Esr. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ayuda aŵauza kuti alipsire

1Pa tsiku limenelo, mfumu Ahasuwero adapatsa mfumukazi Estere nyumba ya Hamani, mdani wa Ayuda uja. Ndipo Mordekai anthu adabwera naye pamaso pa mfumu, popeza kuti Estere adaauza mfumuyo za chibale cha iyeyo ndi Mordekai.

2Pamenepo mfumuyo idavula mphete yake yosindikizira imene adaailanda kwa Hamani, nkuipatsa Mordekai. Ndipo Estere adapatsa Mordekai udindo woyang'anira nyumba ya Hamani.

3Tsono Estere adalankhulanso ndi mfumu. Adadzigwetsa ku mapazi a mfumu, nampempha akulira kuti aletse chinthu choipa chimene Hamani Mwagagi uja adaakonza, ndiponso chiwembu chomwe ankafuna kuŵachita Ayuda.

4Apo mfumu idamloza Estere ndi ndodo yake yaufumu yagolide,

5ndipo Estereyo adadzuka, nakaima pamaso pa mfumu, nati, “Chikakukondwetsani amfumu, ngati ineyo ndakukomerani m'maso, ndipo ngati chopempha changacho chikhale chabwino pamaso panu, ineyo nkukuchititsani kaso amfumu, ndiye kuti lilembedwe lamulo losintha mau a m'makalata amene Hamani Mwagagi uja, mwana wa Hamedata, adalemba. Paja adalemba kuti Ayuda onse amene akukhala m'maiko a mfumu aonongedwe.

6Nanga ndingathe bwanji kupirira, poona tsoka limene likudzagwera anthu a mtundu wanga? Ndingathe bwanji kupirira, pomaona abale anga akuwonongedwa?”

7Pomwepo mfumu Ahasuwero adauza mfumukazi Estere ndi Myuda uja Mordekai kuti, “Onani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndipo Hamaniyo ampachika pa mtengo, chifukwa chakuti ankafuna kupha Ayuda.

8Dan. 6.8Tsono aŵirinu mulembe za Ayudawo monga momwe mungafunire. Mulembe m'dzina la mfumu ndi kusindikiza chizindikiro cha mphete ya mfumu. Paja lamulo lolembedwa m'dzina la mfumu ndi losindikizidwa ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu, silingasinthike.”

9Mfumu idaitanitsa alembi ake nthaŵi yomweyo, pa mwezi wachitatu wa Sivani, pa tsiku la 23 la mweziwo. Ndipo iwowo adalemba lamulo potsata zonse zimene Mordekaiyo adaalamula zokhudza Ayuda. Adalembera akalonga, akazembe ndi akuluakulu a m'madera onse, kuyambira ku dziko la Indiya mpaka ku Etiopiya, onse pamodzi madera 127. Ku dera lililonse adalemberako kalata yakeyake, ndiponso kwa mtundu uliwonse wa anthu m'chilankhulo chaochao. Adalemberanso Ayuda kalata m'chilankhulo chaochao.

10Makalata amenewo adaŵalemba m'dzina la mfumu Ahasuwero, naŵasindikiza ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu. Ndipo makalatawo adaŵatumiza ndi anthu amtokoma okwera pa akavalo othamanga kwambiri, oŵagwiritsa ntchito potumikira mfumu, ochokera m'khola la mfumu.

11Chifukwa cha makalata amenewo, mfumu idalola Ayuda amene ankakhala mu mzinda uliwonse, kuti asonkhane ndi kuteteza moyo wao, ndiponso kuti aononge, aphe ndi kufafaniziratu gulu la adani a mtundu uliwonse kapena m'dera lililonse, limene lingaŵapute. Aononge ana ao ndi akazi ao omwe, ndiponso afunkhe katundu wao yense.

12Adaloledwa kuchita zimenezi pa tsiku limodzi m'madera onse a m'dziko la mfumu Ahasuwero, pa tsiku la 13 la mwezi wa 12, mwezi wa Adara.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help