Mphu. 36 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kupempherera Aisraele kuti apulumuke

1Inu Ambuye, mutichitire chifundo,

Inu Mulungu mwini zonse, mutiyang'ane ife.

2Muwopseze anthu onse a mitundu ina.

3Musamule dzanja lanu ndi kulanga mitundu yachilendo,

kuti onsewo adziŵe mphamvu zanu.

4Monga mudaŵaonetsera kuti ndinu oyera pa

zochita zanu pakati pa ife,

momwemonso mutiwonetse ukulu wanu pa zochita

zanu pakati pa iwowo.

5Aphunzire monga tidaphunzirira ife,

kuti palibe Mulungu wina koma Inu nokha Ambuye.

6Onetsani zizindikiro zatsopano ndi kuchita zozizwitsa zinanso,

muwonetse ulemerero wa dzanja lanu ndi mkono wanu wakumanja.

7Mudzutse mkwiyo wanu, mugwetse ukali wanu,

onongani amaliwongo ndi kuthyoleratu adani.

8Mulifulumize tsiku lake,

ndi kukumbukira nthaŵi yake yosankhidwa.

Anthu azisimba za ntchito zanu zodabwitsa.

9Ukali wa mkwiyo wanu uwononge anthu otsala,

adani a anthu anu atheretu.

10Phwanyani mitu ya mafumu a adani athu

amene amati, “Ife pano! Pali yaninso?”

11Sonkhanitsani mafuko onse a Yakobe,

muŵapatsenso dziko lao, monga mudaachitira kale.

12Inu Ambuye, muŵachitire chifundo anthu

otchedwa dzina lanuŵa,

Israele amene mudamutchula mwana wanu wachisamba.

13Muchitire chifundo mzinda

m'mene muli Nyumba yopembedzeramo Inu,

Yerusalemu, mzinda wopumulirako Inuyo.

14Mudzaze Ziyoni ndi nyimbo zambiri zokutamandani,

Nyumba yanu muidzaze ndi ulemerero wanu.

15Achitireni umboni anthu amene mudaŵalenga pa chiyambi,

muchitedi zimene aneneri adalankhula m'dzina lanu.

16Apatseni mphotho anthu okukhulupirirani,

ndipo aneneri anu apezeke kuti ngokhulupirika.

17Inu Ambuye, mverani pemphero la atumiki anu,

potsata zimene mudalonjeza pamene Aroni

adadalitsa anthu anu.

Apo anthu onse a dziko lapansi adzadziŵadi

kuti Inu ndinu Ambuye, Mulungu wamuyaya.

Za kusankhula

18M'mimba mumaloŵa zakudya zosiyanasiyana,

koma chakudya china chimapambana chinzake.

19Monga lilime limazindikira

mitundu yosiyanasiyana ya nyama,

chonchonso munthu wanzeru

amatha kuzindikira mabodza.

20Munthu wa nzeru zopotoka amadzetsa mavuto,

nkofunika munthu wodziŵa zambiri kuti ambwezere

munthu wotere.

Za kusankha mkazi

21Munthu wamkazi amavomera ukwati

mwamuna aliyense,

koma ana aakazi ena ali bwino

koposa anzao.

22Kukongola kwa munthu wamkazi kumasangalatsa

omuyang'ana,

amuna safuna chinanso kuposa pamenepo.

23Ngati mkazi ngwolankhula mofatsa ndi modzichepetsa,

mwamuna wake ngwamwai kupambana amuna ena onse.

24Munthu akatenga mkazi, ndiye kuti wagwira pakulu,

ali ndi mthandizi womuyenera ndiponso nsanamira

yoyedzamirako.

25Kumene kulibe mpanda, mbala zimabako.

Munthu amene alibe mkazi, ntchito nkuyendayenda

ndi kudandaula.

26Ndanitu angakhulupirire mbala yomangoyendayenda

m'mizinda yosiyanasiyana?

Chimodzimodzi ndani angakhulupirire munthu wopanda kwao,

womangogona kulikonse kumene kwamdera?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help