Mas. 95 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nyimbo yotamanda.

1Bwerani, timuimbire Chauta.

Tiyeni tifuule ndi chimwemwe kwa Iye,

thanthwe lotipulumutsa.

2Tiyeni, tikafike pamaso pake, tikamthokoze,

tiyeni tifuule kwa Iye ndi chimwemwe,

timuimbire nyimbo zotamanda.

3Pakuti Chauta ndiye Mulungu wamkulu,

ndiye Mfumu yaikulu yopambana milungu yonse.

4Maziko ozama a dziko lapansi ali m'manja mwake.

Mapiri aatali omwe ngakenso.

5Nyanja ndi yake, popeza kuti ndiye adailenga.

Mtunda ndi wakenso, popeza kuti ndiye adaupanga.

6Bwerani, timpembedze ndi kumlambira.

Tiyeni tigwade pamaso pa Chauta Mlengi wathu.

7 Ahe. 3.7-11 Ahe. 3.15; 4.7 Pakuti ndiye Mulungu wathu,

ndipo ife ndife anthu a pa busa lake,

ndife nkhosa zodyera m'manja mwake.

Lero mukadamverako mau ake!

8 Eks. 17.1-7; Num. 20.2-13 Musaumitse mitima yanu monga ku Meriba kuja,

monganso tsiku lija ku Masa m'chipululu muja,

9pamene makolo anu adandiputa mondiyesa

ngakhale anali ataona ntchito zanga.

10Pa zaka makumi anai ndidaipidwa ndi mbadwo umenewo,

choncho ndidati,

“Ameneŵa ndi anthu osakhulupirika,

sasamalako njira zanga.”

11 Num. 14.20-23; Deut. 1.34-36; Ahe. 4.3, 5; Deut. 12.9, 10 Choncho ndidakwiya nkulumbira

kuti anthuwo sadzaloŵa ku malo anga ampumulo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help