1 Ako. 4 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kutumikira kwa atumwi a Khristu

1Muzitiwona ngati antchito a Khristu, ngati akapitao osamala zinsinsi za Mulungu.

2Chofunika chachikulu pa akapitao otere nchakuti akhale okhulupirika.

3Kunena za ine ndekha, ndilibe nazo kanthu ngati ndiweruzidwa ndi inu, kapenanso ndi bwalo lina lililonse la anthu. Ndiponsotu ngakhale mwiniwakene sindidziweruza ndekha ai.

4Lun. 17.11Ndilibe kanthu konditsutsa mumtima mwanga, komabe ngakhale chimenechi si chitsimikizo chakuti ndine wolungama. Ondiweruza ndi Ambuye basi.

5Motero musaweruziretu munthu aliyense, Ambuye asanabwere. Iwo ndiwo adzaunika pa zonse zobisika mu mdima, ndipo adzaulula maganizo a m'mitima mwa anthu. Pamenepo aliyense adzalandira kwa Mulungu chiyamiko chomuyenerera.

6Abale, zimene ndanenazi nzokhudza ine ndi Apolo. Ndifuna kuti zimenezi zikuphunzitseni tanthauzo la mau aja akuti, “Musapitirire zimene Malembo akunena.” Nchifukwa chake musamanyadira wina, ndi kupeputsa mnzake.

7Nanga adakusiyanitsa ndi anthu ena ndani? Kaya uli ndi chiyaninso chimene sudachite kuchilandira? Tsono ngati udachita kuzilandira, ukunyadiranji ngati kuti sudangozilandira chabe?

8Ndiye kuti muli nazo kale zonse zimene mumasoŵa! Ndiye kuti mwalemera kale! Ndiye kuti mwasanduka mafumu popanda ife! Ndikadakondwera mukadakhaladi mafumu, kuti ifenso tikhale mafumu pamodzi nanu.

9Ndikuwona kuti atumwife Mulungu adatipatsa malo a kuthungo kwenikweni, ngati anthu oti akukaphedwa. Ndithu tasanduka ngati chinthu chochiwonetsa kwa zolengedwa zonse, osati anthu okha ai, komanso ndi angelo omwe.

10Ife ndife opusa chifukwa cha Khristu, koma inu ndinu anzeru mwa Khristu. Ife ndife ofooka, koma inu ndinu amphamvu. Inu mumalandira ulemu, koma ife timanyozedwa.

11Mpaka tsopano lino timamva njala ndi ludzu, ndipo ndife ausiŵa. Anthu akutimenya, ndipo tilibe pokhala penipeni.

12Ntc. 18.3 Tikugwira ntchito kolimba ndi manja athu kuti tidzisunge. Anthu akamatichita chipongwe, timapempha kuti Mulungu aŵadalitse. Anthu akamatizunza, timangopirira.

13Anthu akamatilalatira, timangoŵayankha moleza. Tasanduka onyozeka, ngati zinyatsi za dziko lapansi, ndipo mpaka tsopano anthu onse akutiyesa zinyalala.

14Ndikukulemberani zonsezi, osati kuti ndikuchititseni manyazi, koma kuti ndikulangizeni, chifukwa ndinu ana anga okondedwa.

15Ngakhale mutakhala nawo aphunzitsi ambirimbiri m'moyo wanu wachikhristu, simukhala ndi atate ambiri ai. Pajatu m'moyo wanu wachikhristu ine ndidachita ngati kukubalani pakukulalikirani Uthenga Wabwino.

161Ako. 11.1; Afi. 3.17Ndikukupemphani tsono kuti muzinditsanzira.

17Nchifukwa chake ndakutumizirani Timoteo, mwana wanga wokondedwa ndi wokhulupirika mwa Ambuye. Iyeyu adzakukumbutsani za mayendedwe anga achikhristu, amene sasiyana ndi zimene ndimaphunzitsa ponseponse m'mipingo yonse.

18Ena mwayamba kudzitukumula, monga ngati sindidzabwerako kwanu.

19Koma Ambuye akalola, ndidzabwera kwanuko posachedwa. Pamenepo ndidzadziŵa zimene odzitukumulawo angathe kuchita, osati zimene amangonena chabe.

20Pakuti mu Ufumu wa Mulungu chachikulu si mau chabe, koma ntchito.

21Nanga mukufuna chiyani? Mukufuna kuti ndidzabwere kwanuko ndi mkwapulo, kapena ndi mtima wachikondi ndi wofatsa?

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help