2 Ako. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Paulo ateteza utumiki wake

1M'dzina la Yesu Khristu wa mtima woleza ndi wofatsa, ine Paulo mwiniwake, amene anthu ena amati ndine wamantha pamene ndili pamaso panu, koma wosaopa konse pamene ndili nanu kutali, ndikuti mundimve.

2Ndikukupemphani kuti ndikadzafika kwanuko ndisadzakakamizidwe kudzudzula mosaopa konse anthu amene akuti machitidwe athu ndi otsata za anthu chabe.

3Ndi zoona kuti ndife anthu, koma sitimenya nkhondo motsata za anthu chabe.

4Pakuti zida zathu zakhondo si za anthu chabe, koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kuwononga malinga. Timagonjetsa maganizo onyenga,

5ndiponso kudzikuza kulikonse koletsa anthu kudziŵa Mulungu. Timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu.

6Ndipo inu mutakhala omvera kwenikweni, tili okonzeka kulanga aliyense amene samvera.

7Ganizani bwino pa zimene mukuwona ndi maso anu. Kodi pali wina amene amakhulupirira kuti ndi wake wa Khristu? Chabwino, koma akumbukire kuti monga iye ali wake wa Khristu, ifenso ndife ake a Khristu.

8Ndipotu ngakhale mwina ndikunyadira mokakata ulamuliro umene Ambuye adatipatsa woti tikulimbitse nawoni, osati kukuwonongani ai, ndithu sindidzachita manyazi.

9Tsono musayese kuti ndikungokuwopsezani ndi makalata anga.

10Paja ena amati, “Makalata a Paulo ngaukali ndi amphamvu, koma mwiniwake akakhala pakati pathu, iyeyo ngwofooka ndipo mau ake ndi achabe.”

11Anthu oganiza zotere, adziŵe kuti palibe kusiyana pakati pa zimene timanena m'makalata pamene tili nanu kutali ndi zimene timachita tikakhala nanu pamodzi.

12Sikuti timayesa kudzilinga kapena kudziyerekeza ndi ena amene amadzichitira okha umboni. Amapusa chabe pakungodziyesa ndi muyeso waowao, ndi kudzilinganiza ndi anzao a m'gulu lao lomwe.

13Kunena za ife, sitinganyade mopitirira malire. Tidzasamala malire omwe Mulungu adatiikira potifikitsa mpaka kwa inu.

14Sitidabzole malire athu, monga ngati sitidakafike kwanu. Tinali oyamba ndife kukafika kwanu ndi kulalika Uthenga Wabwino wonena za Khristu.

15Motero sitinyadira ntchito zimene anthu ena adazigwira m'dera limene Mulungu adatiikira ife. Kwenikweni tikuyembekeza kuti chikhulupiriro chanu chidzakula, ndipo kuti ntchito yathunso pakati panu idzakula, koma osabzola malire a dera lathu.

16Pambuyo pake tingathe kukubzolani nkukalalika Uthenga Wabwino ku maiko enanso, osanyadira ntchito imene munthu wina wachita kale m'dera lake.

17Yer. 9.24 Paja Malembo akuti, “Wofuna kunyada, anyadire Ambuye.”

18Pakuti munthu wovomerezeka, si amene amadzichitira yekha umboni, koma amene Ambuye amamchitira umboni.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help