1 Eks. 15.22—17.16 Luntha lidapambanitsa Aisraele pa ntchito zao
kudzera mwa mneneri woyera mtima.
2Adayenda m'chipululu chopanda anthu,
namanga mahema ao
pamalo pamene sipadapite anthu.
3Adalimbikira pamaso pa amaliwongo ao,
nkuŵapambana adani aowo pa nkhondo.
4Atamva ludzu adakupemphani,
Inu nkuŵapatsa madzi
otumphuka m'thanthwe lolimba zedi,
mudapha ludzu lao potulutsa madzi
m'thanthwe lagwaa.
Mulungu alanga Aejipito5Zimene zidasautsa adani ao ngati chilango,
zidasanduka za phindu kwa eniakewo
pa nthaŵi ya mavuto ao.
6M'malo mwa kasupe wa madzi
oyenda nthaŵi zonse,
adani ao adapeza madzi oonongeka,
ataipa ndi magazi,
7ngati chilango chifukwa cha lamulo lao lija
loti ana aphedwe.
Koma anthu anu mudaŵapatsa madzi ochuluka,
pamene iwo sankayembekezako.
8Zimenezo zidachitika mutaŵamvetsa ludzu,
kuti adziŵe m'mene mudalangira adani ao.
9Pamene munkaŵayesa pakuŵalanga mwachifundo,
iwo adaphunzira m'mene mudazunzira mwaukali
anthu osamvera.
10Pajatu mudaŵayesa ndi kuŵapatsa phunziro,
monga m'mene bambo amachenjezera ana ake.
Koma ena aja mudaŵasautsa,
monga momwe mfumu yankhanza imalangira osamvera.
11Adani ao ankapezabe mavuto,
ngakhale anthu anu atakhala pafupi kapena kutali.
12Chisoni chidaŵagwira moŵirikiza,
ndipo ankabuula pokumbukira
zimene zidaŵagwera kale.
13Pakumva kuti zilango zao
zidathandiza anthu anu olungama,
adaniwo adazindikira kuti
zimenezi adaachita ndi Ambuye.
14Munthu uja amene iwowo adaamutaya kale lija
kenaka nkumuchotsa monyoza,
pambuyo pake adazizwa naye kwakukulu,
chifukwa ludzu lao
lidaapambana kwambiri la anthu olungama.
15 Eks. 8.1-24; 10.12-15 Chifukwa cha maganizo ao opusa ndi oipa,
amene adaŵasokeretsa mpaka kuŵapembedzetsa njoka
ndi nyama zonyansa,
mudaŵalanga pakuŵatumizira unyinji
wa zolengedwa zinanso zopanda nzeru.
16Choncho mudaŵaphunzitsa
kuti choipa chitsata mwini.
17Dzanja lanu lamphamvuzonse,
limene lidapanga zinthu zonse
kuchokera ku chinthu chosakonzeka,
likadatha kuŵatumizira zilombo zochuluka
ndi mikango yaukali.
18Likadathanso kuŵatumizira
zilombo zina zosadziŵika,
zolengedwa chatsopano,
za ukali woopsa,
zopuma mpweya wamoto,
zotulutsa utsi wonunkha m'kamwa,
kapena zoponya zing'aning'ani zoopsa
kuchokera m'maso mwake.
19Zolusazo zikadatha kuwonongadi anthuwo,
komanso ngakhale kungoziwona kokha
kukadatha kupha anthuwo ndi mantha.
20Ngakhale popanda zimenezo,
anthuwo akadatha kufa,
Inu mutangoŵauzira mpweya kamodzi kokha,
poŵalondola ndi chilungamo chanu
ndi kuŵamwaza ndi mpweya wanu wamphamvu.
Koma Inu mudafuna kukonza zonse molongosoka,
mutaziŵerenga ndi kuziyesa pa sikelo.
Mulungu ndi wamphamvu ndiponso wachifundo21Mphamvu zanu mutha kuzigwiritsa ntchito
nthaŵi iliyonse.
Ndani angalimbikire kulimbana ndi dzanja lanu?
22Pamaso panu dziko lonse lapansi lili
ngati kamchenga kopendeketsa sikelo,
ngati dontho la mame am'mamaŵa logwa pa nthaka.
23Komabe chifukwa mungathe kuchita zinthu zonse,
mumaŵachitira chifundo anthu onse.
Mumapsinya maso dala
kuti musaone machimo a anthu,
kuti apeze mpata wotembenukira mtima.
24Mumakonda zolengedwa zonse,
palibe ncholengedwa chimodzi chomwe
chimene chingakunyanseni.
Mukadadana ndi kanthu,
bwenzi mutaleka kukalenga.
25Kanthu kalikonse kakadakhala moyo bwanji,
mukadapanda kukafuna?
Kakadakhalitsa bwanji,
Inu mukadapanda kukasunga?
26Koma zinthu zonse mumazichitira chifundo,
chifukwa zonse nzanu, Inu Ambuye,
amene mumakonda kwambiri chamoyo chilichonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.