ndi wokongola.

3Mafumu adzabwera ndi asilikali ao.

Adzamanga zithando momzinga Yerusalemu,

ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.

4Adzanena kuti,

“Konzekani kuti muuthire nkhondo mzindawu.

Bwerani tiwuthire nkhondo masana ano.”

“Koma tili ndi tsoka, dzuŵa lapendeka,

zithunzithunzi zakumadzulo zikunka zitalika.”

5“Bwerani tsono tiwuthire nkhondo usiku uno,

tiwononge malinga ake.”

6Mau a Chauta Wamphamvuzonse akuti,

“Gwetsani mitengo ya mu Yerusalemu,

ndipo mzindawu muumangire nthumbira zankhondo.

Mzinda umenewu ndi woyenera kulangidwa,

anthu ake amangokhalira kuzunzana.

7Monga momwe chitsime chimasungira madzi ake,

ndimonso m'mene mzindawo umasungira zoipa zake.

Zimene mukumva ndi za chiwonongeko ndi za nkhondo.

Ndikuwonamonso matenda ndi zilonda.

8Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro,

kuwopa kuti chikondi changa pa iwe chingathe,

ndipo ndingakusandutse dziko lachipululu,

dziko lopanda anthu.”

Aisraele ngosamvera

9Mau a Chauta Wamphamvuzonse akuti,

“Akunkheni ndi kuŵalanda zonse

anthu otsala a Aisraele,

monga momwe anthu amachitira,

populula mphesa ku nthambi zake.”

10Kodi ndilankhule ndi yani,

ndipo ndichenjeze yani, kuti amve?

Makutu ao ndi otsekeka,

sangathe kumva.

Mau a Chauta amaŵanyoza kwambiri,

saŵalabadira konse.

11Nchifukwa chake ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Chauta,

sindingathenso kudzimanga kuti usatulukire kunja.

Chauta akuti,

“Mkwiyo umenewu ukauthire pa ana oyenda mu mseu,

ndi pa achinyamata kumene amasonkhanira.

Mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa,

ngakhale aimvi ndi okalamba kwambiri.

12Nyumba zao zidzapatsidwa kwa ena

pamodzi ndi minda yao ndi akazi ao omwe.

Ndithuditu, ndi dzanja langali

ndidzakantha anthu okhala m'dzikomo.

13“Pakuti onse, ang'onoang'ono ndi akuluakulu omwe,

ali ndi khwinthi la phindu lopeza mwakuba.

Aneneri pamodzi ndi ansembe ao,

onsewo ndi onyenga.

14 Ezek. 13.10 Iwo amapoletsa mabala a anthu anga pamwamba pokha.

Amangonena kuti, ‘Kuli mtendere, kuli mtendere,’

chonsecho kulibe konse mtendere.

15 Yer. 8.10-12 Kodi akamachita zonyansa, amachita manyazi ngati?

Iyai, sachita manyazi mpang'ono pomwe.

Sadziŵa nkugwetsa nkhope komwe.

Nchifukwa chake adzagwera pakati pa anzao

amene adagwa kale.

Adzagweratu pa tsiku limene ndidzaŵalanga!”

Akutero Chauta.

16Mau a Chauta ndi aŵa,

“Imani pa mphambano, ndipo mupenye.

Mufunse kumene kuli njira zakale

ndi kumene kuli njira yabwino.

Tsono mutsate njira yabwinoyo,

ndipo mudzakhala pa mtendere.

Koma inuyo mudati, ‘Sitidzaitsata.’

17Chauta adakupatsani alonda oti akutsogolereni nati,

‘Imvani kulira kwa lipenga lokuchenjezani.’

Koma inu mudati, ‘Sitidzasamalako.’

18Nchifukwa chake imvani inu anthu a mitundu ina,

penyetsetsani, inu mwasonkhana panonu,

zimene zidzaŵagwere anthuwo.

19Tamvani inu okhala pa dziko lapansi,

anthuwo ndidzaŵaononga.

Komatu zimenezo nzotsatira za kunyenga kwao,

chifukwa sadamvere mau anga

ndipo sadamvere malamulo anga.

20Kodi pali phindu lanji kwa Ine,

ngakhale abwere ndi lubani kuchokera ku Sheba,

kapena zonunkhira zina kuchokera ku maiko akutali?

Sindidzalandira zopereka zao zopsereza,

nsembe zao sizindikondwetsa.

21Nchifukwa chake anthu ameneŵa

ndidzaŵaikira zoŵakhumudwitsa.

Atate ndi ana ao aamuna,

anansi ndi abwenzi ao,

onsewo adzaonongeka.”

Adani ochokera kumpoto

22Chauta akunena kuti,

“Onani, anthu a mtundu wina akubwera

kuchokera ku dziko lakumpoto.

Mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka

kuchokera mbali zakutalitali za dziko lapansi.

23Atenga mauta ndi mikondo,

ndi anthutu ankhalwe ndi opanda chifundo.

Phokoso lao lili ngati mkokomo wa nyanja.

Akwera pa akavalo,

akonzekera ngati munthu wankhondo,

akudzamenyana nawe, iwe Ziyoni.”

24A ku Yerusalemu akuti,

“Mbiri ya iwowo taimva,

m'nkhongono mwati zii.

Nkhaŵa yatigwira,

ndipo tikumva ululu wonga wa mkazi

panthaŵi yake yochira.”

25Musayesere kupita ku minda,

kapena kuyenda pa mseu,

pakuti adani akubwera ndi nkhondo

ndipo ponseponse pali mantha okhaokha.

26Inu anthu anga, valani ziguduli,

gubuduzikani pa phulusa.

Lirani kwamphamvu,

ngati munthu wolira mwana wake mmodzi yekha,

pakuti mwadzidzidzi woononga adzabwera kudzakuphani.

27“Iwe Yeremiya, ndakusankha

kuti ukhale choyesera zitsulo.

Uŵayese anthu anga

kuti uwone m'mene aliri makhalidwe ao.

28Onsewo ali ndi upandu wokanika,

onsewo ndi akazitape,

ndi olimba ngati mkuŵa ndi chitsulo.

Onse amangochita zoipa zokhazokha.

29Mvukuto zikuuzira kwambiri,

mtovu wasungunuka ndi moto.

Koma ntchito yosungunulayo sikupindula,

chifukwa choti dothi loipa silikuchokapo.

30Iwo ali ngati siliva wotaya,

pakuti Chauta waŵakana.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help