1Ndili ngati duŵa la ku Saroni,
ngati kakombo wam'zigwa.
Mwamuna
2Muja amakhalira kakombo
pakati pa minga,
ndi m'mene aliri wokondedwa wanga
pakati pa atsikana.
Mkazi
3Muja umakhalira mtengo wa apulosi
pakati pa mitengo yam'nkhalango,
ndi m'mene aliri wokondedwa wanga
pakati pa anyamata.
Ndinkakondwa kwambiri ndikausa mumthunzi mwake,
zipatso zake zinali tseketseketseke m'kamwamu.
4Adanditenga kupita nane ku nyumba yaphwando,
mbendera yake yozika pa ine inali chikondi.
5Mundidyetse mphesa zouma,
munditsitsimutse ndi maapulosi,
pakuti ndikumva chikondi chodwala nacho.
6Ha, ndidakakonda
ineyo nditatsamira dzanja lake lamanzere,
iyeyo nkundikumbatira ndi dzanja lamanja!
7Inu akazi a ku Yerusalemu,
ndithu ndakupembani,
pali mphoyo ndi nswala zakuthengo,
chikondichi musachigwedeze kapena kuchiwutsa
mpaka pamene chifunire ichocho.
Nyimbo Yachiŵiri.Mkazi
8Tamvani liwu la wokondedwa wanga!
Taonani akubwera,
akulumphalumpha pa mapiri,
akujoŵajoŵa pa zitunda.
9Wokondedwa wanga ali ngati mphoyo,
kapena mwanawambaŵala.
Si uyo waimirira apoyo,
kuseri kwa khoma lathulo,
akusuzumira m'mawindo,
akuyang'anira pa made a mawindo.
10Wokondedwa wanga akulankhula nkumandiwuza kuti:
Mwamuna
“Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga,
tiye tizipita.
11Ona, nyengo yachisanu yatha,
mvula yatha ndipo yapitiratu.
12Maluŵa ayamba kuwoneka m'dziko,
nthaŵi yoimba yafika,
njiŵa zikumveka kulira m'dziko mwathu.
13Mikuyu ikubereka zipatso,
mipesa ikuyamba maluŵa.
Mitengoyo ikutulutsa fungo lokoma.
Dzuka bwenzi langa, wokongola wanga,
tiye tizipita.
14Iwe nkhunda yanga,
yokhala m'ming'alu yam'matanthwe,
yobisala m'phiri lotsetsereka,
ntaonako nkhope yako,
ntamvako liwu lako.
Paja liwu lako nlomveka bwino,
ndipo nkhope yako ndi yokongola.
15Mutigwirire nkhandwe,
nkhandwe zing'onozing'ono,
zimene zimatiwonongera minda yamphesa,
pakuti mipesa yathu idachita maluŵa.”
Mkazi
16Wokondedwa wangayo ndi wangadi,
ndipo ine ndine wake.
Amadyetsa gulu lake la ziŵeto
pakati pa akakombo.
17Kamphepo kamadzulo kakamayamba kuuzira,
mithunzi ikamayamba kuthaŵa,
unyamuke, iwe wokondedwa wanga,
uthamange ngati mphoyo,
kapena ngati mwanawambaŵala
pakati pa mapiri azigwembezigwembe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.