Mt. 11 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yohane Mbatizi atuma amithenga kwa Yesu(Lk. 7.18-35)

1Yesu atatsiriza kulangiza ophunzira ake khumi ndi aŵiri aja, adachoka kumeneko nkumakaphunzitsa ndi kulalika m'mizinda yao.

2Pamene Yohane Mbatizi anali m'ndende, adaamva zimene Khristu uja ankachita. Choncho adatuma ophunzira ake ena kwa Iye kukamufunsa kuti,

3“Kodi Inu ndinu uja ankati adzabwerayu, kapena tiziyembekezera wina?”

4Yesu adati, “Pitani, kamuuzeni Yohane zimene mukuzimva ndi kuziwona.

5 bwenzi anthu ake atavala kale ziguduli nkudzithira phulusa, kuwonetsa kuti atembenukadi mtima.

22Koma ndikunenetsa kuti pa tsiku lachiweruzo, Mulungu adzachitako chifundo polanga Tiro ndi Sidoni, koposa polanga inu.

23Yes. 14.13-15; Gen. 19.24-28 Ndipo iwe Kapernao, kodi ukuyesa kuti adzakukweza mpaka Kumwamba? Iyai, adzakutsitsa mpaka ku Malo a anthu akufa. Chifukwa zamphamvu zimene zidachitika mwa iwe, achikhala zidaachitikira m'Sodomu, bwenzi mzindawo ukadalipo mpaka lero.

24Mt. 10.15; Lk. 10.12Koma ndikunenetsa kuti pa tsiku la chiweruzo Mulungu adzachitako chifundo polanga Sodomu koposa polanga iwe.”

Yesu ndiye wopatsa mpumulo(Lk. 10.21-22)

25Pa nthaŵi imeneyo Yesu adati, “Atate, Mwini kumwamba ndi dziko lapansi, ndikukuyamikani kuti zinthuzi mudaululira anthu osaphunzira, nkubisira anthu anzeru ndi ophunzira.

26Chabwino Atate, pakuti mudafuna kutero mwa kukoma mtima kwanu.

27 Yoh. 3.35; Yoh. 1.18; 10.15 “Atate adaika zonse m'manja mwanga. Palibe wina wodziŵa Mwana kupatula Atate okha. Palibenso wina wodziŵa Atate kupatula Mwana yekha, ndiponso amene Mwanayo akufuna kumuululira.

28 Mphu. 6.24-30; 24.19; 51.23-26 “Bwerani kwa Ine, inu nonse otopa ndi olemedwa, ndipo Ine ndidzakupatsani mpumulo.

29Yer. 6.16Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa Ine, pakuti ndine wofatsa ndi wa mtima wodzichepetsa; mukatero mudzapeza mpumulo m'mitima mwanu.

30Pajatu goli limene ndimakoleka Ine nlosavuta, ndipo katundu amene ndimasenzetsa Ine ngwopepuka.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help