1Rehobowamu atafika ku Yerusalemu, adasonkhanitsa ankhondo osankhidwa okwanira 180,000, afuko la Yuda ndi la Benjamini, ndi cholinga akamenyane nkhondo ndi anthu a ku Israele, kuti choncho ambwezere Rehobowamu ufumu wake.
2Koma Chauta adadza kwa Semaya, m'meneri wake, namlamula kuti,
3“Ukauze Rehobowamu, mwana wa Solomoni, mfumu ya ku Yuda, ndi Aisraele onse a ku Yuda ndi a ku Benjamini kuti,
4‘Ine Chauta ndikuti, Musapite kukamenyana ndi abale anu. Aliyense abwerere kwao, poti zimene zachitikazi zachokera kwa Ine.’ ” Anthuwo adamvera mau a Chauta, nadabwerera osapita kukamenyana ndi Yerobowamu.
Rehobowamu alimbitsa mizinda5Rehobowamu ankakhala ku Yerusalemu, ndipo adamanga mizinda yamalinga ku Yuda.
6Adamanga Betelehemu, Etamu, Tekowa,
7Betezuri, Soko, Adulamu,
8Gati, Maresa, Zifi,
9Adoraimu, Lakisi, Azeka,
10Zora, Aiyaloni ndi Hebroni. Mizinda yamalinga yonseyo inali ku Yuda ndi ku Benjamini.
11Malinga ake adamanga olimba, ndipo adaikamo atsogoleri a nkhondo. Adaikamonso chakudya, mafuta ndi vinyo.
12Adaikamo zishango ndi mikondo, ndipo adaitchinjiriza kwambiri mizindayo. Choncho ankalamulira anthu a ku Yuda ndi a ku Benjamini.
Ansembe ndi Alevi abwera ku Yuda13Ansembe pamodzi ndi Alevi amene anali m'dziko lonse la Israele adatsata Rehobowamu, kuchoka konse kumene ankakhala.
14Alevi adasiya mabusa ao ndi maiko ao, ndipo adapita ku Yuda ndi ku Yerusalemu, chifukwa chakuti Yerobowamu ndi ana ake anali ataŵachotsa pa ntchito zao zaunsembe zomatumikira Chauta.
151Maf. 12.31 Yerobowamu adaadzisankhira ansembe ake, kuti azitumikira ku kachisi ku zitunda, kupembedza mizimu yoipa ndi mafano a atonde ndi a anaang'ombe amene adaŵapanga.
16Tsono anthu amene adatsimikiza mumtima mwao kuti azitumikira Chauta, Mulungu wa Israele, ankatsatira ansembe ndi Alevi aja, kuchoka ku mafuko a ku Israele, kupita ku Yerusalemu kukapereka nsembe kwa Chauta, Mulungu wa makolo ao.
17Iwowo adalimbitsa ufumu wa Yuda, ndipo adamsunga Rehobowamu mwana wa Solomoni zaka zitatu, chifukwa chakuti pa zaka zitatuzo ankatsata chitsanzo cha Davide ndi cha Solomoni.
Banja la Rehobowamu18Rehobowamu adakwatira Mahalati, amene bambo wake anali Yerimoti, mwana wa Davide, ndipo mai wake anali Abihaili mwana wa Eliyabu mwana wa Yese.
19Mkaziyo adambalira ana aŵa: Yeusi, Semariya ndi Zahamu.
20Adakwatiranso Maaka mwana wa Abisalomu, ndipo adambalira Abiya, Atai, Ziza ndi Selomiti.
21Rehobowamu ankakonda Maaka mwana wa Abisalomu kupambana akazi ake onse, kupambananso azikazi ake. (Adakwatira akazi 18, ndipo anali ndi azikazi okwanira 60, ndipo anali ndi ana aamuna 28, ana aakazi 60.)
22Rehobowamu adasankha Abiya, mwana wa Maaka, kuti akhale mtsogoleri pakati pa abale ake, poti ankafuna kuti amlonge ufumu iyeyo.
23Tsono mwanzeru adaika ena mwa ana ake aamuna m'zigawo zonse za ku Yuda ndi za ku Benjamini, ku mizinda yonse yamalinga. Ankaŵapatsa chakudya chambiri ndi kuŵafunira akazi ochuluka.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.