1Tsono Mordekai adanena kuti, “Zonsezi zachokera kwa Mulungu.
2Ndikukumbukira maloto olosera zimenezi amene ndidaaŵalota aja, ndipo ndikuwona kuti zonse zam'malotomo zapherezeradi.
3Paja panali kakasupe kamene kadaasanduka mtsinje, panalinso kuŵala, dzuŵa ndi madzi ochuluka. Mtsinjewo ndi Estereyu, amene mfumu idamkwatira nkumusandutsa mfumukazi.
4Dzinjoka dziŵiri dzija ndi ineyo ndi Hamani.
5Mitundu ya anthu inayo ndi imene idaafuna kuwononga Israele.
6Ndipo fuko langali la Israele ndi limene lidaalira ndi kudandaula kwa Mulungu, ndipo lidapulumuka. Ndithudi Ambuye adapulumutsa fuko lake, adatichotsera zoopsa zonse. Mulungu adachitadi zodabwitsa zimene sizidaonekepo pakati pa mitundu ina ya anthu.
7Mulungu anali ndi cholinga chake pa fuko lathu, ndipo anali ndi cholinga china pa mitundu inayo.
8Ndipo pa tsiku limene Mulungu adaalifuna, zolinga ziŵirizo zidapherezeradi.
9Choncho Mulungu adakumbukira ndi kupambanitsa fuko lathu limene lili lakelake.
10Nchifukwa chake anthu a fuko lathu adzakumbukira zimenezo pa mwezi wa Adara, tsiku la 14 ndi la 15. Adzachita msonkhano ndipo adzakondwera ndi kusangalala pamaso pa Mulungu chaka ndi chaka mpaka muyaya.”
Mau oonjezera11Pa chaka chachinai cha ufumu wa Ptolemeyo ndi Kleopatra, Dositeo amene ankadzinenerera kuti, “Ndine wansembe ndi mlevita,” pamodzi ndi Ptolemeyo mwana wake, adabwera ndi kalata imene taitchula pamwambayi. Adanenetsa ndithu kuti inali kalata chaiyo imene mfumu idaatumiza, ndipo kuti adaitembenuza ndi Lisimake, mwana wa Ptolemeyo, mmodzi mwa anthu okhala ku Yerusalemu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.