1 Eks. 12.51 Pamene Israele adatuluka ku Ejipito,
pamene banja la Yakobe lidatuluka
kuchokera ku mtundu wa anthu a chilankhulo chachilendo,
2Yuda adasanduka malo opatulika a Chauta,
Aisraele adasanduka anthu a mu ufumu wake.
3 Eks. 14.21; Yos. 3.16 Nyanja idaona zimenezi nithaŵa,
mtsinje wa Yordani udabwerera m'mbuyo.
4Mapiri aakulu adalumphalumpha ngati nkhosa zamphongo,
nazonso zitunda zidalumpha ngati anaankhosa.
5Iwe nyanja, chikukuvuta nchiyani kuti uzithaŵa?
Nanga iwe Yordani, ukubwerereranji m'mbuyo?
6Inu mapiri, chikukuvutani nchiyani,
kuti muzilumphalumpha ngati nkhosa zamphongo?
Nanga inu zitunda, mukulumphiranji ngati anaankhosa?
7Njenjemera iwe dziko lapansi,
chifukwa Chauta akubwera,
zoonadi, akubwera Mulungu wa Yakobe.
8 Eks. 17.1-7; Num. 20.2-13 Iye amasandutsa thanthwe kukhala dziŵe lamadzi,
amasandutsa mwala wolimba kukhala kasupe wa madzi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.