1Tsono, inu okondedwa, popeza kuti tili ndi malonjezo ameneŵa, tiyeni tidzichotsere zinthu zonse zodetsa thupi lathu kapena mtima wathu. Ndipo pakuwopa Mulungu tiziyesetsa ndithu kukhala oyera mtima.
Paulo akondwa chifukwa cha kulapa kwa mpingo2Mutipatse malo m'mitima mwanu. Sitidalakwire munthu aliyense, kapena kumuipitsa, kapena kumchenjerera.
3Sindikunena zimenezi kuti mupezeke olakwa. Paja monga ndanena kale, inu muli m'mitima mwathu ndithu, kotero kuti tili pamodzi, ngakhale tikhale moyo kapena timwalire.
4Ndimakukhulupirirani kwambiri, ndipo ndimakunyadirani kwenikweni. Zondilimbitsa mtima zandichulukira, ndipo m'zovuta zathu zonse ndakondwa kopambana.
5 2Ako. 2.13 Ngakhale pamene tidafika ku Masedoniya sitidapeze mpumulo konse. Tidapeza zovuta ponseponse, popeza kuti panali kukangana ndi adani otizungulira, ndiponso mantha m'mitima mwathu.
6Koma Mulungu amene amalimbitsa otaya mtima, adatilimbitsa ndi kufika kwa Tito.
7Ndipo chimene chidatilimbitsa, si kufika kwake kokha, koma makamakanso mau ake onena za m'mene iyeyo mudamlimbitsira mtima. Adatiwuza kuti mukulakalaka kundiwona, kuti muli ndi chisoni, ndiponso kuti mukuchita changu kundithandiza. Nchifukwa chake ndakondwa koposa.
8Kalata yanga ija idakupwetekani mtima, komabe sindikuchita chisoni kuti ndidailemba. Ndidaachita chisoni poyamba, ndipo ndikuwona kuti kalatayo idakupwetekanidi mtima, ngakhale kanthaŵi pang'ono chabe.
9Koma tsopano ndakondwa, osati chifukwa ndidaakupwetekani mtima, koma chifukwa kuvutika kwanu kudakuthandizani kutembenuka mtima. Kuvutika kwanuko kunali kovomerezeka ndi Mulungu, motero sitidakutayitseni kanthu kabwino kalikonse.
10Paja chisoni chokomera Mulungu chimamtembenuza munthu ndi kumpulumutsa, kotero kuti chisoni chake chimathera pomwepo. Koma kumva chisoni monga m'mene amachitira anthu odalira zapansipano, kumadzetsa imfa.
11Onani zimene chisoni chanu chokomera Mulungu chija chakuchitirani: chakupatsani changu chachikulu, chakukakamizani kwambiri kutsimikiza kuti simudalakwe, chakukwiyitsani kwambiri, ndipo chakuchititsani mantha aakulu. Chakulakalakitsani kuti mundiwone, ndipo chakupatsani changu chonditchinjiriza, ndiponso cholanga olakwa. Pa nkhani yonseyi umboni ulipo wakuti inu simudalakwepo.
12Motero, ngakhale ndidakulemberani kalata imene ija, sindidailembe chifukwa cha amene adalakwa uja, kapena chifukwa cha amene iyeyo adamlakwira. Koma ndidailemba kuti ndikuwonetseni pamaso pa Mulungu kuti changu chanu chotitchinjiriza nchachikulu ndithu.
13Zimenezi zatilimbitsa mtima kwambiri.
Kuwonjezera pa zotilimbitsa mtimazo, chimwemwe cha Tito chidatikondweretsa kopambana, popeza kuti nonsenu mudamsangulutsa.
14Ndidamuuzadi kuti ndimakunyadirani, ndipo inu simudandichititse manyazi. Koma monga momwe zonse zimene tidaakuuzani zinali zoona, momwemonso kudaoneka kuti zimene ndidauza Tito mokunyadirani, zinali zoona.
15Makamaka chikondi chake pa inu nchachikulu kopambana pamene akumbukira kuti nonsenu mudamvera mau anga, ndipo mudamlandira ndi mantha ndi monjenjemerera.
16Ndikukondwa kuti ndingathe kukukhulupirirani pa zonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.