Owe. 13 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kubadwa kwa Samisoni.

1Aisraele adachimwiranso Chauta. Ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Afilisti pa zaka makumi anai.

2Ku Zora kunali munthu wina, wa fuko la Dani, dzina lake Manowa. Mkazi wake analibe ana, anali wosabereka.

3Mngelo wa Chauta adamuwonekera mkaziyo namuuza kuti, “Inu mai, ngakhale mpaka pano muli opanda ana, komabe mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna.

4Ndiye inu mudzisamale bwino, musamamwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa, ndipo musamadye chakudya chilichonse chosaloledwa.

5Num. 6.1-5 Pakuti ndithu mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa, kumutu kwake kusadzapite lumo, pakuti mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulikira Mulungu kuyambira tsiku la kubadwa kwake. Ndipo adzayambapo ntchito yopulumutsa Aisraele kwa Afilisti.”

6Tsono mkaziyo adadzauza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kuno, ndipo nkhope yake inali yoopsa kwambiri ngati nkhope ya mngelo wa Mulungu. Sindidamufunse kumene akuchokera, iyenso sadandiwuze dzina lake.

7Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pathupi ndipo mudzabala mwana wamwamuna. Ndiye musamamwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa, ndipo musamadye chakudya chosaloledwa chilichonse, chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, wopatulikira Mulungu, kuyambira tsiku la kubadwa kwake mpaka tsiku la kufa kwake.’ ”

8Tsono Manowa adapemphera kwa Chauta kuti, “Inu Chauta, ndapota nanu, mulole kuti munthu amene mudaamtuma uja abwerenso, adzatiphunzitse zimene tiyenera kuchita naye mnyamata amene adzabadweyo.”

9Mulungu adamvera pemphero la Manowa, ndipo mngelo wa Mulungu uja adabweranso kwa mkaziyo nampeza atakhala pansi m'munda. Koma mwamuna wake Manowa sanali nao.

10Mkazi uja adathamanga nakauza mwamuna wake kuti, “Munthu uja adaabwera kuno tsiku lijaliyu wandiwonekeranso.”

11Apo Manowa adanyamuka natsata mkazi wake, ndipo adakafika kumene kunali munthuyo nakamufunsa kuti, “Kodi inu ndinu amene mudaalankhula ndi amaiŵa?” Iye adayankha kuti, “Inde ndinedi.”

12Manowa adamufunsa kuti, “Tsono zimene mudanenazi zikadzachitikadi, kodi mnyamatayo azidzakhala bwanji, ndipo azidzachita chiyani?”

13Mngelo wa Chauta uja adauza Manowa kuti, “Zonse zimene ndidaŵauza amaiŵa asamale kuti azichitadi.

14Asati adye chilichonse chochokera ku mphesa, ndipo asati amwe vinyo kapena chakumwa china choledzeretsa kapenanso kudya chinthu chosaloledwa chilichonse. Asunge zonse zimene ndidaŵalamula.”

15Manowa adauza mngelo wa Chauta kuti, “Pepani, tayambani mwaima, tikuti tikuwotchereni kamwanakambuzi.”

16Koma mngelo wa Chauta adauza Manowa kuti, “Ngakhaletu mukundidikiritsa chakudyacho, ine sindidya ai. Koma ngati mukonze nsembe yopsereza, muipereke kwa Chauta.” (Monsemo nkuti Manowa ali wosazindikira kuti mlendoyo ndi mngelo wa Chauta.)

17Apo Manowa adauza mngeloyo kuti, “Timati mutiwuze dzina lanu kuti tidzakulemekezeni, zikadzachitikadi zimene mwanenazi.”

18Mngelo wa Chautayo adafunsa Manowa kuti, “Chifukwa chiyani mukufuna kudziŵa dzina langa? Dzina laketu nlodabwitsa.”

19Pamenepo Manowa adatenga kamwanakambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya, nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Chauta, Iye amene amachita zodabwitsa.

20Pamene malaŵi a moto ankakwera kumwamba kuchokera paguwapo, mngelo wa Chauta uja adakwera m'malaŵi a motowo, Manowa ndi mkazi wake akuyang'ana. Apo iwo adadzigwetsa pansi, naŵeramitsa mitu pansi.

21Mngelo wa Chauta uja sadaŵaonekerenso Manowa ndi mkazi wake. Choncho Manowa adazindikira kuti anali mngelo wa Chauta.

22Tsono adauza mkazi wake kuti, “Ife ndiye tifatu basi, nanga sitaona Mulungu!”

23Koma mkazi wake adati, “Akadakhala kuti Chauta akufuna kutipha, sakadailandira nsembe yathu yopsereza ndi chopereka chathu cha chakudya chija. Ndiponso sakadatiwonetsa zinthu zonsezi kapenanso kutiwuza tsopano zinthu zonga ngati zimenezi.”

24Motero mkaziyo adabala mwana wamwamuna, namutcha dzina lake Samisoni. Mnyamatayo adakula ndipo Chauta adamdalitsa.

25Ndipo Mzimu wa Chauta udayamba kumlimbitsa pamene anali ku zithando za anthu a fuko la Dani, pakati pa Zora ndi Esitaoli.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help