Lev. 2 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nsembe zaufa

1“Munthu wina aliyense akabwera kudzapereka chopereka cha chakudya kwa Chauta, nsembeyo ikhale ya ufa wosalala. Ufawo authire mafuta ndi lubani,

2ndipo abwere nawo kwa ansembe, ana a Aroni. Atapeko ufa wosakaniza ndi mafuta uja dzanja limodzi, ndi lubani wake yense. Tsono wansembe atenthe zimenezo pa guwa, kusonyeza kuti nsembeyo yaperekedwa kwa Chauta, ndi nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.

3Zotsala za chopereka cha chakudyacho zikhale za Aroni pamodzi ndi ana ake. Chimenecho ndicho chigawo chopatulika kopambana, chifukwa chatapidwa pa nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.

4“Ukamapereka chopereka cha chakudya chophika mu uvuni, chikhale buledi wa ufa wa tirigu wosalala wopanda chofufumitsira, wosakaniza ndi mafuta, kapena ikhale timitanda ta buledi wosafufumitsa, topyapyala, topaka mafuta.

5Nsembe yako ikakhala chakudya chophika pa chitsulo chamoto, chikhale buledi wa ufa wosalala wopanda chofufumitsira, wosakaniza ndi mafuta.

6Umuduledule ndi kumupaka mafuta. Chimenecho ndicho chopereka cha chakudya.

7Ndipo nsembe yako ikakhala ya chopereka cha chakudya chophika pa chiwaya, chikhale ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta.

8Tsono ubwere nacho chopereka chimenechi kwa Chauta, ndipo utachipereka kwa wansembe, iyeyo abwere nacho ku guwa.

9Apo wansembeyo atengeko gawo lina la choperekacho kusonyeza kuti chaperekedwa kwa Chauta, tsono achitenthe paguwapo. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, ya fungo lokomera Chauta.

10Ndipo zotsala za chopereka cha chakudyacho zikhale za Aroni ndi ana ake. Chimenecho ndicho chigawo chopatulika kopambana, chifukwa chatapidwa pa nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.

11“Chopereka cha chakudya chimene upereka kwa Chauta chikhale chopanda chofufumitsira, pakuti suyenera kupereka kwa Chauta nsembe yotentha pa moto, imene ili ndi chofufumitsira kapena uchi.

12Ziŵirizo ungathe kubwera nazo ngati nsembe ya zokolola zoyambirira zopereka kwa Chauta. Koma usazitenthere pa guwa kuti zipereke fungo lonunkhira.

13Zopereka zako zonse za zakudya uzithire mchere, osaiŵala ai: mcherewo ndi wosonyeza chipangano cha pakati pa iwe ndi Mulungu wako. Uzithira mchere nsembe zako zonse.

14“Ukamapereka kwa Chauta chopereka cha chakudya choyamba kucha, nsembeyo ikhale ya mbeu zatsopano zokazinga ndi zopunthapuntha.

15Ndipo uchithithire mafuta ndi lubani. Chimenecho ndicho chopereka cha chakudya.

16Tsono wansembe atenthe chigawo cha mbeu zopunthapuntha zija ndi cha mafuta, ndiponso lubani wake yense, kuti ikhale nsembe yachikumbutso. Imeneyo ndiyo nsembe yotentha pa moto, yopereka kwa Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help