Ezek. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ulemerero wa Chauta uchoka ku Nyumba yake

1 Ezek. 1.26; Chiv. 4.2 Ndidayang'ana ku thambo lija lili pamwamba pa mitu ya akerubi, ndipo ndidaona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wokoma wa safiro.

2Chiv. 8.5 Tsono Chauta adauza munthu wovala zabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi, udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa Akerubiwo. Tsono makalawo uŵawaze mu mzinda.” Ndipo ndidamuwona akupitadi.

3Ndiye kuti akerubi adaaimirira ku dzanja lamanja la Nyumba ya Chauta pamene munthuyo ankaloŵa. Ndipo mtambo udaadzaza bwalo lam'kati.

4Ulemerero woŵala wa Chauta udachoka pamene udaali, pamwamba pa akerubi, nukafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Tsono Nyumbayo idadzaza ndi mtambo uja, ndipo ulemerero woŵala uja wa Chauta udadzaza bwalo.

5Phokoso la mapiko a akerubi lidamveka mpaka ku bwalo lakunja, monga momwe limamvekera liwu la Mulungu Mphambe akamalankhula.

6Kenaka Mulungu adauza munthu wovala zabafuta uja kuti akapale moto pakati pa mikombero, kunsi kwa akerubi. Munthuyo adaloŵa nakaima pambali pa mkombero umodzi.

7Pomwepo mmodzi mwa akerubiwo adatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pao. Adapalako motowo, napatsa munthu wovala zabafuta uja. Iyeyo adalandira motowo nkutuluka.

8Ndiye kuti kunsi kwa mapiko a akerubi kunali chinthu chooneka ngati dzanja lamunthu.

9 Ezek. 1.15-21 Pambuyo pake ndidaona mikombero inai pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi. Mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala ya krizoliti.

10Maonekedwe a mikomberoyo anali ofanana, ndipo inali yoloŵanaloŵana.

11Poyenda akerubiwo ankapita mbali iliyonse mwa mbali zao zinai zimene ankayang'ana, osachita kutembenuka. Kumene mutu walunjika, nkumene ankapita.

12Chiv. 4.8 Matupi ao, misana yao, mapiko ao pamodzi ndi mikombero yonse inai, zonse zinali ndi maso.

13Ndidamva phokoso la mikombero monga lomwe ndidaalimva poyamba paja pamene ndinkaona zinthu m'masomphenya.

14Ezek. 1.10; Chiv. 4.7 Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinai. Nkhope yoyamba inali ya kerubi, yachiŵiri inali ya munthu, yachitatu inali ya mkango, yachinai inali ya chiwombankhanga.

15Tsono akerubi aja adauluka. Akerubiwo anali zilengolengo zonzija zimene ndidaaona ku mtsinje wa Kebara.

16Akerubi ankati akamayenda, nayonso mikombero inkayenda m'mbali mwao. Pamene akerubi ankatambasula mapiko ao ndi kuuluka, mikombero inali m'mbali mwao ndithu.

17Zilengolengo zikaima, mikombero inkaimanso. Zikauluka, mikombero inkapita nawo ndithu, pakuti mzimu wa zilengolengozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo.

18Pamenepo ulemerero woŵala wa Chauta udachokapo pa chiwundo cha Nyumba yake nukakhalanso pamwamba pa akerubi.

19Apo Akerubi adatambasula mapiko ao nauluka. Ndidaŵaona akupita, mikombero ili pambali pao. Adakaima pa khomo lakuvuma la Nyumba ya Chauta. Ndipo ulemerero woŵala wa Mulungu wa Israele unali pamwamba pao.

20Zimenezi ndizo zilengolengo zimene ndidaaziwona ku mtsinje wa Kebara, kunsi kwa mpando waufumu wa Mulungu wa Israele. Ndidazindikira kuti zilengolengozo zinali akerubi.

21Akerubiwo aliyense anali ndi mapiko anai ndi nkhope zinai. Analinso ndi chinthu chooneka ngati dzanja lamunthu kunsi kwa mapiko ao.

22Nkhope zao zinali zonga zimene ndidaaziwona m'masomphenya ku mtsinje wa Kebara. Chilengolengo chilichonse chinkayenda molunjika kutsogolo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help