1Atamwalira mfumu Ahabu, Amowabu adaukira Aisraele.
2Tsiku lina mfumu Ahaziya ali ku likulu lake ku Samariya, adagwa kuchokera pa khonde la chipinda chake cham'mwamba, navulala kwambiri. Ndiye adatuma amithenga naŵauza kuti, “Pitani, mukafunse kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni, ngati nditi ndichire.”
3Koma mngelo wa Chauta adauza mneneri Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya, ukaŵafunse kuti, ‘Kodi ku Israele kulibe Mulungu, apa mukupita kukapempha nzeru kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni?’
4Nchifukwa chake tsono mau a Chauta oti mukauze mfumu ndi aŵa: ‘Iweyo sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.’ ” Ndipo Eliya adapita.
5Amithenga aja adabwerera kwa mfumu. Tsono mfumuyo idaŵafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwabwerera?”
6Amithengawo adayankha kuti, “Kudaabwera munthu kudzakumana nafe, ndipo adatiwuza kuti, ‘Bwererani kwa mfumu imene idakutumaniyo, mukaiwuze mau a Chauta akuti, “Kodi ku Israele kulibe Mulungu, apa mukukapempha nzeru kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni? Nchifukwa chake sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.” ’ ”
7Tsono mfumuyo idafunsa amithengawo kuti, “Kodi munthu amene adaabwera kudzakumana nanuyo, namakuuzani zimenezi, ankaoneka bwanji?”
8Mt. 3.4; Mk. 1.6Iwowo adayankha kuti, “Munthuyo adaavala zovala zaubweya ndi lamba wachikopa m'chiwuno.” Apo mfumuyo idati, “Ameneyo ndi Eliya wa ku Tisibe.”
9Pomwepo mfumuyo idatuma mkulu wina wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kukagwira Eliya. Mkuluyo adapita kwa Eliya nampeza atakhala pansi pamwamba pa phiri. Adamuuza kuti, “Inu, munthu wa Mulungu, mfumu ikukulamulani kuti mutsike.”
10 Lk. 9.54 Koma Eliya adauza mkulu wa ankhondo makumi asanu aja kuti, “Ngati ine ndinedi munthu wa Mulungu, moto utsike kumwamba, ukupsereze iweyo pamodzi ndi anthu ako makumi asanuŵa.” Pomwepo moto udatsikadi kumwamba, nupsereza mkuluyo pamodzi ndi anthu ake makumi asanuwo.
11Tsono mfumu idatumanso mkulu wina pamodzi ndi ankhondo ake makumi asanu. Mkuluyo ndi anthu ake adapita, nakauza Eliya uja kuti, “Inu munthu wa Mulungu, mfumu ikukulamulani kuti mutsike msanga.”
12Koma Eliya adamuyankha kuti, “Ngati ine ndinedi munthu wa Mulungu, moto utsike kumwamba, ukupsereze iweyo pamodzi ndi anthu ako makumi asanuŵa.” Pomwepo moto wa Mulungu udatsikadi kumwamba, nupsereza mkuluyo pamodzi ndi anthu ake makumi asanu aja.
13Mfumu ija idatumanso mkulu wina wachitatu pamodzi ndi ankhondo ake makumi asanu. Koma mkulu wachitatu uja adapita nakagwada pamaso pa Eliya, nampempha kuti, “Inu munthu wa Mulungu, chonde ndikukupemphani kuti musandiwononge ineyo pamodzi ndi anthu anga makumi asanuŵa.
14Onani, moto udatsika kumwamba nupsereza anzanga aja, pamodzi ndi anthu ao omwe. Chonde tipulumutseni, musatiwononge.”
15Apo mngelo wa Chauta adauza Eliya kuti, “Pita naye, usamuwope.” Tsono Eliya adanyamuka natsika limodzi ndi mkulu uja, kupita kwa mfumu.
16Ndipo Eliya adauza mfumuyo kuti “Chauta akunena kuti, ‘Pamene udaatuma amithenga kwa Baala-Zebubi, mulungu wa anthu a ku Ekeroni, kodi ndiye kuti kuno ku Israele kulibe Mulungu woti nkumpempha nzeru?’ Nchifukwa chake Chauta akuti, ‘Iweyo sudzuka pabedi wagonapo, koma ufa ndithu.’ ”
17Motero Ahaziya adafadi potsata mau amene Chauta adaalankhula kudzera mwa Eliya. Ndipo popeza kuti Ahaziya adaalibe mwana wamwamuna, Yoramu mbale wake adaloŵa ufumu m'malo mwake, pa chaka chachiŵiri cha ufumu wa Yehoramu, mwana wa Yosafati, mfumu ya ku Yuda.
18Tsono ntchito zina za Ahaziya pamodzi ndi zonse zimene adazichita zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a Aisraele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.