1 Maf. 15 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Abiya mfumu ya ku Yuda(2 Mbi. 13.1—14.1)

1Pa chaka cha 18 cha ufumu wa Yerobowamu mwana wa Nebati, Abiya adaloŵa ufumu wa ku Yuda.

2Adakhala mfumu mu Yerusalemu zaka zitatu. Mai wake anali Maaka, mwana wa Abisalomu.

3Ndipo Abiyayo adatsatira zoipa zonse zimene ankachita bambo wake. Sadatsate Chauta moona monga Davide kholo lake.

41Maf. 11.36 Komabe chifukwa cha Davideyo, Chauta adapatsa Abiya mwana, kuti azilamulira ku Yerusalemu, iyeyo atafa.

52Sam. 11.1-27 Zidatero chifukwa choti Davide adaachita zolungama pamaso pa Chauta, poti sadapatuke pa zimene Chauta adamlamula masiku onse a moyo wake, kupatula nkhani yokha ija ya Uriya Muhiti uja.

62Mbi. 13.3-21 Panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yerobowamu masiku onse a moyo wa Abiyayo.

7Tsono ntchito zina za Abiya ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.

8Tsono Abiya adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide. Ndipo Asa mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Asa mfumu ya ku Yuda(2 Mbi. 15.16—16.6)

9Pa chaka cha 20 cha ufumu wa Yerobowamu mfumu ya ku Israele, Asa adaloŵa ufumu wa ku Yuda,

10ndipo adalamulira zaka 41 ku Yerusalemu. Gogo wake wamkazi anali Maaka, mwana wa Abisalomu.

11Asa adachita zolungama pamaso pa Chauta monga m'mene adachitira Davide kholo lake.

122Mbi. 15.8-15 Adachotsa anthu onse m'dzikomo amene ankachitana zadama potsata chipembedzo chao, nachotsanso mafano onse amene makolo ake adaapanga.

13Adachotsanso gogo wake Maaka pa udindo wa mfumukazi, chifukwa choti ankapembedza fano lonyansa la Asera. Ndipo Asa adaliphwanya fanolo, nakalitenthera ku khwaŵa la Kidroni.

14Akachisi okha opembedzerapo mafano sadaŵaononge. Komabe mtima wa Asa udakhala wokhulupirika kwa Chauta masiku onse a moyo wake.

15Tsono Asayo adabwera nazo ku Nyumba ya Chauta zopereka za bambo wake ndiponso zopereka zakezake za siliva, golide ndi ziŵiya.

16Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa, mfumu ya ku Israele, nthaŵi yonse ya ufumu wao.

17Baasayo adapita kukathira nkhondo dziko la Yuda, namangira linga mzinda wa Rama, kuti aziletsa anthu kuloŵa kapena kutuluka m'dziko la Asa, mfumu ya ku Yuda.

18Tsono Asa adatenga siliva yense pamodzi ndi golide, zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso ku nyumba ya mfumu, napatsira atumiki ake. Ndipo adaŵatuma kuti akazipereke Benihadadi, mwana wa Tabirimoni mdzukulu wa Heziyoni, mfumu ya ku Siriya, amene ankakhala ku Damasiko. Mau a Asa anali akuti,

19“Tiye tigwirizane ine ndi iwe, monga m'mene ankachitira bambo wanga ndi bambo wako. Ona, ndikukutumizira mphatso za siliva ndi golide. Pita ukaphwanye chigwirizano chako ndi Baasa, mfumu ya ku Israele, kuti sadzandithiranso nkhondo.”

20Benihadadi adamvera zimene adanena mfumu Asa zija, motero adatuma atsogoleri a magulu ake ankhondo kukathira nkhondo mizinda ya ku Israele. Adagonjetsa Iyoni, Dani, Abele-Beti-Maaka ndi dera lonse Kineroti pamodzi ndi dziko lonse la Nafutali lomwe.

21Tsono Baasa atazimva zimenezi, adaleka kumangira Rama linga, nakakhala ku Tiriza.

22Apo mfumu Asa adaitana anthu onse a ku Yuda, osasiya ndi m'modzi yemwe, kuti adzanyamule miyala ndi mitengo, imene Baasa ankamangira linga la Rama. Zimenezi mfumu Asa adamangira linga la Geba m'dziko la Benjamini, ndiponso la Mizipa.

23Tsono ntchito zina za Asa, zamphamvu zake zonse, zinthu zimene adazichita ndi mizinda imene adaimanga, zonsezo zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda. Koma pa nthaŵi ya ukalamba wake adadwala nthenda ya miyendo.

24Ndipo adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo mu mzinda wa Davide kholo lake. Mwana wake Yehosafati ndiye adaloŵa ufumu m'malo mwake.

Nadabu mfumu ya ku Israele

25Nadabu, mwana wa Yerobowamu, adayamba kulamulira anthu a ku Israele pa chaka chachiŵiri cha ufumu wa Asa wa ku Yuda. Tsono Nadabuyo adalamulira ku Israele zaka ziŵiri.

26Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta, nayenda njira za bambo wake, ndipo zoipa zakezo adachimwitsa nazo anthu a ku Israele.

27Tsono Baasa mwana wa Ahiya, wa banja la Isakara, adachita chiwembu Nadabuyo. Adamupha ku Gibetoni, mzinda wa Afilisti, pamene Nadabu ndi anthu a ku Israele ankathira nkhondo mzindawo.

28Baasa adapha Nadabu pa chaka chachitatu cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, naloŵa ufumu m'malo mwake.

291Maf. 14.10 Atangoloŵa ufumuwo, adapha anthu onse a banja la Yerobowamu. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe wamoyo pa banjapo, mpaka adaonongeratu banja lonselo, malinga ndi mau amene Chauta adaalankhula kudzera mwa mtumiki wake uja Ahiya wa ku Silo.

30Zimenezi zidachitika chifukwa cha machimo a Yerobowamu ndi zimene adachimwitsa nazo anthu a ku Israele, naputa nazo mkwiyo wa Chauta, Mulungu wa Aisraele.

31Tsono ntchito zina za Nadabu, ndi zonse zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.

32Ndipo panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa masiku onse a ufumu wao.

Baasa mfumu ya ku Israele

33Chaka chachitatu cha ufumu wa Asa wa ku Yuda, Baasa mwana wa Ahiya adayamba kulamulira anthu a ku Israele ku Tiriza, ndipo adakhala mu ufumu zaka 24.

34Iyeyo adachita zoipa pamaso pa Chauta ndipo ankayenda m'njira zoipa za Yerobowamu, namachita zimene adachimwitsa nazo anthu a ku Israele.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help