1Pamene Aisraele anali ku Sitimu, anthu aamuna adayamba kuchita dama ndi akazi a ku Mowabu.
2Akaziwo ankaitana amuna ku nsembe za milungu yao, ndipo amunawo ankadya nawo, ndi kumapembedza milungu yaoyo.
3Choncho Aisraele adapembedza nao Baala wa ku Peori, ndipo Chauta adaŵapsera mtima Aisraele.
4Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Utenge atsogoleri onse a Aisraele ndipo uŵanyonge poyera pamaso panga, kuti ndileke kukwiyira Israele.”
5Apo Mose adauza oweruza a Aisraele kuti, “Aliyense mwa inu aphe anthu ake amene adapembedza nao Baala wa ku Peori.”
6Tsono Mwisraele wina adabwera ndi mkazi Wachimidiyani kubanja kwake, Mose ndi Aisraele onse akupenya, pamene ankalira pakhomo pa chihema chamsonkhano.
7Finehasi mwana wa Eleazara, mdzukulu wa Aroni, ataona zimenezo, adadzuka nasiya mpingowo, nakatenga mkondo.
8Ndipo adatsatira Mwisraele uja mpaka kukaloŵa m'chipinda cham'kati, nabaya onse aŵiriwo, Mwisraeleyo pamodzi ndi mkaziyo. Motero mliri udaleka pakati pa Aisraele.
9Komabe anthu okwanira 24,000 anali atafa kale ndi mliriwo.
10Chauta adauza Mose kuti,
11“Finehasi mwana wa Eleazara, mdzukulu wa Aroni, wandiletsa kuti ndisaŵaononge Aisraele, chifukwa choti sadalole kuti wina aliyense apembedze mulungu wina koma Ine, nchifukwa chake sindidaŵaononge ndili wokwiya.
12Motero umuuze kuti ndikupangana naye tsopano chipangano chamtendere.
13Ndikupangana naye iyeyu ndi zidzukulu zake zonse, chipangano cha unsembe wamuyaya, chifukwa sadalole kuti anthu aukire Ine Mulungu, ndipo adachita ntchito yopepesera machimo a Aisraele.”
14Mwisraele amene adaphedwa pamodzi ndi mkazi Wachimidiyani uja anali Zimiri mwana wa Salu, mtsogoleri wa banja la makolo a Asimeoni.
15Ndipo mkazi Wachimidiyani amene adaphedwayo anali Kozibi mwana wa Zuri, amene anali mtsogoleri wa mbumba ina ya fuko la ku Midiyani.
16Chauta adauza Mose kuti,
17“Uŵathire nkhondo Amidiyani, ndiponso uŵaononge
18chifukwa choti adakuchitani zachabe pokunyengani ku Peori, ndiponso chifukwa cha nkhani ya mlongo wao Kozibi, mwana wamkazi wa mfumu ya ku Midiyani, amene adaphedwa pa nthaŵi ya mliri chifukwa cha zochitika ku Peori zija.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.